Nyimbo ya Solomoni 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nyimbo ya Solomoni 3:1-11

1Usiku wonse ndili pa bedi langa

ndinafunafuna amene mtima wanga umamukonda;

ndinamufunafuna koma osamupeza.

2Ndikudzuka tsopano ndipo ndidzayendayenda mu mzinda,

mʼmisewu yake ndi mʼmabwalo ake;

ndidzamufunafuna amene mtima wanga umamukonda.

Kotero ine ndinamufunafuna iyeyo koma osamupeza.

3Alonda anandipeza

pamene ankayendera mzinda.

“Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?”

4Nditawapitirira pangʼono

ndinamupeza amene mtima wanga umamukonda.

Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achoke

mpaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga,

mʼchipinda cha amene anandibereka.

5Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani

pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo:

Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa

mpaka pamene chifunire ichocho.

6Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululu

ngati utsi watolotolo,

wonunkhira mure ndi lubani,

zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda?

7Ona! Chimenecho ndi chonyamulira Solomoni,

choperekezedwa ndi asilikali 60,

anthu amphamvu a ku Israeli,

8onse atanyamula lupanga,

onse odziwa bwino nkhondo,

aliyense ali ndi lupanga pambali pake,

kukonzekera zoopsa za usiku.

9Mfumu Solomoni anadzipangira chonyamulirachi;

anachipanga ndi matabwa ochokera ku Lebanoni.

10Milongoti yake anayipanga yasiliva,

kumbuyo kwake kwa golide.

Mipando yake inakutidwa ndi nsalu yapepo,

anakongoletsa mʼkati mwake ndi chikondi

cha akazi a ku Yerusalemu.

11Tukulani inu akazi a ku Ziyoni

ndipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu,

chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuveka

pa tsiku la ukwati wake,

tsiku limene mtima wake unasangalala.