Numeri 31 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 31:1-54

Aisraeli Agonjetsa Amidiyani

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Uwabwezere zoyipa Amidiyani chifukwa cha zimene anachitira Aisraeli. Ukatha kuchita zimenezi, iwe udzamwalira.”

3Ndipo Mose anati kwa Aisraeli, “Perekani zida kwa ena mwa anthu anu kuti akamenyane ndi Amidiyani ndi kuwabwezera choyipa mʼmalo mwa Yehova. 4Mutumize ku nkhondoko amuna 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli.” 5Choncho amuna okwana 12,000 anatenga zida kukonzekera nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli. 6Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza.

7Iwo anamenyana ndi Amidiyani monga momwe Yehova analamulira Mose ndipo anapha mwamuna aliyense. 8Mwa anthu ophedwawo munali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani. Ndipo anaphanso ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori. 9Aisraeli anagwira ukapolo amayi a Chimidiyani ndi ana awo ndipo analandanso ngʼombe, ziweto zawo zina zonse ndi katundu wawo yense. 10Anawotcha mizinda yonse imene Amidiyani ankakhalamo pamodzi ndi misasa yawo yonse. 11Anatenga zonse zimene analanda ku nkhondoko, anthu ndi zoweta zomwe. 12Ndipo anabwera nawo akapolowo ndi zolanda ku nkhondozo kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa gulu lonse la Aisraeli ku misasa yawo ku chigwa cha Mowabu, mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko.

13Mose, wansembe Eliezara ndi atsogoleri onse a gululo anapita kukakumana nawo kunja kwa misasa. 14Mose anakwiya nawo akuluakulu a magulu a ankhondowo: olamulira 1,000 ndi olamulira 100, amene ankachokera ku nkhondo.

15Iye anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mwawaleka amoyo amayi onsewa?” 16Paja iwo ndi amene ankatsatira uphungu wa Balaamu ndiponso ndi amene anachititsa Aisraeli kuti asiye Yehova pa zimene zinachitika ku Peori, kotero mliri unagwera anthu a Yehova. 17Tsopano iphani munthu wamwamuna aliyense. Ndiponso iphani mayi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna, 18koma sungani mtsikana aliyense amene sanagonepo ndi mwamuna.

19“Inu nonse amene mwaphapo wina wake, kapena kukhudza aliyense amene anaphedwa mukhale kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachitatu mudziyeretse nokha pamodzi ndi akapolo anu. 20Muyeretsenso zovala zanu ndi china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ubweya wa mbuzi kapenanso ndi mtengo.”

21Tsono wansembe Eliezara anati kwa asilikali amene anapita ku nkhondo aja, “Lamulo limene Yehova anapereka kwa Mose ndi ili: 22Golide, siliva, mkuwa, chitsulo, chiwaya, mtovu 23ndi china chilichonse chimene sichingapse ndi moto muchidutsitse pa moto, ndipo chidzayeretsedwa. Komanso chiyeretsedwe ndi madzi oyeretsa. Ndipo chilichonse chimene chingapse ndi moto muchidutsitse mʼmadzimo. 24Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muchape zovala zanu ndipo mudzayera. Mukatero mutha kulowa mu msasa.”

Kugawana Zolanda ku Nkhondo

25Yehova anawuza Mose kuti, 26“Iwe ndi wansembe Eliezara ndiponso akuluakulu a mabanja a anthuwa, muwerenge anthu onse ndi ziweto zomwe zinagwidwa ku nkhondo. 27Mugawe zolanda ku nkhondozo magawo awiri, lina la ankhondo amene anapita ku nkhondo, lina la anthu onse. 28Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Yehova, pa zofunkha 500 zilizonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, ngʼombe, bulu ndi nkhosa. 29Utenge zimenezo pa theka la gawo la ankhondowo ndipo upereke kwa wansembe Eliezara kuti zikhale zopereka zanu kwa Yehova. 30Kuchokera pa theka la gawo la Aisraeli, utengeko cholanda chimodzi pa makumi asanu aliwonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa, mbuzi kapena zoweta zina. Uzipereke kwa Alevi amene ntchito yawo ndi yosamalira tenti ya Yehova.” 31Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara anachita monga Yehova analamulira Mose.

32Zotsala pa zolanda ku nkhondo zimene ankhondowo anatenga zinali nkhosa 675,000, 33Ngʼombe 72,000, 34abulu 61,000, 35ndi atsikana omwe sanagonepo ndi mwamuna 32,000.

36Gawo la ankhondo amene anapita ku nkhondo linali:

nkhosa 337,500, 37mwa zimenezi gawo la Yehova linali 675;

38ngʼombe zinalipo 36,000 ndipo gawo la Yehova linali 72;

39abulu analipo 30,500 ndipo gawo la Yehova linali 61;

40anthu analipo 16,000 ndipo gawo la Yehova linali 32.

41Mose anapereka kwa wansembe Eliezara gawo limene linali loyenera kupereka kwa Yehova monga momwe Yehova analamulira Mose.

