Obadiya 1 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Obadiya 1:1-21

Masomphenya a Obadiya

1Masomphenya a Obadiya.

Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti,

Tamva uthenga wochokera kwa Yehova:

Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti,

“Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.”

2“Taona, ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina;

udzanyozedwa kwambiri.

3Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,

iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe

ndipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali,

iwe amene umanena mu mtima mwako kuti,

‘Ndani anganditsitse pansi?’

4Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhanga

ndi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi,

ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”

akutero Yehova.

5“Anthu akuba akanabwera kwa iwe,

kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku,

aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe!

Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha?

Ngati anthu othyola mphesa akanafika,

kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?

6Koma Esau adzalandidwa zinthu zonse,

chuma chake chobisika chidzabedwa!

7Anthu onse ogwirizana nawo adzakupirikitsira kumalire;

abwenzi ako adzakunyenga ndi kukugonjetsa;

amene amadya chakudya chako adzakutchera msampha,

koma iwe sudzazindikira zimenezi.”

8Yehova akunena kuti, “Tsiku limenelo,

kodi sindidzawononga anthu onse anzeru a ku Edomu,

anthu odziwa zinthu mʼmapiri a Esau?

9Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha,

ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esau

adzaphedwa pa nkhondo.

10Chifukwa cha nkhanza zimene unachitira mʼbale wako Yakobo,

udzakhala wamanyazi;

adzakuwononga mpaka muyaya.

11Pamene adani

ankamulanda chuma chake

pamene alendo analowa pa zipata zake

ndi kuchita maere pa Yerusalemu,

pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo.

12Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wako

pa nthawi ya tsoka lake,

kapena kunyogodola Ayuda

chifukwa cha chiwonongeko chawo,

kapena kuwaseka pa nthawi ya

mavuto awo.

13Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu anga

pa nthawi ya masautso awo,

kapena kuwanyogodola

pa tsiku la tsoka lawo,

kapena kulanda chuma chawo

pa nthawi ya masautso awo.

14Sunayenera kudikirira pamphambano ya misewu

kuti uphe Ayuda othawa,

kapena kuwapereka kwa adani awo Ayuda opulumuka

pa nthawi ya mavuto awo.”

15“Tsiku la Yehova layandikira

limene adzaweruza mitundu yonse ya anthu.

Adzakuchitira zomwe unawachitira ena;

zochita zako zidzakubwerera wekha.

16Iwe unamwa pa phiri langa loyera,

koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza;

iwo adzamwa ndi kudzandira

ndipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi.

17Koma pa Phiri la Ziyoni padzakhala chipulumutso;

phirilo lidzakhala lopatulika,

ndipo nyumba ya Yakobo

idzalandira cholowa chake.

18Nyumba ya Yakobo idzasanduka moto

ndipo nyumba ya Yosefe idzasanduka lawi la moto;

nyumba ya Esau idzasanduka chiputu,

ndipo adzayitenthe pa moto ndi kuyipsereza.

Sipadzakhala anthu opulumuka

kuchokera mʼnyumba ya Esau.”

Yehova wayankhula.

19Anthu ochokera ku Negevi adzakhala

ku mapiri a Esau,

ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiri

adzatenga dziko la Afilisti.

Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya,

ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi.

20Aisraeli amene ali ku ukapolo

adzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati;

a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradi

adzalandira mizinda ya ku Negevi.

21Opulumukawo adzapita ku Phiri la Ziyoni

ndipo adzalamulira mapiri a Esau.

Koma ufumuwo udzakhala wa Yehova.