Oweruza 10 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 10:1-18

Tola

1Atafa Abimeleki panabwera Tola mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo kudzapulumutsa Aisraeli. Iyeyu anali wa fuko la Isakara ndipo ankakhala ku Samiri mʼdziko la mapiri la Efereimu. 2Iye anatsogolera Aisraeli kwa zaka 23, ndipo anamwalira ndi kuyikidwa ku Samiri.

Yairo

3Atafa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi, amene anatsogolera Israeli kwa zaka 22. 4Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi. 5Atamwalira Yairi anayikidwa mʼmanda ku Kamoni.

Yefita

6Aisraeli anachitanso zoyipira Yehova. Iwo anatumikira Abaala ndi Asitoreti, milungu ya ku Aramu, Sidoni, Mowabu, Aamoni ndi Afilisti. Choncho analeka osatumikiranso Yehova. 7Tsono Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa Afilisti ndi Aamoni. 8Iwowa anawagonjetseratu Aisraeli mʼchaka chimenechi, ndipo kwa zaka 18 anakhala akusautsa Aisraeli onse amene anali pa tsidya la Yorodani, mʼdziko la Aamori ku Giliyadi. 9Aamori anawoloka mtsinje wa Yorodani kukathira nkhondo mafuko a Yuda, Benjamini ndi Efereimu kotero kuti Israeli anavutika kwambiri. 10Kenaka Aisraeli analira kwa Yehova kuti, “Ife takuchimwirani popeza tasiya Inu Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.”

11Yehova anawafunsa kuti, “Suja ine ndinakupulumutsani kwa Aigupto, Aamori, Aamoni ndi Afilisti? 12Ndiponso pamene Asidoni, Aamaleki ndi Amoni anakuzunzani, inu nʼkulirira kwa ine suja ndinakupulumutsani kwa anthu amenewa? 13Komabe inu mwandikana ndipo mukutumikira milungu ina. Choncho sindidzakupulumutsaninso. 14Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.”

15Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.” 16Ndipo anachotsa milungu ya chilendo pakati pawo ndi kuyamba kutumikira Yehova. Ndipo Yehova anamva chisoni poona mmene Aisraeli ankazunzikira.

17Tsono Aamoni anasonkhana ndi kumanga zithando za nkhondo ku Giliyadi. Nawonso Aisraeli anasonkhana ndi kumanga zithando zawo za nkhondo ku Mizipa. 18Kenaka anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi anayamba kufunsana kuti, “Kodi ndi munthu wotani amene atayambe kuthira nkhondo Aamoni? Iyeyu adzakhala mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”

New International Reader’s Version

Judges 10:1-18

Tola

1Tola rose up to save Israel. That happened after the time of Abimelek. Tola was from the tribe of Issachar. He was the son of Puah, who was the son of Dodo. Tola lived in Shamir. It’s in the hill country of Ephraim. 2Tola led Israel for 23 years. After he died, he was buried in Shamir.

Jair

3Jair became the leader after Tola. Jair was from the land of Gilead. He led Israel for 22 years. 4He had 30 sons. They rode on 30 donkeys. His sons controlled 30 towns in Gilead. Those towns are called Havvoth Jair to this day. 5After Jair died, he was buried in Kamon.

Jephthah

6Once again the Israelites did what was evil in the sight of the Lord. They served gods that were named Baal. They served female gods that were named Ashtoreth. They worshiped the gods of Aram and Sidon. They served the gods of Moab and Ammon. They also worshiped the gods of the Philistines. The Israelites deserted the Lord. They didn’t serve him anymore. 7So the Lord became very angry with them. He handed them over to the Philistines and the Ammonites. 8That year they broke Israel’s power completely. They treated the Israelites badly for 18 years. The people who did this lived east of the Jordan River. They lived in Gilead. That was the land of the Amorites. 9The Ammonites also went across the Jordan. They crossed over to fight against the tribes of Judah, Benjamin and Ephraim. Israel was suffering terribly. 10Then the Israelites cried out to the Lord. They said, “We have sinned against you. We have deserted our God. We have served gods that are named Baal.”

11The Lord replied, “The Egyptians and Amorites treated you badly. So did the Ammonites and Philistines. 12And so did the Amalekites and the people of Sidon and Maon. Each time you cried out to me for help. And I saved you from their power. 13But you have deserted me. You have served other gods. So I will not save you anymore. 14Go and cry out to the gods you have chosen. Let them save you when you get into trouble!”

15But the Israelites replied to the Lord, “We have sinned. Do to us what you think is best. But please save us now.” 16Then they got rid of the false gods that were among them. They served the Lord. And he couldn’t stand to see Israel suffer anymore.

17The Ammonites were called together to fight. They camped in the land of Gilead. Then the Israelites gathered together. They camped at the city of Mizpah. 18The leaders of Gilead spoke to one another. They said, “Who will lead the attack against the Ammonites? That person will be the ruler of all the people who live in Gilead.”