Numeri 5 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 5:1-31

Ukhondo wa pa Msasa

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa. 3Muchotse amuna komanso amayi ndipo muwatulutsire kunja kwa msasa kuti asadetse msasa wawo kumene Ine ndimakhala pakati pawo.” 4Aisraeli anachitadi zimenezi. Anawatulutsira kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose.

Kukonza Zolakwika

5Yehova anati kwa Mose, 6“Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene mwamuna kapena mayi walakwira mnzake mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Munthuyo ndi wochimwa ndithu ndipo 7ayenera kuwulula tchimo limene anachitalo. Ayenera kubweza zonse zimene anawononga, ndipo awonjezerepo chimodzi mwa magawo asanu ndi kuzipereka kwa munthu amene anamulakwirayo. 8Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake. 9Zopereka zonse zopatulika zomwe Aisraeli abwera nazo kwa wansembe zikhale za wansembeyo. 10Mphatso zilizonse zopatulika ndi za munthuyo, koma zomwe wapereka kwa wansembe ndi za wansembeyo.’ ”

Mkazi Wosakhulupirika

11Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, 12“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mkazi wa munthu wina ayenda njira yosayenera nakhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, 13nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita), 14mwamuna wake ndi kuyamba kuchita nsanje ndi kukayikira mkazi wakeyo kuti ndi wodetsedwa, komanso ngati amuchitira nsanje ndi kumukayikira ngakhale asanadzidetse, 15apite naye mkaziyo kwa wansembe. Ndipo popita atengenso gawo lakhumi la chopereka chaufa wa barele wokwana kilogalamu imodzi mʼmalo mwa mkaziyo. Asathire mafuta pa nsembeyo kapena lubani, chifukwa ndi nsembe ya chopereka ya chakudya yopereka chifukwa cha nsanje, nsembe yozindikiritsa tchimo.’ ”

16“ ‘Wansembe abwere naye mkaziyo ndi kumuyimitsa pamaso pa Yehova. 17Ndipo wansembeyo atenge madzi oyera mʼmbiya ya dothi ndi kuyika mʼmadzimo fumbi lapansi la mʼTenti ya Msonkhano. 18Wansembe atayimika mkaziyo pamaso pa Yehova, amumasule tsitsi lake, ndipo ayike mʼmanja mwake nsembe yozindikiritsa tchimo, nsembe yachakudya ya nsanje, wansembeyo atanyamula madzi owawa omwe amabweretsa temberero.’ 19Kenaka wansembeyo alumbiritse mkaziyo ndi kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sanagonane ndi iwe ndipo sunayende njira yoyipa ndi kukhala wodetsedwa pomwe uli pa ukwati ndi mwamuna wako, madzi owawa awa omwe amabweretsa temberero asakupweteke. 20Koma ngati wayenda njira yoyipa uli pa ukwati ndi mwamuna wako ndi kudzidetsa pogonana ndi mwamuna amene si mwamuna wako,’ 21pamenepo wansembe alumbiritse mkaziyo ndi mawu a matemberero ndi kumuwuza kuti, ‘Yehova achititse anthu ako kukutemberera ndi kukunyoza pamene awononga ntchafu yako ndi kutupitsa mimba yako. 22Madzi awa obweretsa temberero alowe mʼthupi mwako ndi kutupitsa mimba yako ndi kuwononga ntchafu yako.’ ”

“Pamenepo mkaziyo anene kuti, ‘Ameni, ameni.’ ”

23“ ‘Wansembe alembe matemberero amenewa mʼbuku ndi kuwanyika mʼmadzi owawa aja. 24Amwetse mkaziyo madzi owawawo omwe amabweretsa temberero, ndipo madzi amenewo adzalowa mʼmimba mwake ndi kuyambitsa ululu woopsa. 25Wansembe achotse mʼmanja mwa mkaziyo nsembe yachakudya ya nsanje ija, nayiweyula pamaso pa Yehova ndi kuyipereka pa guwa lansembe. 26Tsono wansembeyo atapeko ufa dzanja limodzi kuti ukhale wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa lansembe. Atatha izi, amwetse mkaziyo madzi aja. 27Ndipo ngati mkaziyo anadzidetsadi ndi kukhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, pamene amwa madzi obweretsa matemberero aja, nalowa mʼmimba mwake, adzamva ululu woopsa. Mimba yake idzatupa ndi ntchafu yake idzawonongeka ndipo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu ake. 28Koma ngati mkaziyo sanadzidetse ndi kuti alibe tchimo, adzakhala wopanda mlandu ndipo adzabereka ana.

