Yeremiya 25 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 25:1-38

Zaka 70 za Ukapolo

1Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. 2Choncho mneneri Yeremiya anawuza anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi onse amene amakhala mu Yerusalemu kuti: 3Kwa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda mpaka lero lino, Yehova wakhala akundipatsa mauthenga ake ndipo ine ndakhala ndikuyankhula ndi inu kawirikawiri, koma inu simunamvere.

4Ndipo ngakhale Yehova kawirikawiri wakhala akukutumizirani atumiki ake onse, aneneri, inuyo simunamvere kapena kutchera khutu. 5Aneneriwo ankanena kuti, “Ngati aliyense wa inu abwerere, kusiya njira zake zoyipa ndi machitidwe ake oyipa, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko limene Yehova anapereka kwa makolo anu kwamuyaya. 6Musatsatire milungu ina nʼkuyitumikira ndi kuyipembedza. Musapute mkwiyo wanga ndi mafano amene mwapanga ndi manja anu. Mukatero Ine sindidzakuwonongani.

7“Koma inu simunandimvere,” akutero Yehova, “ndipo munaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene munapanga ndi manja anu. Choncho munadziwononga nokha.”

8Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Chifukwa simunamvere mawu anga, 9ndidzayitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni,” akutero Yehova, “ndipo adzathira nkhondo dziko lino ndi anthu ake pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ozungulira dzikoli. Ndidzawawononga kwathunthu ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka, mpaka muyaya. 10Ndidzathetsa mfuwu wachimwemwe ndi wachisangalalo, mawu a mkwati ndi mkwatibwi, phokoso la mphero ndi kuwala kwa nyale. 11Dziko lonse lidzakhala bwinja ndi chipululu, ndipo mitundu ina idzatumikira mfumu ya ku Babuloni kwa 70.

12“Koma zaka 70 zikadzatha, ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi anthu ake, chifukwa cha zolakwa zawo,” akutero Yehova, “ndipo dziko lawo lidzakhala chipululu mpaka muyaya. 13Ndidzachita zinthu zonse zimene ndinayankhula zotsutsa dzikolo, zonse zimene zalembedwa mʼbuku lino, ndiponso zonse zimene Yeremiya analosera zotsutsa anthu amenewa. 14Iwo eni adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi mafumu amphamvu. Ndidzawabwezera molingana ndi zochita zawo ndi ntchito za manja awo.”

Chikho cha Ukali wa Mulungu

15Yehova, Mulungu wa Israeli, anandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi vinyo wa ukali wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene ndikukutuma. 16Akadzamwa adzayamba kudzandira ndi kuchita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikuyitumiza pakati pawo.”

17Choncho ine ndinatenga chikhocho mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse ya anthu kumene Iye ananditumako: 18Anandituma ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Yuda, kwa mafumu ake ndi nduna zake kuti ndikawasandutse ngati bwinja ndi chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka ndiponso chotembereredwa, monga mmene alili lero lino. 19Ananditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Igupto, kwa atumiki ake, nduna zake ndi kwa anthu ake onse, 20ndi kwa anthu ena onse a mitundu yachilendo; mafumu onse a ku Uzi; mafumu onse a Afilisti, a ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekroni ndiponso kwa anthu a ku chigwa chotsala cha Asidodi; 21Edomu, Mowabu ndi Amoni. 22Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Turo ndi ku Sidoni; kwa mafumu a kutsidya la nyanja; 23ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa chamʼmbali. 24Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi mafumu onse a anthu achilendo amene amakhala mʼchipululu. 25Anandituma kwa mafumu onse a ku Zimuri, Elamu ndi Mediya; 26ndiponso kwa mafumu onse a kumpoto, akufupi ndi kutali omwe, mafumu onse a dziko lapansi. Ndipo potsiriza pake, idzamwenso ndi mfumu Sesaki.

27“Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Imwani, ledzerani ndipo musanze, mugwe osadzukanso chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ 28Koma ngati akana kutenga chikhocho mʼdzanja lako ndi kumwa, uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Muyenera kumwa ndithu!’ ” 29Taonani, tsopano ndiyamba kulanga mzinda uno umene umadziwika ndi dzina langa. Kodi inu muganiza kuti simudzalangidwa? Ayi, simudzapulumuka chifukwa ndikutumiza nkhondo pa onse okhala pa dziko lapansi, akutero Yehova Wamphamvuzonse.

30“Tsopano iwe nenera mawu owatsutsa ndipo uwawuze kuti,

“ ‘Yehova adzabangula kumwamba;

mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika.

Adzabangula mwamphamvu kukalipira dziko lake.

Iye adzafuwula ngati anthu oponda mphesa,

kukalipira onse amene akukhala pa dziko lapansi.

31Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi,

chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse;

adzaweruza mtundu wonse wa anthu

ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’ ”

akutero Yehova.

32Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Taonani! Mavuto akuti akachoka

pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina;

mphepo ya mkuntho ikuyambira

ku malekezero a dziko.”

33Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Yehova adzangoti mbwee ponseponse, pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzawalire kapena kusonkhanitsa mitemboyo kuti ikayikidwe mʼmanda, koma idzakhala mbwee ngati ndowe.

34Khetsani misozi ndi kufuwula mwamphamvu, abusa inu;

gubudukani pa fumbi, inu atsogoleri a nkhosa.

Pakuti nthawi yanu yophedwa yafika;

mudzagwa ndi kuphwanyika ngati mbiya yabwino kwambiri.

35Abusa adzasowa kothawira,

atsogoleri a nkhosa adzasowa malo opulumukira.

36Imvani kulira kwa abusa,

atsogoleri a nkhosa akulira,

chifukwa Yehova akuwononga msipu wawo.

37Makola awo a nkhosa amene anali pamtendere adzasanduka bwinja

chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.

38Ngati mkango, Yehova wasiya phanga lake,

pakuti dziko lawo lasanduka chipululu

chifukwa cha nkhondo ya owazunza

ndiponso chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.