Yeremiya 37 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 37:1-21

Atsekera Yeremiya Mʼndende

1Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, inakhazika pa mpando waufumu Zedekiya mwana wa Yosiya kukhala mfumu ya Yuda. Iye analowa mʼmalo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu. 2Koma Zedekiya kapena atumiki ake ngakhalenso anthu a mʼdzikomo sanasamalire mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya.

3Tsono Zedekiya anatuma Yehukali mwana wa Selemiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga uwu: “Chonde tipempherereni kwa Yehova Mulungu wathu.”

4Nthawi imeneyinso nʼkuti Yeremiya ali ndi ufulu woyenda pakati pa anthu chifukwa anali asanaponyedwe mʼndende. 5Nthawi imeneyinso nʼkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka mʼdziko la Igupto. Ndipo Ababuloni amene anali atazinga Yerusalemu atamva zimenezi, anachoka ku Yerusalemuko.

6Tsono Yehova anawuza mneneri Yeremiya kuti, 7“Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto. 8Ndipo Ababuloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Iwo adzawugonjetsa ndi kuwutentha.

9“Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani! 10Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”

11Gulu lankhondo la Ababuloni litaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao, 12Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu ndi kumapita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake. 13Koma atafika pa Chipata cha Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anagwira mneneri Yeremiyayo ndipo anati, “Iwe ukuthawira kwa Ababuloni!”

14Yeremiya anati, “Zimenezo si zoona! Ine sindikuthawira kwa Ababuloni.” Koma Iriya sanamumvere. Mʼmalo mwake anagwira Yeremiya nʼkupita naye kwa akuluakulu. 15Akuluakuluwo anamupsera mtima Yeremiya ndipo anamukwapula ndi kumuyika mʼnyumba ya mlembi Yonatani, imene anayisandutsa ndende.

16Yeremiya anayikidwa mʼndende ya pansi pa nthaka, kumene anakhalako nthawi yayitali. 17Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?”

Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.”

18Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo kapena akuluakulu anu kapenanso anthu awa, kuti mundiyike mʼndende? 19Kodi ali kuti aneneri anu amene anakuloserani kuti, ‘Mfumu ya ku Babuloni sidzakuthirani nkhondo pamodzi ndi dziko lino’? 20Koma tsopano, mbuye wanga mfumu, chonde tamverani. Loleni ndinene pempho langa pamaso panu: Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuopa kuti ndingakafere kumeneko.”

21Tsono Mfumu Zedekiya analamula kuti Yeremiya asungidwe mʼbwalo la alonda. Ankamupatsa buledi tsiku ndi tsiku amene ankamugula kwa ophika buledi. Anapitiriza kutero mpaka buledi yense anatha mu mzindamo. Choncho Yeremiya anapitirira kukhala mʼbwalo la alonda.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Иеремия 37:1-21

Иеремия в темнице

1Навуходоносор, царь Вавилона, поставил Цедекию, сына Иосии, царём Иудеи, и он правил вместо Иехонии, сына Иоакима. 2Ни он, ни его слуги, ни народ страны не слушали слов Вечного, произнесённых через пророка Иеремию. 3Однако царь Цедекия послал Юхала, сына Шелемии, со священнослужителем Софонией, сыном Маасеи, к пророку Иеремии, чтобы сказать: «Прошу тебя, помолись о нас Вечному, нашему Богу».

4Иеремия тогда ещё жил свободно среди народа, потому что ещё не был брошен в темницу. 5Войско фараона выступило из Египта, и вавилоняне, которые осаждали Иерусалим, услышав об этом, отступили из-под Иерусалима.

6И было к пророку Иеремии слово Вечного:

7– Так говорит Вечный, Бог Исроила: Скажите царю Иудеи, который послал вас спросить Меня: «Войско фараона, которое выступило тебе на помощь, вернётся в свою собственную землю, в Египет, 8а вавилоняне вернутся и нападут на этот город; они захватят его и сожгут».

9Так говорит Вечный: Не обманывайте себя, думая, что вавилоняне непременно отойдут от вас. Они не отойдут. 10Даже если бы вы одолели всё войско вавилонян, выступившее против вас, и только раненые остались бы у них в палатках, то и они вышли бы и сожгли этот город.

11После того как вавилонское войско отступило из-под Иерусалима из-за приближения войск фараона, 12Иеремия тронулся в путь из Иерусалима в землю Вениамина, чтобы получить свою долю имущества среди своих родственников. 13Когда он добрался до Вениаминовых ворот, начальник стражи по имени Ирия, сын Шелемии, сына Ханании, задержал его и сказал:

– Ты хочешь перебежать к вавилонянам!

14– Неправда! – сказал Иеремия. – Я не собираюсь перебегать к вавилонянам.

Но Ирия не стал его слушать; он взял Иеремию под стражу и отвёл его к приближённым царя. 15Они разгневались на Иеремию и велели избить его и посадить под замок в доме писаря Ионафана, в котором они устроили темницу.

16Иеремию бросили в зиндан, где он провёл много дней. 17Потом царь Цедекия послал за ним. Пророка привели, и царь тайно расспрашивал его у себя во дворце:

– Есть ли какое слово от Вечного?

– Есть, – ответил Иеремия. – Ты будешь отдан в руки царя Вавилона.

18Иеремия сказал царю Цедекии:

– Какое преступление я совершил против тебя, твоих приближённых или этого народа, что вы бросили меня в темницу? 19Где ваши пророки, которые пророчествовали вам: «Царь Вавилона не пойдёт против вас и против этой страны»? 20Но сейчас, умоляю, выслушай, господин мой царь. Позволь обратиться с просьбой к тебе: не отсылай меня назад в дом писаря Ионафана, иначе я умру там.

21Царь Цедекия приказал заточить Иеремию в темницу при царском дворце и выдавать ему с улицы пекарей по лепёшке в день, пока в городе ещё был хлеб. Так Иеремия остался в царской темнице.