Numeri 27 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 27:1-23

Ana Aakazi a Zelofehadi

1Kenaka ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wamwamuna wa Manase, a mʼmabanja a Manase, mwana wa Yosefe anabwera. Mayina a ana aakaziwo anali awa: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anakayima 2pa chipata cha tenti ya msonkhano pamaso pa Mose, wansembe Eliezara, atsogoleri ndi anthu onse, ndipo anati, 3“Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna. 4Nʼchifukwa chiyani dzina la abambo athu lasowa pakati pa fuko lawo, kodi popeza analibe mwana wamwamuna? Tipatseni cholowa chathu pakati pa abale a abambo athu.”

5Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova 6ndipo Yehova anati kwa iye, 7“Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo.

8“Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. 9Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chakecho kwa abale ake. 10Ngati alibe abale muzipereka cholowa chake kwa abale a abambo ake. 11Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ”

Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose

12Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kwera phiri la Abarimu kuti ukaone dziko limene ndalipereka kwa Aisraeli. 13Ukakaliona udzamwalira ngati Aaroni mʼbale wako, 14chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini).

15Mose anati kwa Yehova, 16“Ngati nʼkotheka Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, sankhani munthu woti ayangʼanire gulu ili kuti 17alitsogolere potuluka ndi polowa, kuti anthu a Yehova asakhale ngati nkhosa zopanda mʼbusa.”

18Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene ali ndi mzimu wa utsogoleri, ndipo umusanjike dzanja lako. 19Umuyimiritse pamaso pa wansembe Eliezara ndi pamaso pa gulu lonse ndipo umupatse mphamvu zolamulira, anthuwo akuona. 20Umupatse gawo lina la ulemerero wako kuti Aisraeli onse azimumvera. 21Ayime pamaso pa wansembe Eliezara, amene adzamudziwitse zimene Yehova akufuna pogwiritsa ntchito Urimu. Iye akalamula, Aisraeli onse azituluka ndipo akalamulanso, Aisraeliwo azibwereranso.”

22Mose anachita monga Yehova anamulamulira. Anatenga Yoswa ndi kumuyimiritsa pamaso pa Eliezara wansembe ndi pamaso pa gulu lonse. 23Ndipo anamusanjika manja ndi kumupatsa mphamvu, monga Yehova ananenera kudzera mwa Mose.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

民數記 27:1-23

女兒的繼承權

1西羅非哈約瑟之子瑪拿西的玄孫、瑪吉的曾孫、基列的孫子、希弗的兒子。他的女兒是瑪拉挪阿曷拉密迦得撒。她們前來, 2站在會幕門口對摩西以利亞撒祭司、眾首領和全體會眾說: 3「我們的父親死在曠野,他並沒有跟可拉一夥一起反叛耶和華,而是因自己的罪而死,沒有留下兒子。 4難道因為他沒有兒子,他的名字就要從族中消失嗎?請讓我們在父親的家族中分一份產業吧。」 5摩西就把她們的請求呈到耶和華面前。 6耶和華對摩西說: 7西羅非哈的女兒說得有理。你要從她們父親的家族中分一份產業給她們,讓她們繼承父親的產業。 8你要告訴以色列人,『人死後如果沒有兒子,就由女兒繼承產業; 9如果沒有女兒,就由其兄弟繼承; 10如果沒有兄弟,就由其父的兄弟繼承; 11如果其父沒有兄弟,就由其族中最近的親屬繼承。』」這是耶和華吩咐摩西頒佈給以色列人的律例。

約書亞接替摩西做首領

12耶和華對摩西說:「你上亞巴琳山去眺望我賜給以色列人的土地。 13看了以後,你就要像你哥哥亞倫一樣去祖先那裡了。 14因為會眾在曠野反叛我的時候,你們二人沒有按照我的指示取水,沒有在他們面前尊我為聖。」耶和華指的是米利巴泉事件,發生在曠野的加低斯15摩西對耶和華說: 16「耶和華啊,你是賜人生命的上帝,求你立一個人做會眾的首領, 17帶領他們或進或退,免得你的會眾像沒有牧人的羊群。」 18耶和華對摩西說:「的兒子約書亞心裡有聖靈,你把他召來,按手在他身上, 19讓他站在以利亞撒祭司和全體會眾面前,當著他們的面任命他做首領, 20把你的權柄賜給他,使以色列全體會眾都聽從他。 21遇到事情,他要去以利亞撒祭司那裡,讓祭司藉著烏陵為他求問我。他和全體會眾或進或出都要聽從以利亞撒的指示。」 22摩西遵命而行,把約書亞召來,讓他站在以利亞撒祭司和全體會眾面前, 23然後照耶和華的吩咐按手在他的頭上,任命他做首領。