Yeremiya 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 13:1-27

Lamba Womanga Mʼchiwuno

1Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.” 2Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.

3Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti, 4“Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.” 5Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.

6Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.” 7Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.

8Pamenepo Yehova anandiwuza kuti, 9“Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 10Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu. 11Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.

Zikopa Zothiramo Vinyo

12“Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’ 13Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. 14Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”

Yuda Adzapita ku Ukapolo

15Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,

musadzitukumule,

pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.

16Lemekezani Yehova Mulungu wanu

asanagwetse mdima,

mapazi anu asanayambe kupunthwa

mʼchisisira chamʼmapiri.

Asanasandutse kuwala

mukuyembekezerako kukhala

mdima wandiweyani.

17Koma ngati simumvera,

ndidzalira kwambiri

chifukwa cha kunyada kwanu.

Mʼmaso mwanga

mwadzaza ndi misozi yowawa

chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.

18Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,

“Tsikani pa mipando yaufumuyo,

pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo

zagwa pansi.”

19Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa

ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula.

Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo,

watengedwa yense ukapolo.

20Tukula maso ako kuti uwone

amene akubwera kuchokera kumpoto.

Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,

nkhosa zanu zokongola zija?

21Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira

anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?

Kodi sudzamva zowawa

ngati za mayi pa nthawi yake yochira?

22Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,

“Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”

Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri

kuti zovala zanu zingʼambike

ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.

23Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,

kapena kambuku kusintha mawanga ake?

Inunso amene munazolowera kuchita

zoyipa simungathe kusintha.

24“Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu

amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.

25Limeneli ndiye gawo lanu,

chilango chimene ndakukonzerani

chifukwa chondiyiwala Ine

ndi kutumikira milungu yabodza,

akutero Yehova.

26Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso

kuti umaliseche wanu uwonekere.

27Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu

ndi ziwerewere zanu,

zochitika pa mapiri ndi mʼminda.

Tsoka iwe Yerusalemu!

Udzakhala wosayeretsedwa

pa zachipembedzo mpaka liti?”