Yeremiya 20 – CCL & CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 20:1-18

Yeremiya ndi Pasuri

1Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi. 2Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova. 3Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse. 4Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo. 5Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni. 6Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ”

Madandawulo a Yeremiya

7Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi;

Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana.

Anthu akundinyoza tsiku lonse.

Aliyense akundiseka kosalekeza.

8Nthawi iliyonse ndikamayankhula,

ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka!

Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka

ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse.

9Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye

kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,”

mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga,

amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga.

Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa,

koma sindingathe kupirirabe.

10Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti,

“Zoopsa ku mbali zonse!

Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!”

Onse amene anali abwenzi anga

akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti,

“Mwina mwake adzanyengedwa;

tidzamugwira

ndi kulipsira pa iye.”

11Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu.

Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana.

Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana.

Manyazi awo sadzayiwalika konse.

12Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama

ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu.

Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga

popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.

13Imbirani Yehova!

Mutamandeni Yehova!

Iye amapulumutsa wosauka

mʼmanja mwa anthu oyipa.

14Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!

Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!

15Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga

ndi uthenga woti:

“Kwabadwa mwana wamwamuna!”

16Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene

Yehova anayiwononga mopanda chisoni.

Amve mfuwu mmawa,

phokoso la nkhondo masana.

17Chifukwa sanandiphere mʼmimba,

kuti amayi anga asanduke manda anga,

mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.

18Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni

kuti moyo wanga

ukhale wamanyazi wokhawokha?