Oweruza 3 – CCL & BDS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 3:1-31

1Iyi ndi mitundu ya anthu yomwe Yehova anayisiya kuti ayese nayo Aisraeli amene sanadziwe kumenya nkhondo mu Kanaani 2(Yehova anachita izi kuti Aisraeli onse aphunzire kumenya nkhondo; makamaka amene nʼkale lonse sanadziwe kumenya nkhondo. 3Mitundu ya anthuyo ndi: Mafumu asanu a Afilisti, Akanaani onse, Asidoni, ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni kuyambira ku phiri la Baala-Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. 4Iwowa Yehova anawasiya kuti aziyesa nawo Aisraeli kuti aone ngati angamvere malamulo a Yehova, amene anapatsa makolo awo kudzera mwa Mose.

5Choncho Aisraeli anakhala pakati pa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 6Tsono Aisraeli aja amalola ana awo aamuna ndi aakazi kuti azikwatira ndi kukwatiwa ndi anthu amitundu ina. Kenaka anayamba kupembedza milungu yawo.

Otanieli

7Aisraeli anachita zinthu zoyipira Yehova. Iwowa anayiwala Yehova Mulungu wawo ndi kumatumikira Abaala ndi Asera. 8Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu. 9Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa. 10Mzimu wa Yehova unatsika pa iye, choncho anasanduka mtsogoleri wa Israeli. Iye anapita kukamenya nkhondo, ndipo Yehova anapereka Kusani-Risataimu mfumu ya Aaramu mʼmanja mwake. Choncho anayigonjetsa. 11Ndipo mʼdzikomo munakhala mtendere zaka makumi anayi. Kenaka Otanieli mwana wa Kenazi anamwalira.

Ehudi

12Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Tsono Yehova anapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya Mowabu kuti alimbane ndi Aisraeli aja popeza anachita zinthu zoyipira Yehova. 13Egiloniyo anamemeza Aamori ndi Aamaleki kupita kukamenyana ndi Israeli, ndipo analanda Yeriko, mzinda wa migwalangwa. 14Aisraeli anatumikira ngati akapolo Egiloni mfumu ya Mowabu kwa zaka 18.

15Aisraeli analiranso kwa Yehova, ndipo Iye anawawutsira mpulumutsi, Ehudi. Iyeyu anali mwana wa Gera, munthu wamanzere, wa fuko la Benjamini. Aisraeli ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, kudzera kwa Ehudi. 16Ndipo Ehudi anapanga lupanga lakuthwa kuwiri lotalika masentimita makumi asanu, ndipo anamangirira lupangalo pa ntchafu yake ya kumanja mʼkati mwa zovala zake. 17Iye anakapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, amene anali munthu wonenepa kwambiri. 18Ehudi atapereka msonkhowo, anawuza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. 19Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.”

Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa.

20Kenaka Ehudi anayandikira pafupi ndi mfumuyo, ndipo iyo inakhala yokha mʼchipinda chapamwamba, mozizira bwino. Tsono Ehudi anati, “Ndili ndi mawu ochokera kwa Mulungu woti ndikuwuzeni.” Mfumuyo itadzuka pa mpando wake waufumu, 21Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, anasolola lupanga pa ntchafu yake ya kumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba. 22Lupanga linalowa mʼmimba pamodzi ndi chogwirira chake. Mafuta anaphimba lupangalo popeza silinatulutsidwe mʼmimbamo. Ndiponso matumbo anatuluka. 23Kenaka Ehudi anatuluka panja pa khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda chapamwambacho.

24Ehudi atachoka, atumiki a mfumu aja anabwera, ndipo ataona kuti zitseko za chipinda chapamwamba zinali zokhoma anaganiza kuti mwina mfumu ikudzithandiza mʼkatimo. 25Iwo anadikira nthawi yayitali koma popanda chochitika. Koma ataona kuti mfumuyo sikutsekulabe zitseko za chipindacho, iwo anatenga makiyi ndi kutsekula zitsekozo, ndipo anangoona mbuye wawo atagwera pansi, ali wakufa.

26Ehudi anathawa pamene iwo ankadikira. Iye anadzera ku malo a miyala yozokotedwa kuja ndi kuthawa kupita ku Seiri. 27Atafika kumeneko, anayimba lipenga ku dziko la ku mapiri la Efereimu. Iye akutsogolera, Aisraeli onse anatsika naye pamodzi kuchoka ku mapiriko.

28Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke. 29Nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000. Ophedwawo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anathawa. 30Tsiku limenelo Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Israeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 80.

Samugara

31Ehudi atamwalira, panabwera Samugara mwana wa Anati. Iye anapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ngʼombe. Nayenso anapulumutsa Israeli.

La Bible du Semeur

Juges 3:1-31

1Voici quels peuples l’Eternel laissa subsister pour mettre à l’épreuve les Israélites qui n’avaient pas participé aux guerres pour la conquête de Canaan. 2Il voulait que les nouvelles générations d’Israélites, qui n’avaient pas connu la guerre, apprennent ce qu’est la guerre. 3L’Eternel laissa donc dans le pays les cinq principautés philistines, tous les Cananéens et les Sidoniens3.3 Des Phéniciens (Sidon était la plus ancienne ville de Phénicie)., les Héviens3.3 Voir note Jos 9.7. qui habitaient la chaîne du Liban depuis la montagne de Baal-Hermon jusqu’à Lebo-Hamath.

