Numeri 20 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 20:1-29

Madzi Ochokera Mʼthanthwe

1Pa mwezi woyamba gulu lonse la Aisraeli linafika ku chipululu cha Zini, ndipo anakhala ku Kadesi. Miriamu anafera kumeneko ndipo anayikidwa mʼmanda.

2Kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa, choncho anthuwo anasonkhana motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. 3Anakangana ndi Mose kuti, “Kunali bwino ifenso tikanangofa pamene abale athu anafa pamaso pa Yehova! 4Chifukwa chiyani unabweretsa gulu la Yehova mʼchipululu muno, kuti ife ndi ziweto zathu tife kuno? 5Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto ndi kutibweretsa kumalo woyipa ano? Kuno kulibe tirigu kapena nkhuyu, mphesa kapena makangadza. Ndipo kuno kulibenso madzi akumwa!”

6Mose ndi Aaroni anachoka mu msonkhano ndi kupita pa khomo la tenti ya msonkhano, nagwa pansi chafufumimba ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. 7Yehova anati kwa Mose, 8“Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mʼbale wako Aaroni musonkhanitse anthu onse pamodzi. Uyankhule ndi thanthwe ilo iwo akuona ndipo lidzatulutsa madzi ake. Udzatulutsa madzi mʼthanthwe limeneli kuti anthu onse ndi ziweto zawo amwe.”

9Choncho Mose anatenga ndodo pamaso pa Yehova monga momwe anamulamulira. 10Mose ndi Aaroni anasonkhanitsa anthuwo pamodzi ku thanthwelo ndipo Mose anawawuza kuti, “Tamverani osamvera inu, kodi tikupatseni madzi kuchokera ku thanthwe ili?” 11Choncho Mose anatukula dzanja lake ndi kumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake ndipo madzi ambiri anatuluka mwamphamvu, ndipo anthu ndi ziweto zawo anamwa.

12Koma Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Chifukwa chakuti simunandikhulupirire ndiponso simunandilemekeze monga Woyera pamaso pa Aisraeli, simudzalowetsa anthuwa mʼdziko limene ndikupereka kwa iwo.”

13Awa anali madzi a ku Meriba, kumene Aisraeli anakangana ndi Yehova ndiponso kumene Yehovayo anadzionetsa yekha kuti ndi Woyera pakati pawo.

Aedomu Akaniza Njira Aisraeli

14Mose anatumiza amithenga kuchokera ku Kadesi kupita kwa mfumu ya ku Edomu, kukanena kuti,

“Mʼbale wako Israeli akunena izi: Inuyo mukudziwa za mavuto onse amene anatigwera. 15Makolo athu anapita ku Igupto ndipo tinakhala kumeneko zaka zambiri. Aigupto anatizunza pamodzi ndi makolo athuwo, 16koma titalirira Yehova, Iyeyo anamva kulira kwathuko ndipo anatitumizira mngelo amene anatitulutsa ku Igupto.”

“Taonani, tsopano tili pano pa Kadesi, mzinda wa mʼmalire a dziko lanu. 17Chonde mutilole tidutse mʼdziko lanu. Sitidzera mʼminda yanu kapena mu mpesa wanu, kapenanso kumwa madzi mʼchitsime chilichonse. Tidzayenda kutsata msewu waukulu wa mfumu ndipo sitidzapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere mpaka titadutsa malire a dziko lanu.”

18Koma Edomu anayankha kuti,

“Musadutse kuno: Mukangoyesera tidzabwera ndi kumenyana nanu ndi lupanga.”

19Aisraeli anayankha kuti,

“Tidzayenda motsata msewu waukulu. Ndipo ngati ife kapena ziweto zathu tidzamwa madzi anu tidzalipira. Tikungofuna tidutse nawo, palibenso china.”

20Koma Edomu anayankhanso kuti,

“Musadutse.”

Kenaka Edomu anatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu komanso lamphamvu. 21Edomu anakaniza Israeli kuti adutse mʼdziko lake, choncho Israeli anabwerera.

Aaroni Amwalira

22Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Kadesi ndipo linafika ku phiri la Hori. 23Ali pa phiri la Hori, pafupi ndi malire a Edomu, Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, 24“Aaroni adzakakhala ndi anthu a mtundu wake, sadzalowa mʼdziko limene ndapereka kwa Aisraeli, chifukwa nonse munandiwukira motsutsana ndi malamulo anga ku madzi a ku Meriba. 25Tenga Aaroni ndi mwana wake wamwamuna Eliezara ndipo ukwere nawo ku phiri la Hori. 26Uvule Aaroni zovala zake ndipo umuveke mwana wake Eliezara, pakuti Aaroni adzafera komweko, ndipo adzakakhala ndi anthu a mtundu wake.”

27Mose anachita monga Yehova anamulamulira: Anapita ku phiri la Hori gulu lonse likuona. 28Pamenepo Mose anavula Aaroni zovala zake ndi kuveka mwana wake Eliezara. Aaroni anafa kumeneko pamwamba pa phirilo. Koma Mose ndi Eliezara anatsika ku phiriko, 29ndipo pamene anthu onse anamva kuti Aaroni wafa, nyumba yonse ya Israeli inamulira Aaroniyo masiku makumi atatu.

