Oweruza 9 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 9:1-57

Abimeleki

1Abimeleki mwana wa Yeru-Baala anapita ku Sekemu kwa abale a amayi ake ndi kukawawuza iwowo ndi fuko lonse la banja la abambo a amayi ake kuti, 2“Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno, ‘Chabwino ndi chiyani kwa inu kuti ana onse makumi asanu ndi awiri a Yeru-Baala azikulamulirani, kapena kuti azikulamulirani ndi munthu mmodzi basi?’ Kumbukirani kuti ine ndine mʼbale wanu weniweni.”

3Abale a amayi akewo anamuyankhulira mawu amenewa kwa nzika zonse za ku Sekemu, ndipo mitima ya anthu onse inali pa Abimeleki chifukwa anati, “Uyu ndi mʼbale wathu,” 4Tsono anamupatsa ndalama zasiliva 70 za mʼnyumba ya chipembedzo ya Baala Beriti. Ndi ndalama zimenezi Abimeleki analemba anthu achabechabe ndi osasamala kuti azimutsatira. 5Anapita ku Ofiri ku mudzi kwa abambo ake ndipo anapha abale ake makumi asanu ndi awiri, ana a Yeru-Baala pa mwala umodzi. Koma Yotamu yemwe anali wamngʼono mwa onsewo anapulumuka chifukwa anabisala. 6Tsono nzika za ku Sekemu ndi za ku Beti-Milo zinapita kukasonkhana ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala cha ku Sekemu kuti akalonge Abimeleki ufumu.

7Yotamu atamva izi anapita kukayima pamwamba pa phiri la Gerizimu ndipo anafuwula nati, “Tandimverani inu anthu a ku Sekemu, kuti Mulungu akumvereninso. 8Tsiku lina mitengo inapita kukadzoza mfumu yawo. Tsono mitengoyo inati kwa mtengo wa olivi, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’ ”

9“Koma mtengo wa olivi uja unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye mafuta angawa amene amalemekezera nawo milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo?’ ”

10Apo mitengo inawuza mtengo wa mkuyu kuti, “Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.”

11Koma mtengo wa mkuyu unayankha kuti, “Kodi ndisiye chipatso changa chokoma ndi chozunachi kuti ndizikalamulira mitengo?”

12Kenaka mitengo ija inawuza mtengo wamphesa kuti, “Bwera ndiwe kuti ukhale mfumu yathu.”

13Koma mtengo wamphesa unayankha kuti, “Kodi ine ndisiye vinyo wangayu, amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe kuti ndizikalamulira mitengo?”

14Pomaliza mitengo yonse inawuza mkandankhuku kuti, “Bwera ndipo ukhale mfumu yathu.”

15Mkandankhuku uja unayankha kuti, “Ngati mukufunadi kuti mudzoze ine kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mu mthunzi mwangamu, koma ngati simutero, moto utuluka kwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.”

16Yotamu anatinso, “Kodi mukuti munaonetsadi kuona mtima ndi kukhulupirika podzoza Abimeleki kukhala mfumu? Kodi mukuti munachitira ulemu Yeru-Baala ndi banja lake poganizira ntchito zimene anachita? 17Kodi suja abambo anga anakumenyerani nkhondo ndi kuyika moyo wawo pa chiswe kuti akupulumutseni mʼmanja mwa Amidiyani? 18Koma lero inu mwawukira banja la abambo anga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndiponso mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mdzakazi wake kuti akhale wolamulira anthu a ku Sekemu chifukwa ndi mʼbale wanu. 19Tsono ngati mukuti zimene mwachitira Yeru-Baala ndi banja lake mwazichita moona mtima ndiponso mokhulupirika, ndiye mukondwere ndi Abimeleki, nayenso akondwere nanu! 20Koma ngati sichoncho moto utuluke mwa Abimeleki ndi kupsereza anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndipo moto utulukenso mwa anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndi kupsereza Abimeleki!”

21Kenaka Yotamu anathawira ku Beeri nakakhala komweko chifukwa ankaopa Abimeleki mʼbale wake.

22Abimeleki atalamulira Israeli zaka zitatu, 23Mulungu anayika chidani pakati pa Abimelekiyo ndi anthu a ku Sekemu, motero kuti anthu a ku Sekemu anawukira Abimeleki. 24Mulungu anachita zimenezi kuti zoyipa zimene anachitira ana aamuna 70 a Yeru-Baala aja zimubwerere, ndi kuti magazi awo akhale pa Abimeleki mʼbale wawo ndi pa anthu a ku Sekemu amene anamulimbikitsa mtima kuti aphe abale akewo. 25Choncho anthu a ku Sekemu anayika anthu omubisalira pamwamba pa mapiri. Tsono iwo ankalanda anthu odutsa mʼnjira imeneyo zinthu zawo ndipo Abimeleki anamva zimenezi.

