Nyimbo ya Solomoni 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nyimbo ya Solomoni 4:1-16

Mwamuna

1Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga!

Ndithudi, ndiwe wokongola!

Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu.

Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi

zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.

2Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene,

zochokera kozisambitsa kumene.

Iliyonse ili ndi ana amapasa;

palibe imene ili yokha.

3Milomo yako ili ngati mbota yofiira;

pakamwa pako ndi pokongola kwambiri.

Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba

kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza.

4Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide,

yomangidwa bwino ndi yosalala;

pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000,

zishango zonsezo za anthu ankhondo.

5Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala,

ngati ana amapasa a nswala

amene akudya pakati pa maluwa okongola.

6Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira

ndipo mithunzi ikayamba kuthawa,

ndidzapita ku phiri la mure

ndi ku chitunda cha lubani.

7Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga;

palibe chilema pa iwe.

8Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga,

tiye tichoke ku Lebanoni,

utsikepo pa msonga ya Amana,

kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni,

kuchoka ku mapanga a mikango

ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa.

9Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima,

iwe wanditenga mtima

ndi kapenyedwe ka maso ako,

ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.

10Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa!

Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo,

ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse!

11Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi;

pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi.

Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.

12Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa;

ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa.

13Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza;

muli zipatso zokoma kwambiri,

muli hena ndi nadi,

14nadi ndi safiro,

kalamusi ndi sinamoni,

komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino.

Mulinso mure ndi aloe

ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri.

15Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda,

chitsime cha madzi oyenda,

mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni.

Mkazi

16Dzuka, iwe mphepo yakumpoto,

ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera!

Uzira pa munda wanga,

kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse.

Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake

ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.