Yeremiya 12 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 12:1-17

Madandawulo a Yeremiya

1Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse

ndikati nditsutsane nanu.

Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga.

Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino?

Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?

2Inu munawadzala ndipo anamera mizu;

amakula ndi kubereka zipatso.

Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse,

koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.

3Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa;

mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga.

Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa!

Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!

4Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti

ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti?

Nyama ndi mbalame kulibiretu

chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa.

Iwo amati:

“Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”

Yankho la Mulungu

5Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu

nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo?

Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino,

udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango

za ku Yorodani?

6Ngakhale abale ako

ndi anansi akuwukira,

onsewo amvana zokuyimba mlandu.

Usawakhulupirire,

ngakhale ayankhule zabwino ndi iwe.

7“Ine ndawasiya anthu anga;

anthu amene ndinawasankha ndawataya.

Ndapereka okondedwa anga

mʼmanja mwa adani awo.

8Anthu amene ndinawasankha

asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango.

Akundibangulira mwaukali;

nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.

9Anthu anga amene ndinawasankha

asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga

imene akabawi ayizinga.

Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo.

Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.

10Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa,

anapondereza munda wanga;

munda wanga wabwino uja

anawusandutsa chipululu.

11Unawusandutsadi chipululu.

Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine.

Dziko lonse lasanduka chipululu

chifukwa palibe wolisamalira.

12Anthu onse owononga abalalikira

ku zitunda zonse za mʼchipululu.

Yehova watuma ankhondo ake

kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko,

ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.

13Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga;

anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse.

Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu

chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”

14“Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo. 15Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake. 16Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga. 17Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.