Yeremiya 1 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 1:1-19

1Mawu a Yeremiya mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, mʼdziko la Benjamini. 2Mawuwa Yehova anayankhula naye mʼchaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya Yuda. 3Yehova anayankhulanso naye pa nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu anapita ku ukapolo.

Kuyitanidwa kwa Yeremiya

4Yehova anayankhula nane kuti,

5“Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,

iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;

ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”

6Ine ndinati, “Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono.”

7Koma Yehova anandiwuza kuti, “Usanene kuti, ‘Ndikanali wamngʼono’ popeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. 8Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.

9Pamenepo Yehova anatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga, nandiwuza kuti, “Taona, tsopano ndayika mawu anga mʼkamwa mwako. 10Lero ndakusankha kuti ukhale ndi ulamuliro pa mitundu ya anthu ndi pa maufumu awo kuti uzule ndi kugwetsa, uwononge ndi kugumula, kuti uwamange ndi kudzala.”

11Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?”

Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona nthambi ya mtengo wa mtowo.”

12Yehova anandiwuza kuti, “Waona bwino, chifukwa Ine ndikuonetsetsa kuti mawu angawa akwaniritsidwe.”

13Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti, “Kodi ukuona chiyani?”

Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona mʼphika wa madzi owira, ndipo wagudukira kuno kummwera.”

14Yehova anandiwuza kuti, “Mavuto a anthu onse okhala mʼdziko lino adzachokera kumpoto. 15Ine ndikuyitana anthu onse a ku maufumu a kumpoto,” akutero Yehova.

“Mafumu awo adzabwera ndipo aliyense adzakhazika mpando wake waufumu

polowera pa zipata za Yerusalemu;

iwo adzabwera ndi kuzungulira makoma ake

ndiponso midzi yonse ya dziko la Yuda.

16Ndidzatulutsa mlandu wanga ndi iwo

chifukwa cha zoyipa zimene anachita pondisiya Ine.

Iwo anakafukiza lubani kwa milungu ina,

ndi kupembedza zimene anapanga ndi manja awo.

17“Koma iwe Yeremiya konzeka! Nyamuka ndipo ukawawuze zonse zimene ndakulamulira. Usachite nawo mantha, kuopa kuti Ine ndingakuchititse mantha iwo akuona. 18Taona, lero ndakupanga kukhala ngati mzinda wotetezedwa, ngati mzati wachitsulo ndiponso ngati makoma a mkuwa kuti usaopsedwe ndi munthu aliyense wa mʼdzikomo; kaya ndi mafumu a Yuda, akuluakulu ake, ansembe ake, kapena munthu wamba wa mʼdzikomo. 19Iwo adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, popeza Ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.