Numeri 12 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 12:1-16

Miriamu ndi Aaroni Atsutsana ndi Mose

1Miriamu ndi Aaroni anayamba kuyankhula motsutsana ndi Mose chifukwa cha mkazi wa ku Kusi, popeza Moseyo anakwatira Mkusi. 2Iwowo anafunsa kuti, “Kodi Yehova anayankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sanayankhule kudzeranso mwa ife?” Ndipo Yehova anamva zimenezi.

3(Koma Mose anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense pa dziko lapansi).

4Nthawi yomweyo Yehova anati kwa Mose, Aaroni ndi Miriamu, “Bwerani ku tenti ya msonkhano nonse atatu.” Ndipo atatuwo anapitadi kumeneko. 5Tsono Yehova anatsika mu mtambo, nayima pa khomo la chihema. Kenaka anayitana Aaroni ndi Miriamu. Ndipo onse awiri atapita patsogolo, 6Mulungu anati, “Mverani mawu anga:

“Pakakhala mneneri wa Yehova pakati panu,

ndimadzionetsera kwa iyeyo mʼmasomphenya,

ndimayankhula naye mʼmaloto.

7Koma sinditero ndi Mose mtumiki wanga;

Iyeyu ndi wokhulupirika mʼnyumba yanga yonse.

8Ndimayankhula naye maso ndi maso,

momveka bwino osati mophiphiritsa;

ndipo amaona maonekedwe a Yehova.

Nʼchifukwa chiyani simunaope

kuyankhula motsutsana ndi Mose mtumiki wanga?”

9Ndipo Yehova anawakwiyira, nachoka.

10Pamene mtambo unachoka pamwamba pa Chihema, taonani, Miriamu anagwidwa ndi khate. Aaroni atachewuka anaona Miriamu ali ndi khate; 11ndipo Aaroni anawuza Mose kuti, “Pepani mbuye wanga, musatilange chifukwa cha tchimo limene tachita mopusa. 12Musalole kuti Miriamu akhale ngati mwana wobadwa wakufa kuchoka mʼmimba mwa amayi ake, thupi lake litawonongeka.”

13Tsono Mose anafuwulira Yehova kuti, “Chonde Inu Mulungu, muchiritseni!”

14Yehova anayankha Mose kuti, “Abambo ake akanamulavulira malovu mʼmaso, kodi sakanakhala wonyozeka masiku asanu ndi awiri? Mutsekereni kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri, kenaka mumulowetsenso.” 15Choncho anamutsekera Miriamu kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri ndipo anthu sanayende ulendo wawo mpaka Miriamu atamulowetsanso.

16Pambuyo pake anthu ananyamuka ku Heziroti ndi kukamanga mʼchipululu cha Parani.