Oweruza 5 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 5:1-31

Nyimbo ya Debora

1“Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi:

2“Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli;

ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu,

tamandani Yehova:

3“Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu!

Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova,

Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma.

4“Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri,

pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu,

dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka

nigwetsa madzi.

5Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,

Mulungu wa Israeli.

6“Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati,

pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa;

alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali.

7Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi

mpaka pamene iwe Debora unafika;

unafika ngati mayi ku Israeli.

8Pamene anasankha milungu ina,

nkhondo inabwera ku zipata za mzinda,

ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke

pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.

9Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli,

uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu.

Tamandani Yehova!

10“Inu okwera pa abulu oyera,

okhala pa zishalo,

ndi inu oyenda pa msewu,

yankhulani. 11Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta;

kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana;

akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli.

“Choncho anthu a Yehova

anasonkhana ku zipata za mzinda.

12Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera;

tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo.

Iwe Baraki! nyamuka

Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’

13“Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo;

anthu a Yehova anapita

kukamenyera Yehova nkhondo

kulimbana ndi adani amphamvu.

14Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu;

akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako.

Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri,

ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.

15Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora;

inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki,

ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira.

Koma pakati pa mafuko a Rubeni

panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.

16Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera

zitoliro zoyitanira nkhosa?

Pakati pa anthu a fuko la Rubeni

panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.

17Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani.

Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi?

Aseri anali pa gombe la Nyanja;

anangokhala mʼmadooko mwawo.

18Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa.

Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.

19“Mafumu anabwera, anachita nkhondo;

mafumu Akanaani anachita nkhondo

ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido,

koma sanatengeko zofunkha zasiliva.

20Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo,

zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.

21Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,

chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola.

Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!

22Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu,

akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.

23Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’

‘Tembererani nzika zake mwaukali,

chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova,

kulimbana ndi adani ake amphamvu.’

24“Akhale wodala kupambana akazi onse,

Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni;

inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu.

25Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka;

anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka.

26Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake,

anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja.

Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake,

ndi kumubowola mu litsipa mwake.

27Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa,

anagwa; iye anagona pamenepo.

Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa;

pamene anagwera, pamenepo anaferapo.

28“Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera;

nafuwula mokweza kuti,

‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika?

Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’

29Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha,

ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti,

30‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane;

akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri.

Sisera akumupatsa zofunkha:

zovala zonyikidwa mu utoto,

zoti ndizivala mʼkhosi

zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’

31“Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke,

koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa

pamene lituluka ndi mphamvu zake.”

Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.