26Gaali mwana wa Ebedi anasamukira ku Sekemu ndi abale ake, ndipo anthu a ku Sekemuko anamukhulupirira iye. 27Anthuwo anapita ku munda kukathyola mphesa ndi kuzifinya, ndipo anachita chikondwerero mʼnyumba ya milungu yawo. Anthuwo akudya ndi kumwa, ankatemberera Abimeleki. 28Ndipo Gaali mwana wa Ebedi anati “Kodi Abimeleki ndi ndani, ndipo nʼchifukwa chiyani akutilamulira ife Asekemu? Kodi iyeyu si mwana wa Yeru-Baala ndipo womuthandiza wake si Zebuli? Tiyeni titumikire anthu a ku Hamori, kholo la fuko la Sekemu! Nanga nʼchifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? 29Anthu a mu mzindawo akanakhala pansi pa ulamuliro wanga, ndikanamuchotsa Abimelekiyu. Ndikanamuwuza Abimeleki kuti, ‘Wonjeza ankhondo ako ndipo ubwere tidzamenyane!’ ”

30Zebuli amene ankalamulira mzindawo atamva zimene Gaali mwana wa Ebadi ananena, anakwiya kwambiri. 31Anatumiza amithenga kwa Abimeleki, kukanena kuti, “Gaali mwana wa Ebedi ndi abale ake abwera ku Sekemu ndipo akuwutsa mitima ya anthu a mu mzindawo kuti akuwukireni inu. 32Nʼchifukwa chake usiku womwe uno inu ndi anthu anu mupite, mukabisale mʼminda. 33Mmawa dzuwa likutuluka, mudzuke ndi kukathira nkhondo mzindawo. Gaali ndi anthu amene ali naye akamadzabwera kuti alimbane ndi inu, inu mudzathane nawo monga mmene mungachitire.”

34Choncho Abimeleki ndi ankhondo ake onse anadzuka usiku nakabisalira mzinda wa Sekemu mʼmagulu anayi. 35Gaali mwana wa Ebedi anatuluka nakayima pa khomo pa chipata cha mzinda pamene Abimeleki ndi ankhondo ake anatuluka ku malo kumene anabisala kuja.

36Gaaliyo atawaona, anawuza Zebuli kuti, “Taona anthu akutsika kuchoka pamwamba pa mapiri.”

Koma Zebuli anayankha kuti, “Zimene mukuonazo ndi zithunzi za mapiri chabe osati anthu.”

37Koma Gaaliyo anayankhulanso kuti, “Taona anthu akutsika kuchokera pakati pa phiri, ndipo gulu lina likubwera kuchokera ku mtengo wa thundu wa owombeza mawula.”

38Ndipo Zebuli anamufunsa iye kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iwe amene umanena kuti, Abimeleki ndaninso kuti ife timutumikire? Kodi amenewa si anthu aja umawanyozawa? Tsopano tuluka ukamenyane nawo.”

39Choncho Gaaliyo anatuluka akutsogolera anthu a ku Sekemu kukamenyana ndi Abimeleki. 40Koma Abimeleki anamuthamangitsa ndipo Gaala anathawa. Ambiri a ankhondo ake anagwa napwetekeka njira yonse mpaka ku chipata cha mzinda. 41Abimeleki anakhala ku Aruma, ndipo Zebuli anathamangitsa Gaali pamodzi ndi abale ake, kuwatulutsa mu Sekemu.

42Mmawa mwake anthu a ku Sekemu anapangana zopita ku minda, ndipo Abimeleki anamva zimenezi. 43Tsono Abimeleki anatenga anthu ake, nawagawa magulu atatu ndi kukabisala mʼminda. Ataona anthu akutuluka mu mzindawo, iye anapita kukalimbana nawo ndipo onsewo anawapha. 44Abimeleki pamodzi ndi magulu ake anathamangira kutsogolo nakawakhalira pa chipata cha mzinda. Ndipo magulu awiri ena aja anathamangira anthu amene anali mʼminda ndi kuwapha onse. 45Abimeleki anawuthira nkhondo mzindawo tsiku lonse. Kenaka anawulanda ndi kupha nzika zonse za mu mzindamo. Anawuwonongeratu mzindawo nawuwaza mchere.

46Anthu a mu nsanja ya Sekemu atamva zimenezi, anakalowa mu linga la nyumba yopembedzeramo Baala-Beriti. 47Abimeleki anamva kuti anthu ena asonkhana kumeneko. 48Choncho Abimeleki pamodzi ndi anthu ake onse anapita ku phiri la Zalimoni. Kumeneko anatenga nkhwangwa nadula nthambi za mitengo. Ananyamula nthambi zija pa phewa pake. Tsono anawuza anthu aja kuti, “Zimene mwaona ine ndikuchita, inunso mufulumire kuchita monga ndachitiramu.” 49Tsono aliyense anadula nthambi zake, natsatira Abimeleki. Anakawunjika nthambi zija pa linga paja, kenaka ndi kuliyatsa moto. Choncho anthu onse a ku nsanja ya Sekemu anafa. Analipo anthu pafupifupi 1,000, amuna ndi akazi.

50Kenaka Abimeleki anapita ku Tebezi. Anakawuzungulira mzindawo ndi kuwulanda. 51Koma mu mzindamo munali nsanja yolimba. Anthu onse a mu mzindamo amuna ndi akazi anathawira mu nsanjayo, nadzitsekera mʼkati. Ndipo anakwera ku denga la nsanjayo. 52Abimeleki anapita ku nsanjayo nathira nkhondo. Anafika pafupi ndi chitseko cha nsanja ija kuti ayitenthe. 53Koma mkazi wina anaponya mwala wa mphero pa mutu wa Abimeleki ndi kuswa chibade cha mutuwo.

54Mwamsanga Abimeleki anayitana mnyamata womunyamulira zida za nkhondo namuwuza kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuti anthu asadzanene kuti, ‘Mkazi ndiye anamupha.’ ” Choncho wantchito wake anamubayadi mpaka kutulukira kunja lupangalo ndipo anafa. 55Aisraeli ataona kuti Abimeleki wafa, anapita kwawo.

56Mmenemu ndi mmene Mulungu analipsirira tchimo la Abimeleki limene anachitira abambo ake pakupha abale ake 70 aja. 57Mulungu anawalanganso anthu a ku Sekemu chifukwa cha kuyipa kwawo konse. Ndipo matemberero a Yotamu mwana wa Yeru-Baala anawagweradi.