Yeremiya 26 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 26:1-24

Yeremiya Amangidwa

1Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda atayamba kulamulira, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2“Kayime mʼbwalo la Nyumba ya Yehova. Ndipo ukayankhule kwa anthu onse okhala mʼmizinda ya ku Yuda amene amabwera kudzapembedza ku Nyumba ya Yehova. Ukawawuze zonse zomwe ndakulamula; usakasiyeko ndi mawu amodzi omwe. 3Mwina mwake adzamvera, ndipo aliyense adzatembenuka kuleka njira yake yoyipa. Ndiye ine ndidzaleka osapatsa chilango chimene ndinakonzekera kuti ndiwalange nacho chifukwa cha ntchito zawo zoyipa. 4Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani, 5ndipo ngati simumvera mawu a atumiki anga, aneneri amene ndakhala ndikukutumizirani, ngakhale kuti simunawamvere, 6ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ”

7Ansembe, aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya akuyankhula mawu amenewa mʼNyumba ya Yehova. 8Yeremiya atangotsiriza kuwawuza anthu aja zonse zimene Yehova anamulamula kuti ayankhule, ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse anamugwira ndipo anati, “Uyenera kuphedwa! 9Chifukwa chiyani walosera mʼdzina la Yehova kuti Nyumba ino idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala wopanda anthu ngati chipululu?” Anthu onse anamuzungulira Yeremiya mʼNyumba ya Yehova.

10Koma nduna za ku Yuda zitamva zomwe zinachitikazi, zinanyamuka kuchokera ku nyumba yaufumu kupita ku Nyumba ya Yehova, nakakhala pamalo pawo, pa Chipata Chatsopano cha Nyumba ya Yehova. 11Pamenepo ansembe ndi aneneri anawuza ndunazo pamodzi ndi anthu onse kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa chifukwa amalosera zoyipira mzinda uno. Inu mwadzimvera nokha zimenezi!”

12Ndipo Yeremiya anawuza nduna zija ndi anthu onse kuti, “Yehova anandituma kunenera mawu onse amene mwawamva otsutsa Nyumba ino ndi mzinda uno. 13Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu ndipo mverani Yehova Mulungu wanu. Mukatero ndiye kuti Yehova adzaleka osakupatsani chilango chimene ankati akupatseni. 14Kunena za ine, ndili mʼmanja mwanu; mundichite chilichonse chimene mukuganiza kuti ndi chabwino ndi choyenera. 15Komatu dziwani kuti ngati mundipha, inu pamodzi ndi mzinda uno ndi onse amene amakhala muno, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi Yehova anandituma kuti ndidzayankhule mawu onsewa inu mukumva.”

16Pamenepo ndunazo pamodzi ndi anthu onse anawuza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthu uyu sayenera kuphedwa! Pakuti wayankhula kwa ife mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.”

17Akuluakulu ena a mʼdzikomo anayimirira ndi kuwuza gulu lonse la anthu kuti, 18“Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,

Yerusalemu adzasanduka bwinja,

ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’

19Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!”

20(Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya. 21Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto. 22Komabe Mfumu Yehoyakimu anatuma Elinatani mwana wa Akibori pamodzi ndi anthu ena, ku Igupto. 23Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba).

24Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye anateteza Yeremiya, motero sanamupereke kwa anthu kuti amuphe.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

耶利米書 26:1-24

耶利米被捕

1猶大約西亞的兒子約雅敬執政初期,耶和華對耶利米說: 2「這是耶和華說的,『你要站在我殿的院子裡,把我吩咐你的話一字不漏地告訴從猶大各城前來敬拜的人。 3或許他們會聽從我的話,改邪歸正,那樣我會施憐憫,取消原本用來懲治他們罪惡的災禍。 4你要告訴他們,耶和華這樣說,「如果你們不聽從我的話,不遵行我賜給你們的律法, 5不聽從我屢次派我的僕人——眾先知傳給你們的話, 6我必使這殿像示羅一樣被毀,使耶路撒冷被萬國咒詛。」』」

7祭司、先知和民眾都聽見了耶利米在耶和華的殿裡說的這些話。 8耶利米傳達完耶和華的話之後,祭司、先知和民眾就抓住他,說:「你真該死! 9你為什麼奉耶和華的名預言這殿必像示羅一樣被毀,這城必要荒無人煙呢?」於是,他們在耶和華的殿裡把耶利米圍了起來。

10猶大的首領得知後,就離開王宮,上到耶和華的殿,坐在耶和華殿新門的入口。 11祭司和先知對官員和民眾說:「這人該被處死!因為他預言這城要被毀,這是你們親耳聽到的。」

12耶利米對官員和民眾說:「你們剛才聽見的這些關於這殿和這城的預言都是耶和華差我說的。 13你們要改邪歸正,聽從你們上帝耶和華的話,這樣耶和華必施憐憫,取消本來要降給你們的災禍。 14至於我,我已落在你們手中,你們認為怎樣好就怎樣待我吧! 15不過,你們要知道,如果你們置我於死地,你們和這城及城中的居民必擔當濫殺無辜的罪,因為確實是耶和華派我來告訴你們這些預言的。」

16官員和民眾便對祭司和先知說:「這人不該被處死,因為他是奉我們上帝耶和華的名對我們說話。」 17有幾個長老站起來對眾人說: 18猶大希西迦執政期間,摩利沙彌迦猶大眾人預言說,

『萬軍之耶和華說錫安必被夷為平地,

耶路撒冷必淪為廢墟,

聖殿山要成為一片荒林。』

19「但猶大希西迦猶大眾人並沒有處死他。希西迦敬畏耶和華,求祂開恩,耶和華才施憐憫,沒有把原本預備的災禍降給他們。若處死這人,我們會大禍臨頭。」

20當時,基列·耶琳示瑪雅的兒子烏利亞也奉耶和華的名預言這城和這地方將被毀,內容與耶利米說的一樣。 21約雅敬王和他的王公大臣聽見烏利亞的話,就想處死他。烏利亞得知後,嚇得逃到埃及去了。 22約雅敬王便派亞革波的兒子以利拿單率隨從去埃及捉拿他。 23他們把烏利亞埃及押到約雅敬王面前,王用刀殺了他,把屍首拋在平民的墳地中。 24然而,沙番的兒子亞希甘保護耶利米,他才沒被交給民眾處死。