Nyimbo ya Solomoni 1 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nyimbo ya Solomoni 1:1-17

1Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse.

Mkazi

2Undipsompsone ndi milomo yako

chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo.

3Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino;

dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa.

Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda!

4Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire!

Mfumu indilowetse mʼchipinda chake.

Abwenzi

Ife timasangalala ndi kukondwera nawe,

tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo.

Mkazi

Amachita bwinotu potamanda iwe!

5Ndine wakuda, komatu ndine wokongola,

inu akazi a ku Yerusalemu,

ine ndine wakuda ngati tenti ya ku Kedara,

ngati makatani a tenti ya Solomoni.

6Musandiyangʼane monyoza chifukwa ndine wakuda,

ndine wakuda chifukwa cha dzuwa.

Alongo anga anandikwiyira

ndipo anandigwiritsa ntchito mʼminda ya mpesa;

munda wangawanga sindinawusamalire.

7Ndiwuze iwe, amene ndimakukonda, kumene umadyetsa ziweto zako

ndi kumene umagoneka nkhosa zako nthawi yamasana.

Ndikhalirenji ngati mkazi wachiwerewere

pambali pa ziweto za abwenzi ako?

Abwenzi

8Ngati sukudziwa iwe wokongola kwambiri kuposa akazi ena,

ngati sukudziwa, tsatira makwalala a nkhosa

ndipo udyetse ana ambuzi

pambali pa matenti a abusa.

Mwamuna

9Iwe bwenzi langa,

uli ngati kavalo wamkazi ku magaleta a Farao.

10Masaya ako ndi okongola ndi ndolo zamʼmakutuzo,

khosi lako likukongola ndi mikanda yamiyala yamtengowapatali.

11Tidzakupangira ndolo zagolide

zokongoletsedwa ndi mikanda yasiliva.

Mkazi

12Pamene mfumu inali pa malo ake odyera,

mafuta anga onunkhira anamveka fungo lake.

13Wokondedwa wanga ali ngati kathumba ka mure kwa ine,

kamene kamakhala pakati pa mawere angawa.

14Wokondedwa wanga ali ngati mpukutu wa maluwa ofiira,

ochokera ku minda ya mpesa ya ku Eni-Gedi.

Mwamuna

15Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi!

Ndithu, ndiwe chiphadzuwa,

maso ako ali ngati nkhunda.

Mkazi

16Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi!

Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri!

Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira.

Mwamuna

17Mitanda ya nyumba yathu ndi ya mkungudza,

phaso lake ndi la mtengo wa payini.

Korean Living Bible

아가 1:1-17

1이것은 솔로몬이 지은 노래 중의 노래이다.

첫번째 노래

2(여자) 나에게 입맞춰 주세요. 당신의 사랑은 포도주보다 더 달콤합니다.

3당신의 기름이 향기롭고 당신의 이름이 쏟은 향수와 같으므로 처녀들이 당신을 사랑합니다.

4나를 데려가 주세요. 자, 함께 달려갑시다. 왕이 나를 자기 궁전으로 데려가셨으니 우리는 정말 행복할 것입니다. 당신의 사랑이 포도주보다 나으므로 모든 여자들이 당신을 사랑하는 것도 당연합니다.

5예루살렘의 여자들아, 나는 비록 검지만 아름답단다. 내가 1:5 원문에는 ‘계달의 장막 같을지라도’검은 천막처럼 그을렸어도 솔로몬 궁전의 휘장처럼 아름답단다.

6내 피부가 검다고 나를 흘겨보지 말아라. 햇볕에 그을렸을 뿐이란다. 내 오빠들이 화를 내어 나를 포도원에서 일하게 하였으므로 내가 몸을 돌볼 시간이 없었다.

7내가 사랑하는 님이시여, 오늘은 당신이 양떼를 어디서 먹이며 정오에는 어디에서 쉬는지 말해 주세요. 어째서 내가 이리저리 방황하며 당신 친구들의 양떼 가운데서 당신을 찾아야 합니까?

8(남자) 세상에서 가장 아름다운 여인이여, 그대가 나 있는 곳을 모른다면 내 양떼의 발자취를 따라 목자들의 천막 곁에서 그대의 염소 새끼를 먹이시오.

9나의 사랑이여, 그대는 암망아지처럼 사랑스럽구려.

10머리를 늘어뜨린 그대의 뺨과 목걸이로 장식한 그대의 목이 참으로 아름답소이다.

11우리가 그대를 위해 금으로 귀고리를 만들어 은을 박아 주겠소.

12(여자) 왕이 식탁에 앉았을 때 내 향수 냄새가 진동하였네.

13내 사랑하는 님은 내 품속의 몰약 주머니 같고

141:14 또는 ‘엔게디 포도원의 고벨화 송이로구나’엔 – 게디 정원의 꽃송이 같구나.

15(남자) 나의 사랑이여, 그대는 정말 아름답구려. 그대의 눈은 비둘기 같소이다.

16(여자) 나의 사랑하는 님이시여, 당신은 정말 멋있고 잘생겼습니다. 우리 침대는 푸른 풀밭이요

17우리 집의 들보는 백향목이며 서까래는 잣나무입니다.