Tito 2 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tito 2:1-15

Malangizo Osiyanasiyana

1Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. 2Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.

3Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. 4Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. 5Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.

6Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa. 7Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako. 8Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.

9Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo 10kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu.

11Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. 12Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, 13pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu, 14amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.

15Tsono zimenezi ndi zinthu zomwe uyenera kuphunzitsa. Uziwalimbikitsa anthu ndi kuwatsutsa komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ayi.

Slovo na cestu

Titovi 2:1-15

Pro každého vhodný pokyn

1Veď své posluchače k tomu, co odpovídá zdravému učení: 2starší muži ať jsou střídmí a vážní, zdraví ve víře, lásce a trpělivosti. 3Podobně starší ženy ať se chovají důstojně, nepomlouvají a neholdují alkoholu. Mladším ženám mají být vychovatelkami k dobrému, 4aby milovaly své muže a děti, 5ovládaly své nálady, pečovaly o čistotu těla i duše, pořádně vedly domácnost, byly laskavé a povolné k manželům, aby nezavdaly příčinu ke kritice křesťanské víry.

6Také mladé muže veď k sebeovládání. 7Buď jim vzorem správného jednání po všech stránkách. 8Všechno, čemu učíš, ať je výstižné a odpovídá pravdě, aby protivník neměl co namítnout.

9Podřízení ať poslouchají své představené, ať jsou úslužní, neodmlouvají, 10nepodvádějí a ve všem ať je na ně naprosté spolehnutí. Tak budou vzbuzovat zájem o víru v našeho Zachránce, Boha. 11On ukázal, že miluje všechny lidi a chce je zachránit. 12To nás vede k tomu, abychom se zřekli bezbožnosti a tělesných choutek a žili své dny moudře, spravedlivě a v úctě před Bohem. 13Před námi přece leží věčná radost; vždyť očekáváme, že se ukáže ve své slávě náš veliký Bůh a Zachránce, Ježíš Kristus. 14On se za nás obětoval, abychom už nepodléhali moci hříchu a stali se jeho lidem, nadšeným pro vše dobré.

15Tak lidi uč, naléhavě přesvědčuj a napravuj, kde bude třeba. Nikdo ať tě nebere na lehkou váhu.