Yeremiya 3 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 3:1-25

1“Ngati munthu asudzula mkazi wake

ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,

kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?

Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?

Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.

Komabe bwerera kwa ine,”

akutero Yehova.

2“Tayangʼana ku zitunda zowuma.

Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?

Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,

ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.

Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu

ndi ntchito zanu zoyipa.

3Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,

ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.

Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;

ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.

4Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanena

kuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,

5kodi mudzandikwiyira nthawi zonse?

Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’

Umu ndimo mmene umayankhulira,

koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.”

Kusakhulupirika kwa Israeli

6Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko. 7Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi. 8Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo. 9Chiwerewere cha Israeli chinali chochititsa manyazi kotero kuti chinayipitsa dziko lonse. Anachita chigololo popembedza mafano a miyala ndi mitengo. 10Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akutero Yehova.

11Yehova anandiwuza kuti, “Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda. 12Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti,

“ ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova.

‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale,

pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova.

‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale.

13Ungovomera kulakwa kwako

kuti unawukira Yehova Mulungu wako.

Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo

pansi pa mtengo uliwonse wogudira,

ndiponso kuti sunandimvere,’ ”

akutero Yehova.

14“Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse. 15Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha. 16Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,”

akutero Yehova.

17Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa. 18Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.

19“Ine mwini ndinati,

“ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga

ndikukupatsani dziko labwino kwambiri,

cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’

Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’

ndi kuti simudzaleka kunditsata.

20Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,

momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,”

akutero Yehova.

21Mawu akumveka pa magomo,

Aisraeli akulira ndi kupempha chifundo

chifukwa anatsata njira zoyipa

ndi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.

22Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika;

ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.”

“Inde, tidzabwerera kwa Inu

pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.

23Ndithu kupembedza pa magomo

komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu.

Zoonadi chipulumutso cha Israeli

chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.

24Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu

la ntchito za makolo athu,

nkhosa ndi ngʼombe zawo,

ana awo aamuna ndi aakazi.

25Tilekeni tigone pansi mwa manyazi,

ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe.

Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu,

ife pamodzi ndi makolo athu

kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino

sitinamvere Yehova Mulungu wathu.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 3:1-25

1耶和华说:“如果丈夫休掉妻子,

妻子离去另嫁别人,

前夫怎会再娶她呢?

那样做岂不完全玷污了土地吗?

你曾与许多情人苟合,

现在要归向我吗?

2“你举目看看那些光秃的高山,

哪里没有被你玷污过呢?

你坐在路旁等候情郎,

就像旷野的游牧者,

你的淫乱恶行玷污了土地。

3因此,秋雨不降,

春雨不来。

你却仍然不知羞耻,

一副娼妓的嘴脸。

4你不是刚对我说,

‘我父啊!你从我年幼时就做我的朋友。

5难道你会永远发怒、

怀恨到底吗?’

你虽然这样说,

却仍大肆作恶。”

呼吁不忠的以色列悔改

6约西亚王执政期间,耶和华对我说:“你看见以色列的不忠不贞了吗?她在高山上、在绿荫下放纵情欲。 7我以为她放纵之后会回到我身边,她却执迷不悟。她不忠的妹妹犹大也看见了这事。 8因为以色列不忠贞,我给她休书,把她休掉。她不忠的妹妹犹大却不害怕,竟也去淫乱。 9以色列肆意淫乱,拜石头木头,玷污了土地。 10尽管如此,她不忠的妹妹犹大只是假装归向我,并不诚心。这是耶和华说的。”

11耶和华对我说:“不忠贞的以色列比奸诈的犹大罪过还轻。 12你去向北方宣告,

“‘耶和华说,

不忠贞的以色列啊,回转吧!

我必不向你们发怒,

因为我充满慈爱,

不会永远怀怒。’

这是耶和华说的。

13‘你必须要承认自己的罪,

承认背叛了你的上帝耶和华,

在绿荫树下祭拜各种外邦的神明,

不听从我的话。’

这是耶和华说的。

14“‘不忠贞的子民啊,回转吧!

因为我是你们的主人3:14 主人”或译作“丈夫”。

我要从你们中间选些人带回锡安

每座城邑或每个宗族选一两个人。’

这是耶和华说的。

15“我要赐给你们合我心意的牧人,让他们用知识与智慧牧养你们。 16你们在地上繁衍昌盛的时候,人们不会再提及耶和华的约柜,不会再把它放在心上,不会再感到需要它,也不会再造一个。这是耶和华说的。 17那时,耶路撒冷会被称为‘耶和华的宝座’,万国都要聚集在耶路撒冷敬拜耶和华,不再执迷不悟地作恶。 18那时,犹大人必与以色列人一同从北方来到我赐给你们祖先作基业的地方。

19“我曾想,我多么愿意把你们当成我的儿女,

赐给你们万国中最肥美的土地。

我原以为你们会叫我‘父亲’,

再不离弃我。

20然而,以色列人啊!

你们竟对我不忠,

就像妻子不忠于丈夫。

这是耶和华说的。”

21从光秃的山头传来声音,

以色列子民哭泣呼求的声音,

因为他们走入歧途,

忘掉了他们的上帝耶和华。

22耶和华说:“不忠贞的子民啊,

归来吧!

我要医治你们不忠贞的病。”

他们说:“是的,我们要到你面前,

因为你是我们的上帝耶和华。

23在高山丘陵上狂欢、

拜偶像真是枉然,

唯有我们的上帝耶和华才能拯救以色列

24“从我们年幼时,那些可耻的神像就吞噬了我们祖先辛苦得来的牛羊和儿女。 25我们躺在自己的羞耻中,让我们的耻辱遮盖我们吧!因为我们和我们的祖先都得罪了我们的上帝耶和华,我们自幼至今一直没有顺服我们的上帝耶和华。”