Yeremiya 28 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 28:1-17

Hananiya Atsutsana ndi Yeremiya

1Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinayi, poyambirira pa ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, amene amachokera ku Gibiyoni, anandiwuza ine mʼNyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti, 2“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni. 3Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni. 4Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ”

5Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anasonkhana mʼNyumba ya Yehova. 6Anati, “Ameni! Yehova achitedi zomwezo! Yehova akwaniritse mawu amene waloserawo. Iye abweretsenso pa malo pano ziwiya za mʼNyumba ya Yehova ndi akapolo onse kuchokera ku Babuloni. 7Komabe, tamvera zimene nditi ndikuwuze iweyo pamodzi ndi anthu onse: 8Kunali aneneri kalelo, ine ndi iwe tisanabadwe. Iwowa analosera za nkhondo, mavuto ndi mliri kuti zidzagwera mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu. 9Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”

10Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola, 11ndipo anawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Umu ndi mmene ndidzathyolere goli la Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonse pasanathe zaka ziwiri.’ ” Zitatero, mneneri Yeremiya anachoka.

12Patapita nthawi pangʼono, mneneri Hananiya atathyola goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anawuza Yeremiya kuti, 13“Pita, kawuze mneneri Hananiya kuti, ‘Yehova akuti: Iwe wathyola goli lamtengo, mʼmalo mwake Ine ndidzayika goli lachitsulo. 14Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo iwo adzamutumikiradi. Ndipo ndamupatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”

15Ndipo mneneri Yeremiya anawuza mneneri Hananiya kuti, “Tamvera, Hananiya! Iweyo Yehova sanakutume, koma iwe wanyenga anthuwa kuti akhulupirire zabodza. 16Nʼchifukwa chake Yehova akuti, ‘Ndatsala pangʼono kukuchotsa pa dziko lapansi. Iwe ufa chaka chino chisanathe, chifukwa wakhala ukulalikira zowukira Yehova.’ ”

17Mʼmwezi wachisanu ndi chiwiri wa chaka chomwecho, mneneri Hananiya anamwaliradi.

New Russian Translation

Иеремия 28:1-17

Иеремия и лжепророк Ханания

1В пятом месяце того же года, четвертого года28:1 В середине лета 593 г. до н. э., в начале правления Цедекии, царя Иудеи, пророк Ханания, сын Азура, из Гаваона сказал мне в доме Господнем при священниках и при всем народе:

2– Так говорит Господь Сил, Бог Израиля: «Я разобью ярмо царя вавилонского. 3Не пройдет двух лет, как Я верну сюда всю утварь дома Господня, которую Навуходоносор, царь Вавилона, забрал отсюда и увез в Вавилон. 4Я верну сюда и иудейского царя Иехонию, сына Иоакима, и всех остальных пленников из Иудеи, которых увели в Вавилон, – возвещает Господь, – потому что Я разобью ярмо царя Вавилона».

5И пророк Иеремия ответил пророку Ханании при священниках и при всем народе, который стоял в доме Господнем. 6Он сказал:

– Аминь! Пусть Господь сделает так! Пусть Господь исполнит слова твоего пророчества, вернув сюда из Вавилона утварь Господнего дома и всех пленников. 7Но послушай-ка, что я скажу тебе и всему этому народу: 8пророки, что были до тебя и до меня, издревле пророчили многим странам и великим царствам войны, невзгоды и мор. 9Но пророка, который предсказывал мир, признавали истинным Господним посланником лишь тогда, когда его пророчество сбывалось.

10Тогда пророк Ханания снял ярмо с шеи пророка Иеремии, разбил его 11и сказал всему народу:

– Так говорит Господь: «Не пройдет двух лет, как Я так же разобью ярмо, которое Навуходоносор, царь Вавилона, надел на шею всех народов».

И пророк Иеремия пошел своей дорогой. 12Вскоре после того, как пророк Ханания разбил ярмо, надетое на шею пророка Иеремии, было слово Господне к Иеремии:

13– Иди и скажи Ханании: «Так говорит Господь: Ты разбил деревянное ярмо, но его сменит ярмо железное. 14Так говорит Господь Сил, Бог Израиля: Я надену на шею всех этих народов ярмо из железа, чтобы заставить их служить Навуходоносору, царю Вавилона, и они будут ему служить. Я дам ему власть даже над дикими зверями».

15И пророк Иеремия сказал пророку Ханании:

– Послушай, Ханания! Господь не посылал тебя. Ты заставил этот народ поверить лжи. 16«За это так говорит Господь: Я сотру тебя с лица земли. В этом году ты умрешь за то, что призывал к отступничеству от Господа».

17И в седьмом месяце того же года пророк Ханания умер.