Oweruza 6 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 6:1-40

Gideoni

1Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 2Amidiyani anapondereza Aisraeli. Tsono chifukwa cha Amidiyaniwa, Aisraeli anakonza malo obisalamo mʼmapiri ndi mʼmapanga. Anamanganso malinga. 3Aisraeli amati akadzala mbewu, Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena akummawa amabwera ndi kudzawathira nkhondo. 4Iwo anamanga misasa mʼdzikomo ndi kuwononga zokolola zawo zonse mpaka ku Gaza, ndipo sanawasiyireko chamoyo chilichonse Aisraeliwo, kaya nkhosa kapena ngʼombe ndi bulu yemwe. 5Iwo ankabwera ndi zoweta zawo ndi matenti awo omwe. Ankabwera ambiri ngati dzombe, motero kuti kunali kovuta kuwawerenga anthuwo ndi ngamira zawo. Tsono iwo ankabwera ndi kuwononga dziko lonse. 6Aisraeli anasauka chifukwa cha Amidiyani ndipo analirira kwa Yehova kuti awathandize.

7Pamene Aisraeli analirira kwa Yehova chifukwa cha Amidiyaniwo, 8Iye anawatumizira mneneri amene anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndine amene ndinakutsogolerani kuchokera ku Igupto. Ndinakutulutsani mʼdziko la ukapolo. 9Ine ndinakupulumutsani ku ulamuliro wa Igupto komanso mʼmanja mwa amene amakuzunzani. Ndinawathamangitsa adani anu inu mukufika, ndikukupatsani dziko lawo.’ 10Ndipo ndinakuwuzani kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musapembedze Milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.’ Koma inu simunandimvere.”

11Tsiku lina mngelo wa Yehova anabwera ku Ofura ndi kukhala pansi pa tsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yowasi Mwabiezeri. Tsono Gideoni, mwana wake nʼkuti pa nthawiyo akupuntha tirigu mʼmalo ofinyira mphesa mowabisalira Amidiyani. 12Tsono mngelo wa Yehova uja anamuonekera Gideoni nati kwa iye, “Yehova ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”

13Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.”

14Yehova anamuyangʼana namuwuza kuti, “Pita ndi mphamvu zomwe uli nazo, ukapulumutse Aisraeli mʼmanja mwa Amidiyani. Kodi si ndine amene ndakutuma?”

15Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.”

16Yehova anamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo Amidiyaniwo udzawagonjetsa ngati munthu mmodzi.”

17Gideoni anati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, ndionetseni chizindikiro kusonyeza kuti ndinudi mukuyankhula ndi ine. 18Chonde musachoke msanga mpaka nditabwerera kwa inu ndi chopereka changa cha chakudya kudzachipereka kwa inu.”

Ndipo Yehova anamuwuza kuti, “Ine ndikudikira mpaka utabweranso.”

19Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja.

20Mngelo wa Mulungu anamuwuza iye kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekewa, uziyike pa mwala uwu ndi kuthirapo msuziwu.” Ndipo Gideoni anatero. 21Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso. 22Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!”

23Koma Yehova anamuwuza kuti, “Mtendere ukhale ndi iwe! Usachite mantha, sufa ayi.”

24Choncho Gideoni anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo analitcha kuti, Yehova ndiye mtendere. Kufikira lero lino guwali lilipo ku Ofura wa Mwabiezeri.

25Usiku womwewo Yehova anati kwa Gideoni, “Tenga ngʼombe ya mphongo ya abambo ako, ngʼombe ina yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ugwetse guwa la Baala limene abambo ako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pafupi pake. 26Kenaka umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe ndi miyala yoyala bwino pamwamba pa chiwunda chimenecho. Utenge ngʼombe ya mphongo yachiwiri ija ndipo uyipereke ngati nsembe yopsereza pogwiritsa ntchito mitengo ya fano la Asera imene udule ngati nkhunizo.”

27Choncho Gideoni anatenga antchito ake khumi nachita monga Yehova anamuwuzira. Ndipo popeza ankaopa anthu a pa banja lake ndiponso anthu a mʼmudzimo sanachite zimenezi masana koma usiku.

