Numeri 17 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 17:1-13

Kuphukira kwa Ndodo ya Aaroni

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake. 3Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse. 4Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe. 5Ndodo ya munthu amene ndamusankha idzachita maluwa potero ndidzaletsa madandawulo osatha a Aisraeli otsutsana nawe.”

6Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo. 7Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano.

8Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi. 9Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake.

10Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.” 11Mose anachita monga Yehova anamulamulira.

12Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika! 13Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?”