29“ ‘Limeneli ndiye lamulo la nsanje pamene mkazi wayenda njira yoyipa ndi kudzidetsa ali pa ukwati ndi mwamuna wake, 30kapena pamene maganizo a nsanje abwera kwa mwamuna wake chifukwa chokayikira mkazi wakeyo. Wansembe azitenga mkazi wotere ndi kumuyimiritsa pamaso pa Yehova ndipo agwiritse ntchito lamulo lonseli kwa mkaziyo. 31Mwamunayo adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkaziyo adzasenza zotsatira za tchimo lake.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 5:1-31

送不洁净之人出营

1耶和华对摩西说: 2“你吩咐以色列人把所有患麻风病、漏症和因碰过死尸而不洁净的人, 3无论男女,都送到营外,免得他们玷污了营地,因为我住在其中。” 4以色列人就照耶和华对摩西的吩咐,把这些人送到营外。

赔偿条例

5耶和华对摩西说: 6“你把以下条例告诉以色列人。

“无论男女,若损害别人就是不忠于耶和华,就是犯罪。 7那人必须认罪,赔偿损失,并且必须加赔五分之一。 8如果受害人已死,又没有可以接受赔偿的近亲,赔偿就属于耶和华,要归祭司所有。那人还要再献上一只公绵羊为自己赎罪。 9以色列人带来奉献的一切圣物都要归祭司所有。 10各人奉献的圣物,无论是什么,都要归祭司所有。”

疑妻不贞

11耶和华对摩西说: 12-14“你把以下条例告诉以色列人。

“若有人怀疑妻子出轨,暗中与人通奸,却没有证据,在无法确定是自己疑心还是妻子不忠的情况下, 15他要带妻子到祭司那里,同时为妻子带去一公斤大麦面粉作为供物。不可在上面浇油或加乳香,因为这是因疑心而献上的素祭,要证明他妻子是否有罪。

16“祭司要把那妇人带到耶和华面前, 17用陶器盛一些圣水,从圣幕的地上取一些尘土撒在水中, 18然后让那妇人站在耶和华面前,解开她的头发,把那素祭放在她手里。祭司要拿着带给罪人咒诅的苦水, 19叫她发誓。祭司要对她说,‘如果你没有出轨,没有背着丈夫与人通奸,就不会被这苦水所害。 20如果你曾出轨,背着丈夫与人通奸, 21-22你喝下这苦水后,愿耶和华使你大腿消瘦、肚腹肿胀、不能生育,使你被同胞咒诅和唾弃。’她要说,‘阿们!阿们!’ 23祭司要把这咒诅写在书卷上,再放在苦水里把字洗掉。 24祭司要让妇人喝这可带来咒诅的苦水,不忠的妇人喝下后,肚子会感到剧痛。 25祭司要从妇人手中接过她丈夫因疑心而献的素祭,在耶和华面前摇一摇,然后带到祭坛那里。 26他要从素祭中取出一把面粉作为象征放在祭坛上焚烧,然后叫那妇人喝下苦水。 27如果她曾与人通奸,背叛了丈夫,这可带来咒诅的苦水进入她体内后,会引起剧痛,使她肚腹肿胀、大腿消瘦、不能生育,她也将被同胞咒诅。 28但如果她是贞洁的,没有与人通奸,就不会受伤害,仍能生育。

29“这就是处理丈夫怀疑妻子不忠的条例。遇到妻子背着丈夫与人通奸, 30或是丈夫怀疑妻子不忠,就要让妻子站在耶和华面前,由祭司对她执行这条例。 31无论结果怎样,丈夫都无罪,但妻子若有罪,必承担罪责。”