Oweruza 4 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 4:1-24

Debora

1Ehudi atamwalira, Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. 2Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu. 3Aisraeli analira kwa Yehova kuti awathandize, chifukwa Sisera anali ndi magaleta achitsulo 900 ndipo anazunza Aisraeli mwankhanza kwa zaka makumi awiri.

4Debora, mneneri wamkazi, mkazi wake wa Rapidoti ndiye ankatsogolera Israeli nthawi imeneyo. 5Iye ankakhala pansi pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Beteli mʼdziko la ku mapiri la Efereimu, ndipo Aisraeli ankapita kwa iye kuti akaweruze milandu yawo. 6Debora uja anatuma munthu kuti akayitane Baraki mwana wa Abinoamu wa ku Kedesi mʼdziko la Nafutali ndipo anati kwa iye, “Yehova Mulungu wa Israeli akukulamula iwe kuti, ‘Pita kasonkhanitse anthu ku phiri la Tabori. Ubwere nawo anthu 10,000 a fuko la Nafutali ndi a fuko la Zebuloni. 7Ine ndidzakokera Sisera mkulu wa ankhondo a Yabini pamodzi ndi magaleta ake ndi asilikali ake kwa inu ku mtsinje wa Kisoni ndipo ndidzamupereka mʼmanja mwanu.’ ”

8Baraki anamuyankha kuti, “Mukapita nane limodzi ine ndipita. Koma ngati sitipitira limodzi, inenso sindipita.”

9Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. 10Baraki anayitana mafuko a Zebuloni ndi Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu 10,000 anamutsatira, ndipo Debora anapita naye pamodzi.

11Nthawi imeneyo nʼkuti Mkeni wina dzina lake Heberi atalekana ndi Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, nakamanga tenti yake pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu pafupi ndi Kedesi.

12Pamene Sisera anamva kuti Baraki mwana wa Abinoamu wapita ku phiri la Tabori, 13anasonkhanitsa magaleta ake achitsulo 900 ndi anthu onse amene anali naye ndipo anachoka ku Haroseti-Hagoyimu kupita ku mtsinje wa Kisoni.

14Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata. 15Yehova anasokoneza Sisera ndi magaleta ake pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi anthu ake anawapirikitsa ndipo Sisera anatsika pa galeta yake nayamba kuthawa pansi. 16Baraki analondola magaletawo pamodzi ndi ankhondo onse mpaka ku Haroseti-Hagoyimu, ndipo ankhondo onse a Sisera anaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe anatsala.

17Komabe Sisera anathawa pansi mpaka anakafika ku tenti ya Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni uja, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori ndi banja la Heberi, Mkeni uja.

18Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndipo anati, “Bwerani mbuye wanga, lowani momwemo musaope.” Choncho analowa mʼtenti muja, ndipo anamufunditsa chofunda.

19Anati, “Ndili ndi ludzu, chonde patseniko madzi pangʼono akumwa, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo anatsekula thumba la chikopa mmene munali mkaka, namupatsa kuti amwe, ndipo anamufunditsanso.

20Kenaka anawuza mkaziyo kuti, “Muyime pa khomo la tentili, ndipo munthu wina akabwera kudzakufunsani kuti, ‘Kodi kwafika munthu wina kuno?’ Inu muyankha kuti, ‘Ayi.’ ”

21Koma Yaeli mkazi wa Heberi, anatenga chikhomo cha tenti ndi hamara ndi kupita mwakachetechete kwa Sisera uja. Tsono Sisera ali mtulo chifukwa chotopa, mkazi uja anamukhomera chikhomo chija mʼmutu mwake. Chinatulukira kwinaku mpaka kulowa mʼnthaka, ndipo anafa pomwepo.

22Baraki atafika akulondola Sisera, Yaeli anatuluka kukamuchingamira namuwuza kuti, “Lowani mudzaone munthu amene mukumufunafuna.” Tsono atalowa anangoona Sisera ali thapsa pansi wakufa ndi chikhomo chili mʼmutu mwake.

23“Choncho pa tsiku limenelo Mulungu anagonjetsa Yabini mfumu ya Akanaani, pamaso pa Aisraeli. 24Ndipo Aisraeli anapanikizabe Yabini, mfumu ya Akanaani, mpaka kumuwonongeratu.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

士師記 4:1-24

士師底波拉

1以笏死後,以色列人又做耶和華視為惡的事。 2耶和華把他們交在統治夏瑣迦南耶賓手中。耶賓王的將軍叫西西拉,住在夏羅設3耶賓王擁有九百輛鐵戰車,他殘暴地壓迫以色列人二十年。以色列人向耶和華呼求。

4當時做士師的是一位名叫底波拉的女先知,她是拉比多的妻子, 5經常坐在以法蓮山區拉瑪伯特利之間的底波拉棕樹下,審理以色列人的事情。 6她派人去拿弗他利基低斯召來亞比挪庵的兒子巴拉,對他說:「以色列的上帝耶和華命你率領一萬拿弗他利人和西布倫人上他泊山。 7祂必使耶賓的將軍西西拉率領全軍和戰車到基順河與你交戰,祂必把西西拉交在你手中。」 8巴拉回答說:「你跟我去,我就去;你不跟我去,我就不去。」 9底波拉說:「好,我一定與你同去。不過,你這次出征一定得不到榮耀,因為耶和華要把西西拉交在一名婦人手上。」於是,他們一同前往基低斯10巴拉招聚了一萬名拿弗他利人和西布倫人,底波拉與他一起出征。

11摩西的岳父何巴的後人基尼希百離開自己的族人,在基低斯附近撒拿音的橡樹旁搭帳篷居住。

12西西拉得知亞比挪庵的兒子巴拉已經上了他泊山, 13便召集全軍和九百輛鐵戰車離開夏羅設,向基順河進軍。 14底波拉巴拉說:「出擊吧!今天耶和華要把西西拉交在你手中。看啊,耶和華已經率先出戰了!」於是,巴拉率領一萬人下了他泊山, 15進攻西西拉。耶和華使西西拉的戰車和軍隊驚慌失措,敗在巴拉刀下。西西拉棄車徒步逃跑, 16巴拉追擊他的戰車和軍隊,直到夏羅設西西拉全軍都死於刀下,無一倖免。

17只有西西拉一人徒步逃到基尼希百的妻子雅億的帳篷,因為耶賓王和希百家向來友好。 18雅億出來迎接西西拉,對他說:「我主,請進,不用怕!」西西拉便走進帳篷,雅億為他蓋上毯子。 19西西拉說:「我口渴,請給我一點水吧。」雅億打開皮袋給他奶喝,然後又給他蓋上毯子。 20西西拉又說:「請你守著門口,倘若有人查問,你就說沒人來過這裡。」 21西西拉因疲勞過度,沉沉入睡。雅億乘機拿起錘子和一根帳篷的橛子,悄悄地走到他身旁,把橛子釘進他的太陽穴,直插到地裡。西西拉就這樣死了。 22巴拉追來了,雅億出來迎接他,對他說:「你找的人在這裡,進來看看吧。」巴拉和她進了帳篷,見西西拉死在那裡,太陽穴上還插著橛子。

23那天,上帝使以色列人戰勝了迦南耶賓24以色列人越戰越勇,最終消滅了耶賓王。