Yeremiya 23 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 23:1-40

Nthambi Yolungama

1“Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova. 2Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova. 3“Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana. 4Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.

5Yehova akuti, “Masiku akubwera,

pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka.

Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.

6Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka

ndipo Israeli adzakhala pamtendere.

Dzina limene adzamutcha ndi ili:

Yehova ndiye Chilungamo Chathu.

7Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’ 8koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”

Aneneri Onyenga

9Kunena za aneneri awa:

Mtima wanga wasweka;

mʼnkhongono mwati zii.

Ndakhala ngati munthu woledzera,

ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo,

chifukwa cha Yehova

ndi mawu ake opatulika.

10Dziko ladzaza ndi anthu achigololo;

lili pansi pa matemberero.

Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma.

Aneneri akuchita zoyipa

ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.

11“Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova.

Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,”

akutero Yehova.

12“Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera;

adzawapirikitsira ku mdima

ndipo adzagwera kumeneko.

Adzaona zosaona

mʼnthawi ya chilango chawo,”

akutero Yehova.

13“Pakati pa aneneri a ku Samariya

ndinaona chonyansa ichi:

Ankanenera mʼdzina la Baala

ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.

14Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu

ndaonapo chinthu choopsa kwambiri:

amachita chigololo, amanena bodza

ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa.

Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake.

Kwa Ine anthu onsewa

ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”

15Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Ndidzawadyetsa zakudya zowawa

ndi kuwamwetsa madzi a ndulu,

chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse

ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”

16Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu;

zomwe aloserazo nʼzachabechabe.

Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi,

osati zochokera kwa Yehova.

17Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti,

‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’

Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti,

‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”

18Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova?

Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake?

Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?

19Taonani ukali wa Yehova

uli ngati chimphepo chamkuntho,

inde ngati namondwe.

Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.

20Mkwiyo wa Yehova sudzaleka

mpaka atachita zonse zimene

anatsimikiza mu mtima mwake.

Mudzazizindikira bwino zimenezi

masiku akubwerawa.”

21Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa,

komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo;

Ine sindinawayankhule,

komabe iwo ananenera.

22Iwo akanakhala pa msonkhano wanga

ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga.

Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa

kuti aleke machimo awo.”

23Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,

ndiye sindine Mulungu?

24Kodi wina angathe kubisala

Ine osamuona?”

“Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”

Akutero Yehova.

25“Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ 26Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo. 27Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala. 28Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga? 29Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.

30Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.” 31Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ” 32Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.

Uthenga Wabodza ndi Aneneri Abodza

33Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’ 34Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake. 35Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’ 36Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. 37Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’ 38Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule, 39ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu. 40Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 23:1-40

将来的盼望

1耶和华说:“那些本应像牧人照顾羊群一样统治我子民的人有祸了!因为他们残害、驱散我的子民。” 2以色列的上帝耶和华这样斥责那些统治祂子民的首领:“你们驱散我的子民,没有照顾他们。看啊,我必因你们的恶行而惩罚你们。这是耶和华说的。 3我要把我幸存的子民从我流放他们去的各地召集起来,领他们回到故土,使他们子孙兴旺。 4我要派首领照顾他们,使他们不再担惊受怕,也不再有一人迷失。这是耶和华说的。”

5耶和华说:“看啊,时候将到,我要为大卫选立一个公义的苗裔,使他执掌王权。他必秉公行义,治国有方。 6在他掌权的日子,犹大必得拯救,以色列必国泰民安。他将被称为‘耶和华是我们的公义’。”

7耶和华说:“看啊,时候将到,那时人不再凭把以色列人带出埃及的耶和华起誓, 8而是凭把他们从流放之地——北方和列国领回来的永活耶和华起誓。他们必在自己的国土上安居乐业。”