Korean Living Bible

민수기 20:1-29

가데스 사건

1이스라엘 백성은 월에 진 광야에 도착하여 가데스에서 진을 쳤으며 거기서 미리암이 죽어 장사하였다.

2그 곳에는 물이 없었기 때문에 백성들이 모세와 아론에게 몰려와

3이렇게 항의하였다. “여호와께서 우리 형제들을 죽이실 때 우리가 함께 죽지 못한 것이 한스럽소!

4어째서 당신들이 우리를 이 광야로 끌고 와서 우리 짐승들과 함께 우리를 죽이려 하시오?

5무엇 때문에 당신들은 우리를 이집트에서 끌어내어 아무것도 없는 이 황무지로 데려왔소? 이 곳에는 곡식도 없고 무화과도 없고 포도도 없고 석류도 없고 마실 물마저 없지 않소!”

6모세와 아론이 그들을 떠나 성막 입구로 가서 여호와 앞에 엎드리자 여호와께서 영광의 광채로 그들에게 나타나셔서

7모세에게 말씀하셨다.

8“너는 네 지팡이를 가지고 네 형 아론과 함께 백성을 모으고 그들 앞에서 바위를 향해 물을 내라고 말하라. 너는 그 바위에서 물을 나오게 하여 백성과 모든 짐승이 마시게 하라.”

9그래서 모세는 여호와께서 명령하신 대로 여호와 앞에 두었던 지팡이를 가져와

10아론과 함께 백성을 그 바위 앞에 모아 놓고 “이 반역자들이여, 우리가 당신들을 위해 이 바위에서 물을 내야 하겠소?” 하며

11지팡이를 들어 바위를 두 번 쳤다. 그러자 물이 분수처럼 솟구쳐나와 백성과 그들의 짐승이 다 그 물을 마셨다.

12그러나 여호와께서 모세와 아론에게 “너희가 나를 믿지 않고 이스라엘 백성들 앞에서 나를 거룩한 자로 높이지 않았으므로 너희는 그들을 인도하여 내가 준 땅으로 들어가지 못할 것이다!” 하고 말씀하셨다.

13여기서 이스라엘 백성이 여호와와 다투었으므로 이 곳 물을 20:13 ‘다툰다’ 는 뜻.‘므리바’ 물이라 하였다. 그리고 여호와께서는 자신이 거룩한 분임을 그들에게 보여 주셨다.

에돔이 이스라엘 백성을 통과하지 못하게 함

14모세는 가데스에서 에돔 왕에게 사람을 보내 이렇게 말하였다. “우리는 당신의 친척 이스라엘의 후손입니다. 우리가 겪은 고생을 들어서 잘 알고 있겠지만

15우리 조상들이 이집트로 내려갔기 때문에 우리가 거기서 오랫동안 살게 되었습니다. 그런데 이집트 사람들이 우리 조상들과 우리를 학대하므로

16우리가 여호와께 부르짖었더니 우리의 부르짖음을 들으시고 천사를 보내 우리를 이집트에서 인도해 내셨습니다. 그래서 지금 우리는 당신 영토의 경계 지역인 가데스에 있습니다.

17우리가 당신의 땅을 통과할 수 있도록 허락해 주십시오. 우리가 밭이나 포도원으로 통과하지 않고 우물물도 마시지 않으며 큰 길로만 통과하여 왕의 땅을 다 지나갈 때까지 그 길에서 이탈하지 않겠습니다.”

18그러나 에돔 왕은 “우리 땅을 통과하지 못한다. 네가 만일 내 땅에 발을 들여놓으면 내가 나가서 칼로 너를 치겠다” 하고 대답하였다.

19그래서 이스라엘 사람들이 “우리가 큰 길로만 통과하겠습니다. 만일 우리나 우리 짐승이 왕의 나라에 있는 물을 마시면 우리가 그 값을 다 치르겠습니다. 다만 우리가 원하는 것은 왕의 땅을 통과하는 것뿐입니다” 하였으나

20에돔 왕은 “통과하지 못한다” 하고 거절하였다. 그러고서 그가 많은 군대를 거느리고 국경 지대로 나와

21이스라엘 백성이 그리로 통과하지 못하게 하였으므로 그들은 하는 수 없이 거기서 발길을 돌렸다.

아론의 죽음

22-23이스라엘 백성은 가데스를 출발하여 에돔 국경 지대인 호르산에 도착하였다. 거기서 여호와께서는 모세와 아론에게 이렇게 말씀하셨다.

24“아론은 내가 이스라엘 백성에게 준 땅에 들어가지 못하고 죽게 될 것이다. 이것은 너희 두 사람이 므리바에서 내 명령을 거역하였기 때문이다.

25모세 너는 아론과 그의 아들 엘르아살을 데리고 호르산으로 올라가거라.

26그리고 거기서 아론의 제사장복을 벗겨 그의 아들 엘르아살에게 입혀라. 아론은 거기서 죽게 될 것이다.”

27그래서 모세는 여호와께서 명령하신 대로 모든 백성이 지켜 보는 가운데 그들을 데리고 호르산으로 올라갔다.

28모세가 아론의 옷을 벗겨 그의 아들 엘르아살에게 입힌 후에 아론은 산꼭대기에서 죽었고 모세와 엘르아살은 그 산에서 내려왔다.

29모든 이스라엘 백성은 아론이 죽었다는 말을 듣고 30일 동안 그의 죽음을 슬퍼하였다.