Numeri 11 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 11:1-35

Moto Wochokera kwa Yehova

1Anthu atadandaula kwa Yehova chifukwa cha mavuto awo, Yehovayo anamva ndipo anakwiya kwambiri. Kenaka moto wa Yehova unayaka pakati pawo ndi kutentha zigawo zina za kunja kwa msasa. 2Anthuwo analira kwa Mose ndipo Moseyo atapemphera kwa Yehova, motowo unazima. 3Motero malowo anawatcha Tabera, chifukwa moto wa Yehova unayaka pakati pawo.

Zinziri Zochokera kwa Yehova

4Anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraeli anayamba kukhumba chakudya cha ku Igupto ndipo Aisraeli nawonso anayamba kufuwula kwambiri nʼkumati, “Tikanangopeza nyama yoti nʼkudya! 5Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo. 6Koma tsopano chilakolako chathu chatha. Sitikuona kanthu kena kakudya koma mana basi!”

7Mana ankafanana ndi mbewu zamapira ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wowuma. 8Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi. 9Mame akamagwa pa msasawo usiku ankagwera kumodzi ndi manawo.

10Mose anamva anthu a banja lililonse akufuwula, banja lililonse pa khomo la tenti yake. Yehova anakwiya kwambiri ndipo Mose anavutikanso mu mtima. 11Mose anafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani mwabweretsa mavuto otere pa mtumiki wanune? Nʼchiyani chimene ndachita choti sichinakusangalatseni mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onsewa? 12Kodi Ndine amene ndinatenga pathupi pa anthu onsewa? Kodi ndinawabala ndine? Bwanji mukundiwuza kuti ndiwanyamule mʼmanja mwanga, monga momwe mlezi amanyamulira kamwana, kupita nawo ku malo omwe munalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo? 13Ndingayipeze kuti nyama yoti anthu onsewa adye? Iwowa akulirira ine kuti, ‘Tipatse nyama tidye!’ 14Sindingathe kusamala anthu onsewa ndekha. Katundu ameneyu ndi wolemera kwambiri kwa ine. 15Ngati umu ndi mmene muzichitira nane, chonde ingondiphani pompano. Koma ngati mwandikomera mtima ndiye ndisaonenso mavutowa.”

16Yehova anawuza Mose kuti, “Undibweretsere anthu 70 ochokera pakati pa akuluakulu a Aisraeli, amene umawadziwa kuti ndiwo atsogoleri komanso akuluakulu a mabanja. Abwere ku tenti ya msonkhano kuti ayime kumeneko pamodzi ndi iwe. 17Ndidzatsika ndi kuyankhula nawe kumeneko, ndipo ndidzatenga mzimu umene uli pa iwe ndi kuyika pa iwowo. Adzakuthandiza kusenza nkhawa za anthuwa ndipo sudzasenzanso wekha.”

18“Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. 19Simudzadya tsiku limodzi lokha, kapena masiku awiri, kapena asanu, khumi kapena masiku makumi awiri, 20koma mwezi wonse, mpaka itakukolani ndi kutopa nayo chifukwa mwakana Yehova yemwe ali pakati panu ndipo mwalira pamaso pake kuti, ‘Bwanji tinachoka ku Igupto?’ ”

21Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’ 22Kodi ngakhale titapha nkhosa ndi ngʼombe, zingawakwanire? Ngakhale titagwira nsomba zonse za mʼnyanja, kodi zingawakwanire iwowa?”

23Yehova anayankha Mose kuti, “Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi.”

24Choncho Mose anatuluka nakawuza anthu zomwe Yehova ananena. Anasonkhanitsa pamodzi akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja ndi kuwayimiritsa mozungulira Chihema. 25Ndipo Yehova anatsika mʼmitambo ndi kuyankhula naye ndipo anatengako mzimu womwe unali pa Mose ndi kuwuyika pa akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja. Pamene mzimuwo unakhazikika pa akuluakuluwo, anayamba kunenera koma sanapitirize.

26Koma anthu ena awiri omwe mayina awo anali Elidadi ndi Medadi, anatsalira mu msasa. Anali nawo mʼgulu la olembedwa aja, koma sanapite nawo ku Chihema. Komabe mzimu unakhala pa iwo ndipo ananenera ali mu msasa. 27Mnyamata wina anathamanga kudzawuza Mose kuti, “Elidadi ndi Medadi akunenera mu msasa.”

28Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha kuti, “Mbuye wanga Mose, aletseni!”

29Koma Mose anati, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikanakonda kuti anthu onse a Yehova akhale aneneri ndi kuti Yehova ayike mzimu wake pa iwo!” 30Mose ndi akuluakulu a Israeli aja anabwerera ku msasa.

31Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi. 32Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse. 33Koma pamene anthuwo ankadya nyamayo, asanayimeze nʼkomwe, ukali wa Yehova unafika pa iwo ndipo Iye anawakantha ndi mliri woopsa. 34Nʼchifukwa chake malowo anawatcha Kibiroti Hatava chifukwa pamenepo anakwirirapo anthu osusuka aja.

35Kuchoka pa Kibiroti Hatava anthuwo anayenda kupita ku Heziroti ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi.