28Anthu a mu mzindamo atadzuka mʼmamawa anangoona guwa la Baala litagwetsedwa ndi fano la Asera limene linali pamwamba pake litadulidwa ndiponso ngʼombe yamphongo yachiwiri ija itaperekedwa ngati nsembe yopsereza pa guwa limene linamangidwa lija.

29Iwo anafunsana wina ndi mnzake, “Wachita zimenezi ndani?”

Atafufuza ndi kufunsafunsa, analingalira kuti, “Gideoni mwana wa Yowasi ndiye wachita zimenezi.”

30Ndipo anthuwo anawuza Yowasi kuti, “Tulutsa mwana wako, ayenera kufa chifukwa wagumula guwa lansembe la Baala ndipo wadula fano la Asera lomwe linali pamwamba pake.”

31Koma Yowasi anawuza anthu amene anamuzungulirawo kuti, “Kodi inu mukuti mukhale woyankhulira Baala mlandu? Kodi ndinu amene mukuti mumupulumutse? Amene akufuna kumumenyera nkhondo Baala akhala atafa pofika mmawa! Ngati Baalayo ndi mulungudi, musiyeni adzimenyere yekha nkhondo popeza munthu wina wamugwetsera guwa lansembe lake.” 32Choncho tsiku limenelo Gideoni anatchedwa, Yeru-Baala, kutanthauza kuti, “Baala alimbana naye, popeza anagwetsa guwa lake la nsembe.”

33Tsopano Amidiyani, Amaleki ndi anthu ena akummawa anasonkhana ndipo atawoloka Yorodani anakamanga zinthando za nkhondo ku chigwa cha Yezireeli. 34Ndipo Mzimu wa Yehova unatsikira pa Gideoni, ndipo anayimba lipenga kuyitana Abiezeri kuti amutsatire iye. 35Iye anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Manase kuti akamenye nkhondo ndipo Amanase anayitanidwanso kuti amutsate. Anatumanso amithenga kwa Aseri, Azebuloni ndi Anafutali, ndipo onsewo anapita kukakumana naye.

36Gideoni anati kwa Mulungu, “Ngati mudzapulumutsa Israeli ndi dzanja langa monga mwalonjezeramu, 37onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera.” 38Ndipo zimenezi zinachitikadi. Gideoni atadzuka mʼmamawa ndi kuwufinya ubweya uja, anafinya madzi odzaza mtsuko.

39Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.” 40Ndipo Mulungu anachita zomwezo usiku umenewo. Pa ubweya pokha panali powuma, koma pa nthaka ponse panagwa mame.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

士師記 6:1-40

士師基甸

1後來,以色列人又做耶和華視為惡的事,耶和華就把他們交在米甸人手中,受他們統治七年。 2米甸人勢力強盛,以色列人只好躲進山裡,藏在洞穴和營寨中。 3每當他們撒種的時候,米甸人、亞瑪力人及東方人就前來進犯, 4在他們境內安營,摧毀他們遠至迦薩一帶的莊稼,不給他們留下任何糧食,也不留下一隻羊、一頭牛或驢。 5入侵者帶著牲畜和帳篷像蝗蟲一樣湧來,人和駱駝不計其數,摧毀了整個地區。 6以色列人因米甸人的入侵而極其貧乏,就呼求耶和華。

7以色列人因米甸人的入侵而呼求耶和華的時候, 8耶和華就差遣先知對他們說:「以色列的上帝耶和華說,『我曾把你們從受奴役之地——埃及領出來, 9將你們從埃及人及一切欺壓者的手中拯救出來,為你們趕走敵人,把他們的土地賜給你們。』 10我曾對你們說,『我是你們的上帝耶和華。你們雖然住在亞摩利人的地方,但不可祭拜他們的神明。』你們卻充耳不聞。」

