Numeri 36 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 36:1-13

Cholowa cha Ana Aakazi a Zelofehadi

1Atsogoleri a mabanja a fuko la Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase omwe anali ochokera ku fuko la ana a Yosefe anabwera ndi kuyankhula ndi Mose, atsogoleri ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli. 2Iwo anati, “Pamene Yehova analamula mbuye wanga kuti apereke dziko ngati cholowa kwa Aisraeli mwa maere, anakulamulani inu kupereka cholowa cha mʼbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi. 3Tsopano ngati akwatiwa ndi aamuna ochokera ku mafuko ena a mitundu ya Aisraeli, cholowa chawo chidzatengedwa kuchoka pa cholowa cha makolo athu ndipo adzachiwonjezera ku fuko limene akwatiwakolo. Ndipo gawo lina la cholowacho, lopatsidwa kwa ife lidzatengedwa. 4Pamene chaka cha chikondwerero cha zaka makumi asanu, cha Aisraeli chafika, cholowa chawo chidzawonjezeredwa ku fuko limene iwo akwatiwako. Ndipo katundu wawo adzachotsedwa pa cholowa cha fuko la makolo athu.”

5Tsono mwa lamulo la Yehova, Mose anapereka lamulo ili kwa Aisraeli: “Zimene ana a Yosefe akunena ndi zoona. 6Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo 7kuti cholowa cha Israeli chisapite ku fuko lina, pakuti Mwisraeli aliyense ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. 8Mwana wamkazi aliyense amene adzalandira cholowa cha dziko la fuko lililonse la Israeli ayenera kukwatiwa ndi munthu wa fuko la abambo ake. 9Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.”

10Choncho ana aakazi a Zelofehadi anachita monga Yehova analamulira Mose. 11Ana aakazi a Zelofehadi amene ndi Mahila, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, anakwatiwa ndi asuweni awo a ku mbali ya abambo awo. 12Anakwatiwa mʼmafuko a zidzukulu za Manase mwana wa Yosefe, ndipo cholowa chawo chinakhalabe mʼfuko la abambo awo.

13Awa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kupyolera mwa Mose ku chigwa cha Mowabu mʼmbali mwa Yorodani, ku Yeriko.

Korean Living Bible

민수기 36:1-13

여자 상속인의 결혼 문제

1요셉 자손 중에서 므낫세의 손자이며 마길의 아들인 길르앗 집안 가장 들이 이스라엘 지도자들 앞에서 모세에게

2이렇게 말하였다. “여호와께서는 제비를 뽑아 이스라엘 백성에게 땅을 나누어 주라고 당신에게 명령하셨으며 또 우리 형제 슬로브핫의 땅을 그의 딸들에게 주라고 명령하셨습니다.

3그러나 그 딸들이 다른 지파 사람과 결혼하게 되면 그들의 땅이 시집 지파의 재산이 되어 우리 지파의 땅은 줄어들게 될 것입니다.

4그리고 일단 다른 지파에게 넘어간 땅은 희년이 되어도 다시 우리에게 돌아오지 않을 것입니다.”

5그래서 모세는 여호와의 지시를 받아 이스라엘 백성에게 이렇게 말하였다. “므낫세 지파 사람들의 말이 옳습니다.

6여호와께서는 슬로브핫의 딸들이 자기가 원하는 사람과 결혼할 수 있으나 자기 지파 안에서만 결혼해야 한다고 말씀하셨습니다.

7이렇게 하면 이스라엘 각 지파의 재산이 자기 지파 재산으로 유지될 것입니다.

8이스라엘 각 지파에서 재산을 상속받은 딸들은 반드시 자기 지파 사람과 결혼해야 합니다. 그래야만 이스라엘 자손이 그 조상의 유산을 보존하게 될 것입니다.

9이렇게 함으로써 땅이 한 지파에서 다른 지파로 이전되지 않고 각 지파는 자기들의 땅을 계속 소유하게 될 것입니다.”

10-12슬로브핫의 딸 말라와 디르사와 호글 라와 밀가와 노아는 여호와께서 모세에게 명령하신 대로 요셉의 아들 므낫세 지파 안에서 그들의 사촌과 결혼하였다. 그래서 그들의 재산이 그 아버지의 지파에 그대로 남아 있게 되었다.

13이상은 여호와께서 여리고 맞은편 요단 강변의 모압 평야에서 모세를 통해 이스라엘 백성에게 주신 명령과 규정이다.