Numeri 16 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 16:1-50

Kora, Datani ndi Abiramu Awukira Mose

1Kora mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Perezi, ana a Rubeni, anayamba kudzikuza, 2ndipo anawukira Mose. Mʼgulu mwawo munali atsogoleri a Aisraeli 250, anthu otchuka amene anasankhidwa ndi anthu pa msonkhano. 3Iwo anasonkhana kudzatsutsana ndi Mose ndi Aaroni nawawuza kuti, “Mwawonjeza! Anthu onsewa ndi oyera, aliyense wa iwo, ndipo Yehova ali pakati pawo. Chifukwa chiyani mukudzikuza pakati pa gulu lonse la Yehova?”

4Mose atamva izi, anagwa chafufumimba. 5Ndipo iye anawuza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti, “Yehova mawa mmawa adzasonyeza yemwe ndi wake ndiponso amene ndi woyera mtima. Munthuyo adzabwera pafupi ndi Iye. Munthu amene adzamusankheyo adzamusendeza pafupi. 6Iwe Kora pamodzi ndi onse amene akukutsatira chitani izi: Tengani zofukizira 7ndipo mawa muyikemo moto ndi lubani pamaso pa Yehova. Munthu amene Yehova amusankhe ndiye amene ali woyera. Alevi inu mwawonjeza kwambiri!”

8Mose anawuzanso Kora kuti, “Inu Alevi, tsopano tamverani! 9Kodi sizinakukwanireni kuti Mulungu wa Israeli anakupatulani pakati pa gulu lonse la Aisraeli ndi kukubweretsani pafupi ndi Iye, kuti muzigwira ntchito ku nyumba ya Yehova ndi kumayima pamaso pa gulu, kumatumikira? 10Wakubweretsa iwe pamodzi ndi Alevi anzako kufupi ndi Iye mwini. Koma tsopano ukufuna kutenganso unsembe. 11Nʼkulakwira Yehova kuti iwe ndi gulu lako lonseli mwasonkhana kuti mutsutsane ndi Yehova. Kodi Aaroni ndani kuti muzikangana naye?”

12Kenaka Mose anayitana Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu koma iwo anati, “Sitibwera! 13Kodi sikukwanira kuti unatitulutsa, kutichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphe mʼchipululu muno? Kodi tsopano ukufunanso kutilemetsa? 14Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!”

15Pamenepo Mose anakwiya kwambiri ndipo anati kwa Yehova, “Musalandire chopereka chawo. Sindinatenge kalikonse kwa iwo ngakhale bulu, ndiponso sindinalakwire wina aliyense wa iwo.”

16Mose anati kwa Kora, “Iwe ndi okutsatira onse mudzaonekere pamaso pa Yehova mawa, iweyo ndi iwowo pamodzi ndi Aaroni. 17Munthu aliyense akatenge chofukizira ndi kuyikamo lubani, zofukizira 250 zonse pamodzi ndi kuzibweretsa pamaso pa Yehova. Iwe ndi Aaroni mudzabweretsenso zofukizira zanu.” 18Choncho munthu aliyense anatenga chofukizira chake nayikamo moto ndi lubani, ndipo anayima pamodzi ndi Mose ndi Aaroni pa khomo la tenti ya msonkhano. 19Kora atasonkhanitsa omutsatira ake onse amene amatsutsa nawo pa khomo la tenti ya msonkhano, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa gulu lonselo. 20Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 21“Chokani pakati pa gulu ili kuti ndithetse mkanganowu kamodzinʼkamodzi.”

22Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa chafufumimba ndipo analira mokweza, “Chonde Mulungu, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, kodi mudzakwiyira gulu lonse pamene munthu mmodzi yekha ndiye amene wachimwa?”

23Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, 24“Uza gulu lonse kuti, ‘Khalani kutali ndi matenti a Kora, Datani ndi Abiramu.’ ”

25Mose anayimirira napita kwa Datani, Abiramu ndi kwa akuluakulu a Israeli amene ankamutsatira. 26Anachenjeza gulu lonse kuti, “Khalani kutali ndi matenti a anthu oyipawa! Musakhudze kanthu kawo kalikonse, mukatero mudzawonongedwa limodzi nawo chifukwa cha machimo awo.” 27Choncho anthuwo anachokadi ku matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali atatuluka nayima pamodzi ndi akazi awo, ana awo ndi makanda awo pa makomo a matenti awo.

28Tsono Mose anati, “Umu ndi mmene mudzadziwire kuti Yehova ndiye amene anandituma kuti ndichite zinthu zonsezi ndipo kuti si maganizo anga. 29Ngati anthu awa afa ndi imfa ya chilengedwe ndi kuwachitikira zomwe zimachitikira munthu aliyense, ndiye kuti Yehova sananditume. 30Koma Yehova akachita china chake chachilendo, nthaka nitsekula pakamwa pake ndi kuwameza iwo pamodzi ndi zonse zimene ali nazo, iwowa nʼkulowa mʼmanda ali moyo, pamenepo mudzazindikira kuti anthu amenewa ananyoza Yehova.”

31Atangotsiriza kuyankhula zimenezi, nthaka ya pamene anayimapo inagawikana 32ndipo dziko linatsekula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi nyumba zawo ndi anthu onse a Kora ndi katundu wawo yense. 33Analowa mʼmanda amoyo pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. Nthaka inawatsekera ndi kuwawononga ndipo sanaonekenso. 34Atamva kulira kwawo, Aisraeli onse amene anali pafupi ndi anthuwo anathawa akufuwula kuti, “Nthaka imezanso ife!”

35Ndipo moto wochokera kwa Yehova unabwera nʼkunyeketsa anthu 250 amene ankapereka nsembe yofukiza aja.

36Yehova anawuza Mose kuti, 37“Uza Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe kuti atenge zofukizirazo pakati pa mitembo yopsererayo ndipo amwazire makalawo kutali chifukwa zofukizirazo nʼzopatulika. 38Izi ndi zofukizira za anthu omwe anafa chifukwa cha uchimo wawo. Musule zofukizirazo kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, chifukwa zinaperekedwa kwa Yehova ndipo ndi zopatulika. Zimenezi zikhale chizindikiro kwa Aisraeli.”

39Choncho Eliezara, wansembe, anasonkhanitsa zofukizira zamkuwa zija zomwe anthu opsererawo anabwera nazo ndipo anazisula kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, 40monga momwe Yehova anamulangizira kudzera mwa Mose. Chimenechi chinali chikumbutso kwa Aisraeli kuti munthu wina aliyense, kupatula zidzukulu za Aaroni, sayenera kupsereza lubani pamaso pa Yehova, kuopa kuti munthu woteroyo angakhale ngati Kora ndi omutsatira ake.

41Tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisraeli linatsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Iwo anati, “Inu mwapha anthu a Yehova.”

42Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. 43Pamenepo Mose ndi Aaroni anapita patsogolo pa tenti ya msonkhano ija 44ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 45“Chokani pakati pa gulu la anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.” Ndipo iwo anagwa pansi chafufumimba.

46Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Tenga chofukizira chako ndipo ikamo lubani pamodzi ndi moto wochokera pa guwa lansembe, fulumira, pita pa gulu la anthuwo ndipo ukachite nsembe yopepesera machimo awo popeza mkwiyo wa Yehova wafika, mliri wayamba.” 47Ndipo Aaroni anachita monga ananenera Mose, nathamangira mʼkatikati mwa gulu la anthuwo. Pamenepo nʼkuti mliri utayamba kale pakati pa anthu aja ndipo Aaroni anafukiza lubani ndi kupereka nsembe yopepesera machimo awo. 48Iye anayimirira pakati pa anthu amoyo ndi akufa ndipo mliri unaleka. 49Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora. 50Ndipo Aaroni anabwerera kwa Mose ku khomo la tenti ya msonkhano, chifukwa mliriwo unali utatha.