11一天,耶和華的天使來到俄弗拉,坐在亞比以謝族人約阿施的橡樹下。約阿施的兒子基甸因為要躲避米甸人,正躲在榨酒池裡打麥子。 12耶和華的天使向基甸顯現,說:「英勇的戰士啊,耶和華與你同在。」 13基甸說:「我主啊,如果耶和華與我們同在,我們怎會有這些遭遇?我們的祖先曾告訴我們有關耶和華帶領他們離開埃及的事,如今祂那些奇妙的作為在哪裡呢?現在祂已經丟棄我們,把我們交在米甸人手裡。」 14耶和華轉向他,說:「你盡自己的力量去從米甸人手中拯救以色列人吧,我現在派你去。」 15基甸說:「主啊,我出身於瑪拿西支派最貧窮的家族,在家裡最微不足道,我怎能拯救以色列人呢?」 16耶和華說:「我必與你同在,你必如擊打一人一樣擊打米甸人。」 17基甸說:「如果我在你面前蒙恩,求你給我一個憑據,使我知道與我說話的真是你耶和華。 18請你在這裡等一等,讓我回去拿禮物獻給你。」耶和華說:「我必等你回來。」

19基甸回家預備了一隻山羊羔,用十公斤麵粉做了無酵餅,把肉放進籃子,把湯盛在壺中,然後拿到橡樹下獻給耶和華的天使。 20上帝的天使對基甸說:「把肉和無酵餅放在這磐石上,把湯倒在上面。」他一一照做。 21耶和華的天使伸出手中的杖碰了一下餅和肉,火就從磐石中噴出來燒盡了它們。耶和華的天使也不見了。 22基甸發現他果然是耶和華的天使,便說:「唉!主耶和華啊,不好了,我面對面見了你的天使。」 23耶和華對他說:「放心吧,不用害怕,你不會死。」 24基甸在那裡為耶和華築了一座壇,稱之為「耶和華賜平安」。這壇如今仍在亞比以謝族的俄弗拉

25那天晚上,耶和華吩咐基甸:「牽來你父親的第二頭牛,就是那頭七歲的牛,拆毀你父親為巴力築的祭壇,砍倒壇旁的亞舍拉神像。 26然後,在這座山頂上把石頭堆放整齊,為你的上帝耶和華築一座祭壇,用砍倒的亞舍拉神像作柴,把那頭牛獻作燔祭。」 27於是,基甸帶了十個僕人遵命而行。不過,他因為害怕家人和城中的人,不敢在白天行動,便在夜間行動。

28第二天清早,城裡的人發現巴力的祭壇已經被人拆毀,壇旁的亞舍拉神像被砍倒,第二頭公牛被獻在新建的祭壇上。 29他們彼此議論說:「這是誰幹的?」他們仔細調查後得知是約阿施的兒子基甸所為, 30便對約阿施說:「把你兒子交出來!他拆毀了巴力的祭壇,砍倒了壇旁的亞舍拉神像,我們要處死他!」 31約阿施對氣勢洶洶的人群說:「你們這樣做是要為巴力辯護嗎?是要救它嗎?誰為巴力辯護,今天早晨就處死誰。有人拆毀巴力的祭壇,如果它是神明,就讓它為自己辯護吧!」 32因此,那天他們稱基甸耶路·巴力,意思是「讓巴力為自己辯護」,因為他拆毀了巴力的祭壇。

33那時,米甸人、亞瑪力人及東方人一起過了約旦河,在耶斯列的平原安營。 34耶和華的靈降在基甸身上,他就吹起號角,號召亞比以謝族的人跟從他。 35他派人走遍瑪拿西亞設西布倫拿弗他利各支派召集軍隊,得到了人們的回應。 36基甸對上帝說:「若如你所言,你要用我去拯救以色列人, 37求你給個憑據。我把一團羊毛放在麥場上,若明天早晨只是羊毛上有露水,地面卻是乾的,我就知道,如你所言,你要用我去拯救以色列人。」 38果然如此,基甸一早醒來,從羊毛中擠出滿滿一碗露水。 39基甸又對上帝說:「求你不要發怒,容許我再試一次,這次讓羊毛是乾的,地面有露水。」 40那天晚上,耶和華就照他所求使地面佈滿露水,唯獨羊毛是乾的。