Numeri 4 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 4:1-49

Akohati

1Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: 2“Werengani Akohati omwe ndi gawo limodzi la Alevi monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo. 3Werengani amuna onse amene ali ndi zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu amene amabwera kudzagwira ntchito mu tenti ya msonkhano.

4“Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri. 5Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni. 6Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.

7“Pa tebulo pamene pamakhala buledi wa ansembe aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo, ndipo aziyikapo mbale, mabeseni, zipande ndi mitsuko yoperekera nsembe yachakumwa. Aziyikaponso buledi wokhala pamenepo nthawi zonse. 8Tsono pamwamba pa izi aziyalapo nsalu yofiira, ndi kuzikuta mʼzikopa za akatumbu ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.

9“Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta. 10Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake.

11“Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira.

12“Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake.

13“Azichotsa phulusa la pa guwa lansembe lamkuwa ndi kuyalapo nsalu yapepo pamwamba pake. 14Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake.

15“Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.

16“Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.”

17Yehova anawuzanso Mose ndi Aaroni kuti, 18“Onetsetsani kuti mabanja a fuko la Kohati asachotsedwe kwa Alevi. 19Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula. 20Koma Akohati asalowe kukaona zinthu zopatulika, ngakhale kanthawi pangʼono, chifukwa akatero adzafa.”

Ageresoni

21Yehova anawuza Mose kuti, 22“Werenganso Ageresoni monga mwa mabanja ndi mafuko awo. 23Uwerenge amuna onse a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu zakubadwa amene amabwera kudzatumikira ku tenti ya msonkhano.

24“Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi: 25Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano, 26makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi. 27Ntchito yawo yonse, kaya kunyamula kapena kugwira ntchito zina, achite Ageresoni motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Uwagawire ntchito zonse zimene akuyenera kugwira. 28Iyi ndiye ntchito ya fuko la Ageresoni ku tenti ya msonkhano. Ntchito zawo zichitike motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.

Amerari

29“Werenga Amerari monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo. 30Werenga amuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu zakubadwa amene akatumikire mu tenti ya msonkhano. 31Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde, 32ndiponso mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema, zingwe ndi zipangizo zake zonse ndiponso zonse zokhudzana ndi ntchito yake. Uwuze munthu aliyense chomwe ayenera kuchita. 33Iyi ndiyo ntchito ya mafuko a Amerari pamene akugwira ntchito ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.”

Chiwerengero cha Fuko la Levi

34Mose, Aaroni ndi atsogoleri a magulu a anthu anawerenga Akohati monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 35Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano, 36atawawerenga mwa mafuko awo, anali 2,750. 37Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.

38Ageresoni anawerengedwanso monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 39Amuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano, 40atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 2,630. 41Ichi chinali chiwerengero cha Ageresoni mwa mabanja awo amene ankatumikira ku tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.

42Amerari anawawerenga monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 43Amuna onse kuyambira zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzatumikira ntchito mu tenti ya msonkhano, 44atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 3,200. 45Ichi ndicho chinali chiwerengero cha mabanja a Amerari. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga momwe Yehova anawalamulira kudzera mwa Mose.

46Kotero Mose, Aaroni ndi atsogoleri a Israeli anawerenga Alevi onse monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 47Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu omwe anabwera kudzagwira ntchito yonyamula zinthu ku tenti ya msonkhano 48analipo 8,580. 49Aliyense anamupatsa ntchito ndi kumuwuza choti anyamule monga mwa lamulo la Yehova kudzera mwa Mose.

Anawawerenga chomwechi potsata zimene Yehova analamula Mose.

Bibelen på hverdagsdansk

4. Mosebog 4:1-49

Levitternes arbejde med åbenbaringsteltet

1Da sagde Herren til Moses og Aron: 2-3„Optæl hvor mange mandlige efterkommere af Levis søn Kehat, der er mellem 30 og 50 år. Det er dem, der skal arbejde i åbenbaringsteltet 4med de helligste ting:

5Hver gang I er klar til at pakke lejren sammen, skal Aron og hans sønner først gå ind i helligdommen og tage forhænget mellem det hellige og det allerhelligste rum ned og lægge det over pagtens ark. 6Oven på det skal de lægge et kraftigt stykke læder, som igen skal dækkes med purpurfarvet klæde, før de anbringer bærestængerne i guldringene.

