Yeremiya 2 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 2:1-37

Aisraeli Asiya Mulungu

1Yehova anandiwuza kuti, 2“Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti,

“ ‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako,

mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi,

mmene unkanditsata mʼchipululu muja;

mʼdziko losadzalamo kanthu.

3Israeli anali wopatulika wa Yehova,

anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola;

onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa

ndipo mavuto anawagwera,’ ”

akutero Yehova.

4Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo,

inu mafuko onse a Israeli.

5Yehova akuti,

“Kodi makolo anu anandipeza nʼcholakwa chanji,

kuti andithawe?

Iwo anatsata milungu yachabechabe,

nawonso nʼkusanduka achabechabe.

6Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti,

amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto

natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma

ndi lokumbikakumbika,

mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima,

dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’

7Ndinakufikitsani ku dziko lachonde

kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina.

Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langa

ndi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa.

8Ansembe nawonso sanafunse kuti,

‘Yehova ali kuti?’

Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe;

atsogoleri anandiwukira.

Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala,

ndi kutsatira mafano achabechabe.

9“Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,”

akutero Yehova.

“Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.

10Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone,

tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino;

ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe:

11Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene unasinthapo milungu yake?

(Ngakhale kuti si milungu nʼkomwe).

Koma anthu anga asinthitsa Mulungu wawo waulemerero

ndi mafano achabechabe.

12Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi,

ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,”

akutero Yehova.

13“Popeza anthu anga achita machimo awiri:

Andisiya Ine

kasupe wa madzi a moyo,

ndi kukadzikumbira zitsime zawo,

zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.

14Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi.

Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere?

15Adani ake abangulira

ndi kumuopseza ngati mikango.

Dziko lake analisandutsa bwinja;

mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.

16Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesi

akuphwanyani mitu.

17Zimenezitu zakuchitikirani

chifukwa munasiya Yehova Mulungu wanu

pamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu?

18Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto,

kukamwa madzi a mu Sihori?

Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya,

kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?

19Kuyipa kwanuko kudzakulangani;

kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani.

Tsono ganizirani bwino,

popeza ndi chinthu choyipa

kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu;

ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu.

Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.

20“Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu

ndi kudula msinga zanu;

munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’

Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere.

Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali

ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.

21Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika;

unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika.

Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesa

wachabechabe wonga wa kutchire?

22Ngakhale utasamba ndi soda

kapena kusambira sopo wambiri,

kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,”

akutero Ambuye Yehova.

23“Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse;

sindinatsatire Abaala’?

Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja;

zindikira bwino zomwe wachita.

Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro

yomangothamanga uku ndi uku,

24wakhala ngati mbidzi yozolowera mʼchipululu,

yonka ninunkhiza pa nthawi yachisika.

Ndani angayiretse chilakolako chakecho?

Mphongo iliyonse yoyikhumba sidzavutika.

Pa nthawi yachisika chakecho mphongoyo idzayipeza.

25Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi

ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu.

Koma unati, ‘Zamkutu!

Ine ndimakonda milungu yachilendo,

ndipo ndidzayitsatira.’

26“Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa,

moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi;

Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo,

ansembe ndi aneneri awo.

27Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’

ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’

Iwo andifulatira Ine,

ndipo safuna kundiyangʼana;

Koma akakhala pa mavuto amati,

‘Bwerani mudzatipulumutse!’

28Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha?

Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani

pamene muli pamavuto!

Inu anthu a ku Yuda,

milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.

29“Kodi mukundizengeranji mlandu?

Nonse mwandiwukira,”

akutero Yehova.

30“Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu;

iwo sanaphunzirepo kanthu.

Monga mkango wolusa,

lupanga lanu lapha aneneri anu.

31“Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova:

“Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israeli

kapena ngati dziko la mdima wandiweyani?

Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda;

sitidzabweranso kwa Inu’?

32Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake,

kapena kuyiwala zovala zake za ukwati?

Komatu anthu anga andiyiwala

masiku osawerengeka.

33Mumadziwa bwino njira zopezera zibwenzi!

Choncho ngakhale akazi oyipa omwe mumawaphunzitsa njira zanu.

34Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo

magazi a anthu osauka osalakwa.

Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba.

Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,

35inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa,

sadzatikwiyira.’

Ndidzakuyimbani mlandu

chifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’

36Chifukwa chiyani

mukunkabe nimusinthasintha njira zanu?

Aigupto adzakukhumudwitsani

monga momwe Asiriya anakuchititsani manyazi.

37Mudzachokanso kumeneko

manja ali kunkhongo.

Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira,

choncho sadzakuthandizani konse.

