Yeremiya 17 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 17:1-27

1“Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,

lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.

Uchimowo walembedwa pa mitima yawo

ndiponso pa nyanga za maguwa awo.

2Ngakhale ana awo amakumbukira

maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,

pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,

pa mapiri aatali mʼdzikomo.

3Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense

ndidzazipereka kwa ofunkha

kuti zikhale dipo lawo

chifukwa cha machimo

ochitika mʼdziko lonse.

4Mudzataya dziko limene ndinakupatsani

kuti likhale cholowa chanu.

Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu

mʼdziko limene inu simukulidziwa,

chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,

ndipo udzayaka mpaka muyaya.”

5Yehova akuti,

“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,

amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize

pamene mtima wake wafulatira Yehova.

6Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;

iye sadzapeza zabwino.

Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,

mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.

7“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,

amene amatsamira pa Iye.

8Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi

umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.

Mtengowo suopa pamene kukutentha;

masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.

Suchita mantha pa chaka cha chilala

ndipo sulephera kubereka chipatso.”

9Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse

ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika.

Ndani angathe kuwumvetsa?

10“Ine Yehova ndimafufuza mtima

ndi kuyesa maganizo,

ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake

ndiponso moyenera ntchito zake.”

11Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo

ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.

Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,

ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.

12Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero

wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.

13Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,

onse amene amakusiyani adzachita manyazi.

Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi

chifukwa anakana Yehova,

kasupe wa madzi amoyo.

14Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;

pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,

chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.

15Anthu akumandinena kuti,

“Mawu a Yehova ali kuti?

Zichitiketu lero kuti tizione!”

16Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.

Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.

Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.

17Musandichititse mantha;

ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.

18Ondizunza anga achite manyazi,

koma musandichititse manyazi;

iwo achite mantha kwambiri,

koma ine mundichotsere manthawo.

Tsiku la mavuto liwafikire;

ndipo muwawononge kotheratu.

Kusunga Tsiku la Sabata

19Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu. 20Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’ 21Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu. 22Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu. 23Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga. 24Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli. 25Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya. 26Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova. 27Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 17:1-27

犹大的罪与罚

1犹大人的罪是用铁笔记录的,用钻石镌刻的,写在了他们心坎上和祭坛角上。 2他们的儿女没有忘记绿树下、高岗上、 3山野间的丘坛和亚舍拉神像。因为他们境内的罪恶,我必使敌人掳掠他们的财宝和神庙。 4他们必失去我赐给他们的产业,被敌人掳到异乡做奴隶,因为他们激起了我的怒火,永难熄灭。”

5耶和华说:

“信靠世人、倚靠血肉之躯、

背叛耶和华的人该受咒诅!

6这样的人毫无福乐,

像沙漠中的灌木。

他要住在旷野中干旱无人的盐碱地。

7信靠耶和华、倚靠耶和华的人有福了!

8这样的人像一棵栽在水边的树,

根扎入水中,

不怕炎热,不怕干旱,

绿叶如荫,不断结果。

9“人心比什么都诡诈,

无可救药,

谁能识透呢?

10我耶和华鉴察人心,

察看人的意念,

按照人的行为报应人。”

11谋取不义之财的人就像孵其他鸟蛋的鹧鸪,

他中年便会失去不义之财,

最后成了愚昧之人。

12我们的圣殿是从太初就矗立在高处的荣耀宝座。

13耶和华啊,你是以色列的盼望。

背弃你的人必蒙羞,

背叛你的人必像写在尘土上的名字一样消逝,

因为他们背弃了耶和华——活水的源泉。

14耶和华啊,

你医治我,我必痊愈;

你拯救我,我必脱离危难,

因为你是我所赞美的。

15人们常讥讽我说:“耶和华说的那些事在哪里?

怎么还没有实现呢?”

16但我并没有逃避牧养你子民的工作,

也没有求你降祸给他们。

你知道我说的每一句话。

17你是我患难中的避难所,

求你不要使我恐惧。

18愿你使那些迫害我的人蒙羞,

不要使我蒙羞;

愿你使他们惊慌,

不要使我惊慌。

求你使他们大祸临头,

彻底毁灭他们。

遵守安息日

19耶和华对我说:“你去站在犹大君王出入的城门前和耶路撒冷的各城门前, 20宣告,‘从这些城门进出的犹大君王、百姓以及耶路撒冷的居民啊,你们都要听耶和华的话。 21耶和华说,如果你们想保住性命,就要小心,不要在安息日带货物进耶路撒冷的城门, 22也不要从家中运出货物,不要在安息日做任何工作。要按照我对你们祖先的吩咐守安息日为圣日。 23然而,他们却不听,毫不理会,顽固不化,不肯受教。

24“‘耶和华说,你们要留心听我的话,在安息日不可运货物进耶路撒冷的城门,不可做任何工作,要守安息日为圣日。 25这样,坐大卫宝座的君王及其官员必乘车骑马和犹大人以及耶路撒冷的居民从城门出入。这城必永远有人居住。 26人们必带着燔祭、平安祭、素祭、乳香和感恩祭从犹大的城邑、耶路撒冷四周、便雅悯地区、丘陵、山区和南地去耶和华的殿。 27但如果你们不听我的话,不守安息日为圣日,仍在安息日运货物进耶路撒冷的城门,我必在各城门点起无法扑灭的大火,烧毁耶路撒冷的宫殿。’”