Numeri 34 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 34:1-29

Malire a Dziko la Kanaani

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:

3“ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere. 4Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, 5kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.

6“ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.

7“ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori 8ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi, 9ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.

10“ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. 11Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti. 12Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere.

“ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”

13Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka, 14chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo. 15Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”

16Yehova anawuza Mose kuti, 17“Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni. 18Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. 19Mayina awo ndi awa:

Kalebe mwana wa Yefune,

wochokera ku fuko la Yuda,

20Semueli mwana wa Amihudi,

wochokera ku fuko la Simeoni;

21Elidadi mwana wa Kisiloni,

wochokera ku fuko la Benjamini;

22Buki mwana wa Yogili,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;

23Hanieli mwana wa Efodi,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;

24Kemueli mwana wa Sifitani,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.

25Elizafani mwana wa Parinaki,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;

26Palitieli mwana wa Azani,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,

27Ahihudi mwana wa Selomi,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;

28Pedaheli mwana wa Amihudi,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”

29Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 34:1-29

迦南的疆域

1耶和华对摩西说: 2“你把以下指示告诉以色列人。

“你们进入赐给你们作产业的迦南后,你们四境的疆界如下。

3“南部疆界从旷野沿着以东边界延伸,东起死海的尽头, 4往南至亚克拉滨坡南面,经直到加低斯·巴尼亚南面,再延伸至哈萨·亚达,经押们5转向埃及河,直到地中海。

6“西部以地中海为界。

7“北部疆界从地中海开始直到何珥山, 8再到哈马口,经西达达9西斐仑直到哈萨·以难

10“东部疆界从哈萨·以难一直划到示番11往南到亚延东面的利比拉,再往南到基尼烈湖东岸。 12然后沿约旦河南下直到死海。这是你们国土四面的疆界。”

13摩西又对以色列人说:“这就是耶和华吩咐用抽签的方式分给你们九个半支派的土地。 14吕便支派和迦得支派已经按着宗族得到了他们的土地,玛拿西半个支派也得到了土地。 15这两个半支派的土地在耶利哥对面的约旦河东岸。”

分地的首领

16耶和华对摩西说: 17“负责给你们分地的是以利亚撒祭司和的儿子约书亚18每支派要选出一位首领来协助分地。

19“以下是这些首领的名字:

犹大支派耶孚尼的儿子迦勒

20西缅支派亚米忽的儿子示姆利

21便雅悯支派基斯伦的儿子以利达

22支派约利的儿子布基

23约瑟之子玛拿西支派以弗的儿子汉聂

24以法莲支派拾弗但的儿子基姆利

25西布伦支派帕纳的儿子以利撒番

26以萨迦支派阿散的儿子帕铁

27亚设支派示罗米的儿子亚希忽

28拿弗他利支派亚米忽的儿子比达黑。”

29这些是奉耶和华之命在迦南以色列人分产业的首领。