King James Version

Jeremiah 2:1-37

1Moreover the word of the LORD came to me, saying, 2Go and cry in the ears of Jerusalem, saying, Thus saith the LORD; I remember thee, the kindness of thy youth, the love of thine espousals, when thou wentest after me in the wilderness, in a land that was not sown.2.2 thee: or, for thy sake 3Israel was holiness unto the LORD, and the firstfruits of his increase: all that devour him shall offend; evil shall come upon them, saith the LORD. 4Hear ye the word of the LORD, O house of Jacob, and all the families of the house of Israel:

5¶ Thus saith the LORD, What iniquity have your fathers found in me, that they are gone far from me, and have walked after vanity, and are become vain? 6Neither said they, Where is the LORD that brought us up out of the land of Egypt, that led us through the wilderness, through a land of deserts and of pits, through a land of drought, and of the shadow of death, through a land that no man passed through, and where no man dwelt? 7And I brought you into a plentiful country, to eat the fruit thereof and the goodness thereof; but when ye entered, ye defiled my land, and made mine heritage an abomination.2.7 a plentiful…: or, the land of Carmel 8The priests said not, Where is the LORD? and they that handle the law knew me not: the pastors also transgressed against me, and the prophets prophesied by Baal, and walked after things that do not profit.

9¶ Wherefore I will yet plead with you, saith the LORD, and with your children’s children will I plead. 10For pass over the isles of Chittim, and see; and send unto Kedar, and consider diligently, and see if there be such a thing.2.10 over: or, over to 11Hath a nation changed their gods, which are yet no gods? but my people have changed their glory for that which doth not profit. 12Be astonished, O ye heavens, at this, and be horribly afraid, be ye very desolate, saith the LORD. 13For my people have committed two evils; they have forsaken me the fountain of living waters, and hewed them out cisterns, broken cisterns, that can hold no water.

14Is Israel a servant? is he a homeborn slave? why is he spoiled?2.14 spoiled: Heb. become a spoil? 15The young lions roared upon him, and yelled, and they made his land waste: his cities are burned without inhabitant.2.15 yelled: Heb. gave out their voice 16Also the children of Noph and Tahapanes have broken the crown of thy head.2.16 have…: or, feed on thy crown 17Hast thou not procured this unto thyself, in that thou hast forsaken the LORD thy God, when he led thee by the way? 18And now what hast thou to do in the way of Egypt, to drink the waters of Sihor? or what hast thou to do in the way of Assyria, to drink the waters of the river? 19Thine own wickedness shall correct thee, and thy backslidings shall reprove thee: know therefore and see that it is an evil thing and bitter, that thou hast forsaken the LORD thy God, and that my fear is not in thee, saith the Lord GOD of hosts.

20¶ For of old time I have broken thy yoke, and burst thy bands; and thou saidst, I will not transgress; when upon every high hill and under every green tree thou wanderest, playing the harlot.2.20 transgress: or, serve 21Yet I had planted thee a noble vine, wholly a right seed: how then art thou turned into the degenerate plant of a strange vine unto me? 22For though thou wash thee with nitre, and take thee much soap, yet thine iniquity is marked before me, saith the Lord GOD. 23How canst thou say, I am not polluted, I have not gone after Baalim? see thy way in the valley, know what thou hast done: thou art a swift dromedary traversing her ways;2.23 thou art…: or, O swift dromedary 24A wild ass used to the wilderness, that snuffeth up the wind at her pleasure; in her occasion who can turn her away? all they that seek her will not weary themselves; in her month they shall find her.2.24 A wild…: or, O wild ass, etc2.24 used: Heb. taught2.24 her pleasure: Heb. the desire of her heart2.24 turn…: or, reverse it? 25Withhold thy foot from being unshod, and thy throat from thirst: but thou saidst, There is no hope: no; for I have loved strangers, and after them will I go.2.25 There…: or, Is the case desperate? 26As the thief is ashamed when he is found, so is the house of Israel ashamed; they, their kings, their princes, and their priests, and their prophets, 27Saying to a stock, Thou art my father; and to a stone, Thou hast brought me forth: for they have turned their back unto me, and not their face: but in the time of their trouble they will say, Arise, and save us.2.27 brought…: or, begotten me2.27 their back: Heb. the hinder part of the neck 28But where are thy gods that thou hast made thee? let them arise, if they can save thee in the time of thy trouble: for according to the number of thy cities are thy gods, O Judah.2.28 trouble: Heb. evil

29Wherefore will ye plead with me? ye all have transgressed against me, saith the LORD. 30In vain have I smitten your children; they received no correction: your own sword hath devoured your prophets, like a destroying lion.

31¶ O generation, see ye the word of the LORD. Have I been a wilderness unto Israel? a land of darkness? wherefore say my people, We are lords; we will come no more unto thee?2.31 We are…: Heb. We have dominion 32Can a maid forget her ornaments, or a bride her attire? yet my people have forgotten me days without number. 33Why trimmest thou thy way to seek love? therefore hast thou also taught the wicked ones thy ways. 34Also in thy skirts is found the blood of the souls of the poor innocents: I have not found it by secret search, but upon all these.2.34 secret…: Heb. digging 35Yet thou sayest, Because I am innocent, surely his anger shall turn from me. Behold, I will plead with thee, because thou sayest, I have not sinned. 36Why gaddest thou about so much to change thy way? thou also shalt be ashamed of Egypt, as thou wast ashamed of Assyria. 37Yea, thou shalt go forth from him, and thine hands upon thine head: for the LORD hath rejected thy confidences, and thou shalt not prosper in them.