7Dernæst skal de brede et purpurfarvet klæde ud over bordet med de hellige brød og anbringe de forskellige fade, skåle og kander, der bruges ved drikofrene, oven på klædet sammen med de brød, der altid ligger fremme. 8Ovenpå igen skal de brede et skarlagenrødt klæde og et kraftigt stykke læder, før de anbringer bærestængerne i bordets guldringe.

9Lysestagen, lamperne, vægesaksene, vægebakkerne og beholderne til olivenolie skal anbringes på bærestativet, hvorefter de dækkes med et purpurfarvet klæde 10og derefter med et stykke kraftigt læder.

11Så skal de brede et purpurfarvet klæde over røgelsesalteret af guld, dække det med et kraftigt stykke læder og anbringe bærestængerne i alterets guldringe. 12Alle de øvrige redskaber, der bruges i helligdommen, skal dækkes med purpurfarvet klæde og kraftigt læder, før de anbringes på bærestativet.

13Brændofferalteret skal også dækkes til med et purpurfarvet klæde, men først skal asken fjernes. 14Alle redskaber, der bruges ved ofringen, skal lægges oven på klædet—både bakker til gløder, kødgafler, skovle og skåle—hvorefter det hele skal dækkes til med kraftigt læder. Til sidst skal bærestængerne anbringes i ringene.

15Når Aron og hans sønner har pakket helligdommens inventar og redskaber sammen, skal kehatitterne træde til og bære det hele til næste lejrplads. Men hvis de rører disse hellige ting, skal de dø. Det er altså kehatitternes opgave at bære helligdommens inventar.

16Arons søn Eleazar er ansvarlig for lampeolien, den hellige røgelse, det daglige afgrødeoffer og salveolien—ja, han skal have overopsynet med åbenbaringsteltet og alt dets inventar og de hellige redskaber.”

17Dernæst sagde Herren til Moses og Aron: 18„I må passe på, at kehatitterne ikke mister livet. 19I skal nøje overholde de forskrifter, jeg her har givet, så de ikke dør under udførelsen af deres opgave. Det er Aron og hans sønner, der skal fortælle kehatitterne, hvad de hver især skal bære. 20Men kehatitterne må først komme ind i helligdommen, efter at det hele er pakket ned, for hvis de ser de hellige ting, skal de dø.”

21Herren sagde nu til Moses: 22-23„Optæl hvor mange mandlige efterkommere af Levis søn Gershon, der er mellem 30 og 50 år. De skal også arbejde ved åbenbaringsteltet. 24-25Det er deres opgave at transportere boligens teltduge, de to tagdækninger af vædderskind og kraftigt læder samt indgangsforhænget. 26Derudover har de til opgave at transportere forgårdens teltvægge og forhænget over indgangen til forgården, som indhegner helligdommen og brændofferalteret. Endelig skal de også transportere diverse snore og værktøj, der bruges ved arbejdet. 27Aron og hans sønner skal uddelegere arbejdet blandt gershonitterne, 28og gershonitterne skal stå til regnskab for deres arbejde over for Arons søn Itamar.

29-30Optæl hvor mange mandlige efterkommere af Levis søn Merari, der er mellem 30 og 50 år. De skal også arbejde ved åbenbaringsteltet. 31Efter at teltet er pakket sammen, er det deres opgave at afmontere og transportere helligdommens vægmoduler, tværstænger, stolper og sokler, 32forgårdens stolper og sokler, samt alle pløkker og barduner—og alt det værktøj, der bruges under arbejdet. Enhver skal være helt klar over, hvori deres opgave består, 33så arbejdet kan gå hurtigt; og Arons søn Itamar skal have overopsynet med det.”

34-37På Herrens befaling foretog Moses og Aron og folkets ledere så en optælling af levitterne. Først lavede de en liste over Kehats slægt, familie for familie, over alle mænd, der var mellem 30 og 50 år, og som havde pligt til at arbejde ved åbenbaringsteltet. Det samlede antal var 2750. 38-41En tilsvarende optælling over Gershons slægt blev til 2630, 42-45og over Meraris slægt 3200. 46-48Det samlede antal mænd mellem 30 og 50 år, der havde pligt til at arbejde ved åbenbaringsteltet, var 8580. 49Aron mønstrede alle disse mænd og forklarede dem deres opgaver, sådan som Herren havde befalet gennem Moses.