4Ces peuples servirent à éprouver les Israélites pour savoir s’ils obéiraient aux commandements que l’Eternel avait donnés à leurs ancêtres par Moïse. 5Ainsi les Israélites habitèrent au milieu des Cananéens, des Hittites, des Amoréens, des Phéréziens, des Héviens et des Yebousiens. 6Ils épousèrent leurs filles, donnèrent leurs propres filles à leurs fils et adorèrent leurs dieux.

Otniel

7Les Israélites firent ce que l’Eternel considère comme mal : ils oublièrent l’Eternel leur Dieu et rendirent un culte aux dieux Baals et Ashéras. 8L’Eternel se mit en colère contre Israël et il les livra au pouvoir de Koushân-Risheatayim, roi de Mésopotamie. Les Israélites lui furent assujettis pendant huit ans. 9Ils implorèrent l’Eternel et celui-ci leur suscita un libérateur en la personne d’Otniel, fils de Qenaz, qui était le frère cadet de Caleb. Et Otniel les délivra3.9 Otniel s’était déjà signalé par la prise d’Hébron (voir Jos 15.17 ; Jg 1.13-15).. 10L’Esprit de l’Eternel vint sur lui et il prit la direction d’Israël. Il partit en guerre contre Koushân-Risheatayim, roi de Mésopotamie, et l’Eternel lui donna la victoire sur lui. 11Après cela, la région fut en paix pendant quarante ans ; puis Otniel, fils de Qenaz, mourut.

Ehoud

12Les Israélites recommencèrent à faire ce que l’Eternel considère comme mal. A cause de cela, l’Eternel fortifia Eglôn, roi de Moab, et le dressa contre Israël. 13Eglôn s’allia aux Ammonites et aux Amalécites3.13 Les Ammonites étaient les descendants de Loth (Gn 19.38), les Amalécites ceux d’Esaü (Gn 36.12, 16) ; ils vivaient dans le Néguev (Nb 13.29). Ennemis des plus farouches, ils étaient voisins d’Israël à l’est et au sud., et ils attaquèrent les Israélites, les battirent et s’emparèrent de la ville des palmiers3.13 Jéricho (voir 1.16).. 14Pendant dix-huit ans, les Israélites furent assujettis à Eglôn, roi de Moab.

15Alors ils implorèrent l’Eternel, et celui-ci leur suscita un libérateur en la personne d’Ehoud, fils de Guéra, de la tribu de Benjamin, un homme qui était gaucher. Les Israélites le chargèrent de porter le tribut à Eglôn, roi de Moab. 16Ehoud se fabriqua une épée à deux tranchants d’environ cinquante centimètres de long et il la ceignit sous ses vêtements, le long de la cuisse droite. 17Il alla remettre le tribut à Eglôn, roi de Moab qui était très gros. 18Lorsqu’il eut fini de présenter le tribut, il renvoya les hommes qui l’avaient apporté. 19Arrivé aux idoles de pierre à côté de Guilgal, il revint sur ses pas et dit au roi : Majesté, j’ai un message secret à te communiquer. Le roi ordonna à tous ceux qui se tenaient autour de lui de le laisser, et tous ses familiers se retirèrent. 20Alors Ehoud s’approcha du roi qui était assis dans la chambre haute3.20 Sens incertain. Autre traduction : le palais d’été. qu’il s’était réservée sur la terrasse, au frais. Ehoud lui dit : J’ai pour toi un message de Dieu. Le roi se leva de son siège. 21De sa main gauche, Ehoud saisit l’épée qu’il portait sur sa cuisse droite et l’enfonça dans le ventre du roi. 22La poignée elle-même pénétra après la lame, et la graisse se referma sur la lame, car Ehoud laissa l’arme dans le ventre du roi, 23puis il sortit par le vestibule3.23 Autre traduction : par-derrière., après avoir fermé les portes de la chambre haute à clé derrière lui.

24Quand il fut sorti, les serviteurs du roi revinrent et ils constatèrent que les portes de la chambre haute étaient fermées à clé. Ils attendirent, se disant que le roi était en train de faire ses besoins dans la chambre d’été. 25Ils attendirent un bon moment. Enfin, ne sachant plus que penser, et comme il n’ouvrait toujours pas les portes, ils prirent la clé et ouvrirent eux-mêmes et voici que leur maître était étendu à terre, mort. 26Pendant qu’ils s’étaient ainsi attardés, Ehoud s’était échappé. Il dépassa les idoles de pierre et s’enfuit vers Seïra3.26 Localisation incertaine, dans la région du mont Séir en Edom ou au nord de Jéricho.. 27Dès qu’il fut arrivé là, il sonna du cor dans les montagnes d’Ephraïm. Les Israélites descendirent des collines et il se mit à leur tête.

28Suivez-moi, leur dit-il, car l’Eternel vous donne la victoire sur vos ennemis les Moabites.

Ils le suivirent donc et ils occupèrent les gués du Jourdain pour couper le passage aux Moabites, ne laissant personne traverser la rivière. 29Ils tuèrent ce jour-là environ dix mille hommes de Moab, tous robustes et aguerris et ils ne laissèrent aucun rescapé. 30Moab fut affaibli à partir de là par les Israélites et la région connut la paix pendant quatre-vingts ans.

Shamgar

31Après Ehoud, vint Shamgar, fils d’Anath. Il tua six cents Philistins avec un aiguillon à bœufs. Lui aussi fut un libérateur d’Israël.