Numeri 24 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 24:1-25

1Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu. 2Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye 3ndipo ananena uthenga wake:

“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,

uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,

4uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,

yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,

yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:

5“Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo,

misasa yako, iwe Israeli!

6“Monga zigwa zotambalala,

monga minda mʼmbali mwa mtsinje,

monga aloe wodzalidwa ndi Yehova,

monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.

7Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake;

mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri.

“Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi;

ufumu wake udzakwezedwa.

8“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto

ali ndi mphamvu ngati za njati.

Amawononga mitundu yomuwukira

ndi kuphwanya mafupa awo,

amalasa ndi mivi yake.

9Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi,

monga mkango waukazi, adzamuputa ndani?

“Amene adalitsa iwe, adalitsike

ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”

10Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka. 11Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”

12Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine, 13kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena? 14Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”

Uthenga Wachinayi wa Balaamu

15Ndipo iye ananena uthenga wake nati,

“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,

uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka.

16Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,

amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba,

amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,

amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:

17“Ndikumuona iye koma osati tsopano;

ndikumupenya iye koma osati pafupi.

Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo;

ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli.

Iye adzagonjetsa Mowabu

ndi kugonjetsa ana onse a Seti.

18Edomu adzagonjetsedwa;

Seiri, mdani wake, adzawonongedwa

koma mphamvu za Israeli zidzachuluka.

19Wolamulira adzachokera mwa Yakobo

ndipo adzawononga otsala a mu mzindamo.”

Uthenga Wachisanu wa Balaamu

20Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu:

“Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu

koma potsiriza pake adzawonongeka.”

Uthenga Wachisanu ndi Chimodzi wa Balaamu

21Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake,

“Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa,

chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe;

22komabe inu Akeni mudzawonongedwa,

pamene Asuri adzakutengeni ukapolo.”

Uthenga Wachisanu ndi Chiwiri wa Balaamu

23Ndipo ananenanso uthenga wina kuti,

“Aa, ndani adzakhala ndi moyo Mulungu akachita zimenezi?

24Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu;

kupondereza Asuri ndi Eberi,

koma iwonso adzawonongeka.”

25Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake.