Oweruza 12 – CCL & CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 12:1-15

Yefita ndi Aefereimu

1Gulu la nkhondo la fuko la Efereimu linayitanidwa ndipo anawolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Nʼchifukwa chiyani unawoloka kukachita nkhondo ndi Aamoni osatiyitana kuti tipite nawe? Ife tikutenthera mʼnyumba mwakomu.”

2Yefita anayankha kuti, “Ine ndi anthu anga tinakangana kwambiri ndi Aamoni. Ndinakuyitanani koma inu simunandipulumutse mʼmanja mwawo. 3Nditaona kuti simundithandiza, ndinayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndinawoloka kukachita nkhondo ndi a Aamoni. Yehova anandithandiza ndipo ndinawagonjetsa. Nanga nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine lero kuti muchite nane nkhondo?”

4Choncho Yefita anasonkhanitsa anthu a ku Giliyadi ndi kuchita nkhondo ndi Aefereimu. Ndipo Agiliyadi anagonjetsa Aefereimu chifukwa Aefereimuwo amati, “Inu a Giliyadi ndinu othawa kuchokera ku Efereimu ndi pakati pa Amanase.” 5Choncho Agiliyadi analanda Aefereimu madooko a mtsinje wa Yorodani. Munthu aliyense wothawa ku Efereimu amati akanena kuti, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agaliyadi ankafunsa kuti, “Kodi ndiwe mu Efurati?” Ngati iye ayankha kuti, “Ayi” 6Ndiye amamuwuza kuti, “Nena kuti ‘Shiboleti.’ ” Tsono munthuyo akanena kuti Siboleti popeza samatha kutchula bwino mawuwa, ankamugwira ndi kumupha pomwepo pa madooko a mtsinje wa Yorodani. Nthawi imeneyo anaphedwa Aefereimu 42,000.

7Yefita anatsogolera Israeli zaka zisanu ndi chimodzi. Kenaka Yefita wa ku Giliyadi anamwalira, ndipo anayikidwa mu mzinda wake ku Giliyadi.

Ibizani, Eloni ndi Abidoni

8Atamwalira Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu anatsogolera Israeli. 9Iye anali ndi ana aamuna makumi atatu ndi ana aakazi makumi atatu. Anakwatitsa ana ake akaziwo kwa anthu a fuko lina, ndipo ana ake aamuna aja anawabweretsera atsikana makumi atatu kuti awakwatire amenenso anali a fuko lina. Ibizani anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 10Kenaka Ibizani anamwalira, ndipo anayikidwa mu Betelehemu.

11Iye atamwalira, Eloni wa fuko la Zebuloni anakhala mtsogoleri wa Aisraeli, ndipo anatsogolera Aisraeli kwa zaka khumi. 12Kenaka Eloni anamwalira ndipo anayikidwa ku Ayaloni mʼdziko la Zebuloni.

13Iye atamwalira, Abidoni mwana wa Hilelo wochokera ku Piratoni, anatsogolera Israeli. 14Iye anali ndi ana aamuna makumi anayi ndi zidzukulu makumi atatu, amene ankakwera pa abulu 70. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi zitatu. 15Ndipo Abidoni mwana wa Hilelo Mpiratoni uja anamwalira, nayikidwa ku Piratoni, mʼdziko la Efereimu, dziko lamapiri la Aamaleki.