9论到那些先知,

我的心都碎了,

我的骨头都颤抖。

因为耶和华和祂圣言的缘故,

我好像不胜酒力的醉汉。

10这里到处是拜偶像的人,

他们行为邪恶,滥用权力。

大地因受咒诅而悲哀,

旷野的草场都枯干了。

11耶和华说:“先知和祭司都不敬虔,

我甚至看见他们在我的圣殿里行恶。

12因此,他们必被赶到黑暗中,

在湿滑的路上跌倒,

因为我必在报应的日子降灾祸给他们。

这是耶和华说的。

13我看见撒玛利亚的先知行为可憎,

他们靠巴力说预言,

引诱我的子民走入歧途。

14我也看见耶路撒冷的先知行为可恶,

他们通奸,谎话连篇,

怂恿恶人,

以致无人悔过自新。

在我眼中,耶路撒冷人就像 所多玛人和蛾摩拉人一样败坏。

15因此,论到这些先知,

万军之耶和华说,

‘看啊,我要使他们吃苦艾,

喝毒药,因为亵渎之风从耶路撒冷的先知那里蔓延,

遍及全境。’”

16万军之耶和华对祂的子民说:“你们不要听信这些先知的预言,他们使你们充满虚假的盼望,他们的预言是自己编的,不是耶和华说的。 17他们不断对藐视我的人说,‘耶和华说你们必安享太平。’他们对那些执迷不悟的人说,‘灾祸不会降到你们身上。’

18“然而,他们谁曾站在耶和华面前看见并听见祂说话呢?

他们谁曾留心听祂的话呢?

19看啊,耶和华的怒气像暴风一样袭来,

像旋风一样吹到恶人头上。

20耶和华不完成祂心中的计划决不息怒。

将来你们会清楚地明白这一切。

21“我没有差遣这些先知,

他们却妄自行动;

我没有对他们说话,

他们却乱发预言。

22他们若曾站在我面前听我说话,

早就向我的子民宣告我的话,

使他们改邪归正了。”

23耶和华说:“我是无处不在的上帝。” 24耶和华说:“难道人藏起来我就看不见了吗?我岂不是充满天地之间吗?这是耶和华说的。 25我听见假先知奉我的名说,‘上帝托梦给我了!上帝托梦给我了!’ 26这些先知谎话连篇,凭空预言要到何时呢? 27他们彼此传讲所做的梦,想借此使我的子民忘记我,正如他们的祖先因祭拜巴力而忘记了我。 28让做梦的先知尽管宣扬他们的梦吧,但得到我话语的先知要忠心地传达我的话。糠秕怎能与麦子相比呢!这是耶和华说的。” 29耶和华说:“难道我的话不像火吗?不像击碎岩石的铁锤吗?” 30耶和华说:“看啊,我要对付那些假先知,他们盗用同伙的话,却妄称是我的话。” 31耶和华说:“看啊,我要对付那些假先知,他们妄自说预言,却谎称是耶和华的话。” 32耶和华说:“看啊,我要对付那些假先知,他们谎称我托梦给他们,四处宣扬,用弥天大谎把我的子民引入歧途。其实我并没有差遣他们,也没有委派他们,他们对我的子民毫无益处。这是耶和华说的。”

33耶和华说:“耶利米啊,如果有百姓、先知或祭司问你,‘耶和华有什么启示?’你要对他们说,‘你们就是耶和华的重担23:33 重担”希伯来文也有“启示”的意思。,耶和华说要丢弃你们。’ 34如果有先知、祭司或百姓宣称有耶和华的启示,我必惩罚他和他全家。 35你们各人要问自己的亲友,‘耶和华有什么答复?’或‘耶和华说了什么?’ 36你们不可再说有耶和华的启示,因为你们把自己的话当成祂的启示,曲解你们永活的上帝——万军之耶和华的话。 37耶利米啊,你要这样问先知,‘耶和华有什么答复?耶和华说了什么?’ 38如果他们说,‘这是耶和华的启示。’你就说,‘耶和华说,你们无视我的警告,宣称有我的启示, 39我必彻底忘记你们,把你们和我赐给你们及你们祖先的城邑抛弃。 40我要使你们永远蒙羞受辱、遗臭万年。’”