42Pa gawo la Aisraeli, Mose anapatula theka limodzi kuchotsa pa zolanda ku nkhondo zonse zimene zinabwera ndi ankhondo aja. 43Tsono gawo la Aisraeli linali ili: nkhosa 337,500, 44ngʼombe 36,000, 45abulu 30,500, 46anthu 16,000. 47Kuchoka pa gawo la Aisraelilo, Mose anatengapo chimodzi pa zolanda ku nkhondo makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo anazipereka kwa Alevi amene ankayangʼanira tenti ya Yehova monga Yehova analamulira Mose.

48Pamenepo omwe ankayangʼanira magulu a ankhondo olamulira 1,000 ndi olamulira 100 anabwera kwa Mose, 49iwo anati kwa iye, “Ife anthu anu tawerenga ankhondo amene timawalamulira. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene wasowa. 50Ndipo tabweretsa zopereka kwa Yehova zimene munthu aliyense anapeza: ziwiya zagolide, zibangiri, zigwinjiri, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda kuti tichitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.”

51Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara analandira kuchokera kwa atsogoleriwo golide pamodzi ndi zipangizo zonse zosula. 52Golide yense wochokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 zomwe Mose ndi Eliezara anapereka ngati mphatso kwa Yehova zinali zolemera makilogalamu 200. 53Wankhondo aliyense anatenga zomwe analanda yekha ku nkhondo. 54Mose ndi Eliezara wansembe analandira golide kuchokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 ndi kukamuyika mu tenti ya msonkhano ngati chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 31:1-54

攻打米甸人

1耶和华对摩西说: 2“你要为以色列人向米甸人报仇,之后你将归到祖先那里。” 3于是,摩西对民众说:“你们男子要拿起兵器去攻打米甸,为耶和华报仇。 4以色列的每个支派要派一千人出战。” 5于是,他们从以色列每个支派选出一千人,武装了一万二千军兵。 6每个支派选出的一千军兵由摩西派遣出战,以利亚撒祭司的儿子非尼哈拿着圣所的器具和号角随行。 7他们照耶和华对摩西的吩咐去攻打米甸人,杀死了米甸的所有男子, 8包括以未利金苏珥户珥利巴五个王,还杀了比珥的儿子巴兰9以色列人虏获了米甸的妇女、孩子、牛羊和财物, 10将他们的城邑营寨付之一炬, 11带走了掳掠的人畜等战利品。 12他们来到耶利哥对面、约旦河边的摩押平原,把战利品交给摩西以利亚撒祭司和以色列全体会众。

13摩西以利亚撒祭司以及所有民众的首领都到营外迎接他们。 14摩西对回来的千夫长和百夫长发怒, 15说:“你们为什么让这些妇女活着? 16就是她们听了巴兰的指使在毗珥引诱以色列人背叛耶和华,以致瘟疫降在耶和华的会众身上。 17现在,你们要杀掉所有的男孩以及与男人发生过关系的女子, 18但可以留下那些处女。 19你们凡杀了人和碰过死人的都要在营外待七天。在第三天和第七天,你们要洁净自己及掳来的人, 20也要洁净自己所有的衣服、皮具、山羊毛织的物品和木器。” 21以利亚撒祭司对打仗回来的军兵说:“以下是耶和华借摩西颁布的律例。 22金、银、铜、铁、锡、铅, 23凡耐火之物都要用火来洁净,还要用除秽水加以洁净;不耐火之物要用水来洁净。 24第七天,你们洗完衣服后就洁净了,可以回营。”

25耶和华对摩西说: 26“你和以利亚撒祭司以及会众的各族长要统计俘虏和牲畜的数目, 27然后把这些战利品分成两份,一份给出征的战士,一份给会众。 28要从战士分得的俘虏、牛、驴和羊群中抽出五百分之一献给耶和华, 29要把那五百分之一交给以利亚撒祭司献给耶和华作举祭。 30要从会众分得的俘虏和牛、驴、羊等牲畜中抽出五十分之一交给在我圣幕司职的利未人。” 31摩西以利亚撒祭司遵命而行。

32战士虏获的战利品中有六十七万五千只羊, 33七万二千头牛, 34六万一千头驴, 35三万二千名处女。 36战士分得的战利品有三十三万七千五百只羊, 37其中六百七十五只献给耶和华; 38三万六千头牛,其中七十二头献给耶和华; 39三万零五百头驴,其中六十一头献给耶和华; 40一万六千名处女,其中三十二人献给耶和华。 41摩西照耶和华的吩咐,把献给耶和华的举祭交给以利亚撒祭司。

42以色列会众分得的那一半战利品,即摩西从出征之人的战利品中分出来给他们的, 43有三十三万七千五百只羊、 44三万六千头牛、 45三万零五百头驴、 46一万六千名处女。 47摩西照耶和华的吩咐,从中抽出五十分之一交给在圣幕里司职的利未人。

48统领军队的千夫长和百夫长来见摩西49说:“仆人们统计了手下出征的战士,未失一兵一卒。 50现在我们把各自虏获的臂环、镯子、图章戒指、耳环、项链等金器都带来献给耶和华,作为我们生命的赎价。” 51摩西以利亚撒祭司收了他们所献的各种金制物品。 52千夫长和百夫长献给耶和华作举祭的金子约二百公斤。 53战士则保留了自己虏获的财物。 54摩西以利亚撒祭司就把千夫长和百夫长献的金子带进会幕,在耶和华面前作以色列人的纪念。