Oweruza 2 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 2:1-23

Mngelo wa Yehova ku Bokimu

1Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu, 2ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? 3Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.”

4Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza, 5ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova.

Agonjetsedwa Chifukwa Chosamvera

6Yoswa atawuza Aisraeli kuti achoke, iwo anapita kukatenga dzikolo, aliyense dera lake. 7Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira.

8Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110. 9Ndipo anamuyika mʼmanda a mʼdziko lake, ku Timnati-Heresi mʼdziko la mapiri la Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.

10Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli. 11Choncho Aisraeli anayamba kuchita zinthu zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anatumikira Abaala. 12Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova. 13Iwo anasiya Yehova ndi kumatumikira Baala ndi Asiteroti. 14Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse. 15Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu.

16Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo. 17Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi. 18Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa. 19Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani.

20Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere, 21Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira. 22Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.” 23Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

士师记 2:1-23

耶和华责备以色列人

1耶和华的天使从吉甲来到波金,对以色列人说:“我带你们离开埃及,领你们去我起誓要赐给你们祖先的土地。我说,‘我永不废弃跟你们立的约, 2你们不可跟这里的居民立约,要毁掉他们的祭坛。’可是你们为什么不听呢? 3因此,我告诉你们,我必不赶走这里的居民,他们必成为你们肋旁的刺,他们的神明必成为你们的网罗。” 4以色列人听了耶和华的天使说的话,就放声大哭, 5他们称那地方为波金2:5 波金”意思是“哭泣”。,在那里向耶和华献祭。

约书亚去世

6约书亚遣散以色列人后,他们便各自去攻占所分得的土地。 7约书亚在世的时候,以色列人都事奉耶和华。他死后,那些目睹耶和华为以色列人行大事的长老还在世的时候,以色列人仍然事奉耶和华。 8耶和华的仆人、的儿子约书亚去世时享年一百一十岁。 9以色列人把他葬在他自己的土地上,在迦实山以北、以法莲山区的亭拿·希烈10那一代人都去世后,新一代不认识耶和华,也不知道耶和华为以色列人所行的事。

11以色列人做耶和华视为恶的事,祭拜巴力12他们背弃了领他们祖先离开埃及的上帝耶和华,追随、祭拜邻邦的各种神明,因而惹耶和华发怒。 13他们背弃耶和华,去祭拜巴力亚斯她录14耶和华向他们发怒,使他们遭到掠夺者的攻击和四周仇敌的压制,毫无抵抗之力。 15他们每次出战,耶和华都与他们为敌,使他们战败,正如祂的誓言。他们苦不堪言。

16后来,耶和华使士师2:16 士师”意思是“首领”。兴起,从掠夺者手中拯救他们。 17但他们不听从士师的话,与其他神明苟合,祭拜它们,很快偏离他们祖先的道路,没有像他们的祖先那样遵行耶和华的命令。 18耶和华见他们因敌人的压迫和苦待而哀号,就怜悯他们,使士师陆续兴起,并与每位士师同在。士师在世之日,耶和华从仇敌手中拯救他们。 19士师去世以后,他们又故态复萌,追随、祭拜其他神明,比他们的祖先更败坏。他们执迷不悟,怙恶不悛。 20耶和华向他们发怒,说:“这百姓违背了我跟他们祖先所立的约,不听从我的话。 21因此,我不再逐出约书亚去世时还没有赶走的外族人, 22我要借此试验以色列人,看他们是否像他们祖先一样谨遵我的道。” 23这就是为什么耶和华留下那些外族人,没有立刻把他们赶走,也没有把他们交在约书亚手中。