Numeri 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 8:1-26

Za Nyale

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Yankhula ndi Aaroni kuti pamene uyimika nyale zisanu ndi ziwiri, nyalezo ziziyaka kutsogolo kwa choyikapo nyale.”

3Aaroni anachitadi zomwezo. Anayimika nyale ndi kuziyangʼanitsa kumene kunali choyikapo nyale monga Yehova analamulira Mose. 4Choyikapo nyalecho chinapangidwa motere: chinasulidwa kuchokera ku golide, kuyambira pa tsinde pake mpaka ku maluwa ake. Choyikapo nyalecho chinapangidwa monga momwe Yehova anaonetsera Mose.

Za Kupatulidwa kwa Alevi

5Yehova anawuza Mose kuti, 6“Tenga Alevi pakati pa Aisraeli ndipo uwayeretse. 7Powayeretsa uchite izi: uwawaze madzi oyeretsa ndipo amete thupi lawo lonse ndi kuchapa zovala zawo kuti adziyeretse. 8Atenge ngʼombe yayimuna yayingʼono ndi chopereka cha chakudya cha ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Atengenso ngʼombe ina yayimuna, yayingʼono, ya chopereka chopepesera machimo. 9Ubwere nawo Aleviwo kutsogolo kwa tenti ya msonkhano ndipo usonkhanitse gulu la Aisraeli. 10Ubwere nawo pamaso pa Yehova, ndipo Aisraeli asanjike manja awo pa iwo. 11Aaroni apereke Alevi aja pamaso pa Yehova ngati chopereka choweyula kuchokera kwa Aisraeli kuti akhale okonzeka kugwira ntchito ya Yehova.

12“Alevi akatsiriza kusanjika manja awo pa mitu ya ngʼombe zazimuna, imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza ya kwa Yehova, kupepesera machimo a Alevi. 13Uyimiritse Aleviwo pamaso pa Aaroni ndi ana ake aamuna ndipo uwapereke ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. 14Pochita zimenezi mudzapatula Alevi pakati pa Aisraeli ndipo Aleviwo adzakhala anga.

15“Utatha kuyeretsa ndi kupereka Aleviwo monga nsembe yoweyula, apite kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano. 16Iwo ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwathunthu kwa Ine. Ndawatenga kuti akhale anga mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Mwisraeli aliyense wamkazi. 17Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini. 18Ndipo ndatenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa mu Israeli. 19Mwa Aisraeli onse, ndapereka Alevi kuti akhale mphatso kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kugwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti azikapereka nsembe yopepesera machimo, kuti mliri usadzaphe Aisraeli pamene ayandikira ku malo wopatulika.”

20Mose, Aaroni pamodzi ndi gulu lonse la Israeli anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose. 21Alevi anadziyeretsa ndi kuchapa zovala zawo. Kenaka Aaroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe yopepesera machimo yowayeretsa. 22Zitatha zimenezi, Alevi anapita kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose.

23Yehova anawuza Mose kuti, 24“Ntchito za Alevi ndi izi: Amuna a zaka 24 kapena kuposera pamenepa ndiye azibwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano. 25Koma akakwana zaka makumi asanu, apume pa ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku ndi kulekeratu kugwira ntchitoyo. 26Atha kuthandiza abale awo kugwira ntchito za ku tenti ya msonkhano, koma iwowo asamagwire ntchitoyo. Mmenemu ndimo ugawire ntchito yomwe azigwira Alevi.”