Nyimbo ya Solomoni 5 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nyimbo ya Solomoni 5:1-16

Mwamuna

1Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga;

ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga.

Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe;

ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.

Abwenzi

Idyani abwenzi anga, imwani;

Inu okondana, imwani kwambiri.

Mkazi

2Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso.

Tamverani, bwenzi langa akugogoda:

“Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa,

nkhunda yanga, wangwiro wanga.

Mutu wanga wanyowa ndi mame,

tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.”

3Ndavula kale zovala zanga,

kodi ndizivalenso?

Ndasamba kale mapazi anga

kodi ndiwadetsenso?

4Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko;

mtima wanga unagunda chifukwa cha iye.

5Ndinanyamuka kukamutsekulira wachikondi wangayo,

ndipo manja anga anali noninoni ndi mure,

zala zanga zinali mure chuchuchu,

pa zogwirira za chotsekera.

6Ndinamutsekulira wachikondi wanga,

koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita.

Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake.

Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze.

Ndinamuyitana koma sanandiyankhe.

7Alonda anandipeza

pamene ankayendera mzindawo.

Anandimenya ndipo anandipweteka;

iwo anandilanda mwinjiro wanga,

alonda a pa khoma aja!

8Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani,

mukapeza wokondedwa wangayo,

kodi mudzamuwuza chiyani?

Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi.

Abwenzi

9Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,

kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji?

Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotani

kuti uzichita kutipempha motere?

Mkazi

10Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzi

pakati pa anthu 1,000.

11Mutu wake ndi golide woyengeka bwino;

tsitsi lake ndi lopotanapotana,

ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala.

12Maso ake ali ngati nkhunda

mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,

ngati nkhunda zitasamba mu mkaka,

zitayima ngati miyala yamtengowapatali.

13Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya

zopatsa fungo lokoma.

Milomo yake ili ngati maluwa okongola

amene akuchucha mure.

14Manja ake ali ngati ndodo zagolide

zokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali.

Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovu

woyikamo miyala ya safiro.

15Miyendo yake ili ngati mizati yamwala,

yokhazikika pa maziko a golide.

Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni,

abwino kwambiri ngati mkungudza.

16Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri;

munthuyo ndi wokongola kwambiri!

Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa,

inu akazi a ku Yerusalemu.