New Russian Translation

Числа 11:1-35

Ропот израильтян

1Народ сетовал перед Господом на тяготы, и, услышав их, Он разгневался. Огонь Господа загорелся среди них и стал пожирать край лагеря. 2Народ стал звать на помощь Моисея. Моисей помолился Господу, и огонь угас. 3То место было названо Тавера11:3 По звучанию это название напоминает еврейское слово «горение»., потому что огонь Господа загорелся среди них.

4Чужеземцами, которые были среди них, овладела прихоть. Тогда и израильтяне вновь принялись плакать вместе с ними и говорить:

– Поесть бы нам мяса! 5Мы помним рыбу, которую ели в Египте даром, огурцы, дыни, лук-порей, репчатый лук и чеснок. 6Но теперь силы у нас иссякли. Ничего, ну совсем ничего, – мы видим только одну манну!

7Манна была похожа на кориандровое семя, цвета же она была светло-желтого11:7 Букв.: «видом как бдолах». Бдолах – ароматная прозрачная смола одного из деревьев, растущих в Аравии.. 8Народ ходил и собирал ее, а затем перемалывал ее ручными жерновами или толок в ступе. Они готовили ее в горшке или делали из нее лепешки. По вкусу она напоминала лепешки, испеченные с оливковым маслом. 9Когда ночью на лагерь опускалась роса, опускалась на него и манна.

Семьдесят старейшин

10Моисей услышал, как народ в каждой семье плачет у входа в свои шатры. Господь очень разгневался, и Моисей огорчился. 11Он спросил Господа:

– За что Ты так мучаешь меня? Чем я прогневил Тебя, что Ты возложил на меня бремя этого народа? 12Разве я зачал этот народ? Разве я родил его? Почему Ты велишь мне нести его на руках, как нянька носит младенца, в страну, которую Ты с клятвой обещал их отцам? 13Где мне взять мясо для этого народа? Они плачут предо мной и говорят: «Накорми нас мясом!» 14Я не могу нести бремя этого народа один; мне это не под силу. 15Если Ты собираешься так обходиться со мной, то прошу, предай меня смерти прямо сейчас, если я нашел у Тебя расположение, чтобы мне не видеть своей беды.

16Господь сказал Моисею:

– Приведи Мне семьдесят человек из израильских старейшин, которых ты знаешь как вождей народа. Пусть они придут к шатру собрания и встанут там с тобой. 17Я сойду и буду говорить с тобой там. Я возьму от Духа, что на тебе, и возложу на них. Они помогут тебе нести бремя народа, чтобы тебе не нести его одному.

18Скажи народу: «Освятитесь к завтрашнему дню, и будете есть мясо. Господь услышал, как вы плакали и говорили: „Поесть бы нам мяса! В Египте было лучше!“ Господь накормит вас мясом. 19Вы будете есть его не один день, не два, не пять, не десять, не двадцать дней, 20а целый месяц, пока оно не полезет у вас из ноздрей и не станет для вас отвратительным, потому что вы отвергли Господа, Который среди вас, и плакали перед Ним, говоря: „Зачем мы ушли из Египта!“»

21Моисей сказал:

– Я здесь среди шестисот тысяч пеших мужчин, а Ты говоришь: «Я буду кормить их мясом целый месяц!» 22Да разве хватит им, если для них забьют весь скот, какой только есть? Разве хватит им, если для них выловят в море всю рыбу?

23Господь ответил Моисею:

– Разве рука Господа коротка? Сейчас ты увидишь, исполнится ли тебе Мое слово.

24Моисей вышел и передал народу то, что сказал Господь. Он собрал семьдесят человек из старейшин и поставил их вокруг шатра. 25Тогда Господь сошел в облаке и говорил с ним. Он взял от Духа, что был на нем, и возложил на семьдесят старейшин. Дух почил на них, и они пророчествовали, но потом перестали11:25 Или: «пророчествовали, и не прекращали»..

26Два человека, которых звали Элдад и Медад, оставались в лагере. Они были записаны между старейшинами, но не вышли к шатру. Дух почил и на них, и они пророчествовали в лагере. 27Юноша прибежал и сказал Моисею:

– Элдад и Медад пророчествуют в лагере.

28Иисус, сын Навин, который был помощником Моисея с юности11:28 Или: «один из его избранных»., сказал:

– Моисей, господин мой, останови их!

29Но Моисей ответил:

– Ты ревнуешь за меня? Я хотел бы, чтобы все в народе Господа стали пророками и Господь послал бы на них Своего Духа!

30Потом Моисей и старейшины Израиля возвратились в лагерь.

Перепела от Господа

31И поднялся ветер от Господа и принес перепелов с моря. Они были везде на расстоянии дневного пути в каждую сторону от лагеря, летая на высоте около двух локтей от земли. 32Весь тот день, всю ночь и весь следующий день народ ходил собирать перепелов, и никто не собрал меньше десяти хомеров11:32 Возможно, около 1 000 кг.. Они разложили их вокруг лагеря. 33И пока еще мясо было у них на зубах, прежде чем его можно было проглотить, Господь разгневался на народ и поразил его лютым мором. 34Поэтому то место было названо Киврот-Гаттаава11:34 Это название означает «могилы страстного желания».: там похоронили одержимых прихотью.

35Из Киврот-Гаттаавы народ двинулся к Хацероту и остановился там.