Yeremiya 14 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 14:1-22

Chilala, Njala, Lupanga

1Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:

2“Yuda akulira,

mizinda yake ikuvutika;

anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni,

kulira kwa Yerusalemu kwakula.

3Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi.

Apita ku zitsime

osapezako madzi.

Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi.

Amanyazi ndi othedwa nzeru

adziphimba kumaso.

4Popeza pansi pawumiratu

chifukwa kulibe madzi,

alimi ali ndi manyazi

ndipo amphimba nkhope zawo.

5Ngakhale mbawala yayikazi

ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo

chifukwa kulibe msipu.

6Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu

nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe;

maso awo achita chidima

chifukwa chosowa msipu.”

7Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa,

koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.

Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu;

ife takuchimwirani.

8Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani

ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso,

chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno?

Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?

9Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa,

kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa?

Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu,

ndipo tikudziwika ndi dzina lanu;

musatitaye ife!”

10Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi:

“Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri;

samatha kudziretsa.

Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire,

ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo

ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”

11Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino. 12Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”

13Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”

14Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo. 15Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala. 16Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.

17“Awuze mawu awa:

“ ‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza

usana ndi usiku;

chifukwa anthu anga okondedwa

apwetekeka kwambiri,

akanthidwa kwambiri.

18Ndikapita kuthengo,

ndikuona amene aphedwa ndi lupanga;

ndikapita mu mzinda,

ndikuona amene asakazidwa ndi njala.

Ngakhale aneneri pamodzi

ndi ansembe onse atengedwa.’ ”

19Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu?

Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni?

Chifukwa chiyani mwatikantha chotere

kuti sitingathenso kuchira?

Ife tinayembekezera mtendere

koma palibe chabwino chomwe chabwera,

tinayembekezera kuchira

koma panali kuopsezedwa kokhakokha.

20Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu

ndiponso kulakwa kwa makolo athu;

ndithu ife tinakuchimwiranidi.

21Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe;

musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero.

Kumbukirani pangano lanu ndi ife

ndipo musachiphwanye.

22Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina,

kodi pali mulungu amene angagwetse mvula?

Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu,

popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu

amene mukhoza kuchita zimenezi.