Nehemiya 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nehemiya 13:1-31

Kukonza Zinthu Kotsiriza kwa Nehemiya

1Pa tsiku limenelo anawerenga buku la Mose anthu akumva. Ndipo anapeza mawu akuti, Mwamoni kapena Mmowabu asalowe konse mu msonkhano wa Mulungu. 2Paja iwowa sanawachingamire Aisraeli kukawapatsa chakudya ndi madzi. Mʼmalo mwake analemba ganyu Baalamu kuti adzawatemberere. Komabe Mulungu wathu anasandutsa tembererolo kukhala mdalitso. 3Anthu atamva lamuloli, anachotsa pakati pawo onse amene anali achilendo.

4Izi zisanachitike, wansembe Eliyasibu anali atasankhidwa kukhala woyangʼanira zipinda zosungiramo katundu za Nyumba ya Mulungu. Iyeyu ankagwirizana kwambiri ndi Tobiya. 5Choncho anamupatsa chipinda chachikulu chimene kale ankasungamo zopereka zakudya, lubani, ziwiya, zopereka za chakhumi za tirigu, vinyo ndi mafuta zoyenera kuperekedwa kwa Alevi, oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, komanso mphatso zoyenera kupereka kwa ansembe.

6Koma pamene izi zonse zinkachitika mu Yerusalemu, ine kunalibe popeza mʼchaka cha 32 cha Aritasasita mfumu ya Babuloni ine ndinabwerera kwa mfumu. Patapitanso nthawi ndinapempha chilolezo kwa mfumuyo 7ndipo ndinabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko ndinamva za chinthu choyipa chimene Eliyasibu anachita pomupatsa Tobiya chipinda mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu. 8Ndinapsa mtima kwambiri ndipo ndinataya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali mʼchipindamo. 9Ndinalamulira kuti ayeretse zipinda, ndipo kenaka ndinabwezeramo zida za mʼNyumba ya Mulungu, pamodzi ndi chopereka cha zakudya ndi lubani.

10Ndinapezanso kuti Alevi sankalandira magawo awo amene amayera kulandira. Chotsatira chake Alevi onse pamodzi ndi oyimba nyimbo amene ankagwira ku Nyumba ya Mulungu anathawa, aliyense kupita ku munda wake. 11Choncho ndinadzudzula akuluakulu aja ndipo ndinawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa?” Ndipo ine ndinawayitanitsa pamodzi ndi kuwayika mʼmalo awo.

12Pambuyo pake Ayuda anayambanso kubwera ndi zopereka zawo za chakhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta kuti ziperekedwe ku nyumba yosungiramo chuma. 13Ndipo ndinasankha wansembe Selemiya, mlembi Zadoki, ndi Mlevi wotchedwa Pedaya kukhala oyangʼanira zipinda zosungiramo. Ndinasankhanso Hanani mwana wa Zakuri mwana wa Mataniya kukhala wowathandizira chifukwa ndinaona kuti anthu awa anali odalirika. Ntchito yawo inali yogawira abale awo zinthu zofunika.

14Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zimenezi, ndipo musafafanize ntchito zanga zimene ndachita mokhulupirika pa Nyumba yanu pofuna kukutumikirani.

15Nthawi imeneyo ndinaona anthu a mu Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la Sabata. Ena ankawunjika tirigu milumilu ndi kumasenzetsa abulu. Enanso ankabwera ndi vinyo, mphesa, mkuyu ndi katundu wa mitundumitundu ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Choncho ndinawachenjeza za kugulitsa zakudya pa tsiku la Sabata. 16Nawonso anthu a ku Turo amene ankakhala mu Yerusalemu ankabweretsa nsomba ndi akatundu ena onse amalonda kudzagulitsa pa Sabata kwa anthu a mʼdziko la Yuda ndi a mu Yerusalemu. 17Ndipo ndinadzudzula anthu olemekezeka a dziko la Yuda. Ndinawafunsa kuti, “Nʼchoyipa chanji mukuchitachi, kumayipitsa tsiku la Sabata chotere? 18Makolo anu anachita zomwezi ndipo Mulungu wathu anadzetsa mavuto pa ife ndi pa mzinda uwu. Kodi inu mukufuna kuwutsanso mkwiyo wa Mulungu pa Israeli pamene mukudetsa tsiku la Sabata?”

19Nʼchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuyamba kuda, tsiku la Sabata lisanayambe, azitseka zipata zonse za Yerusalemu ndipo asazitsekule mpaka sabata litatha. Ndinayika ena mwa antchito anga oyangʼanira pa zipata kuti katundu aliyense asalowe mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata. 20Choncho kamodzi kapena kawiri anthu amalonda ndi anthu ogulitsa katundu osiyanasiyana ankagona usiku wonse kunja kwa Yerusalemu. 21Koma ndinawachenjeza ndi kuwafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Ngati muchitanso zimenezi, ine ndidzakugwirani.” Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerenso pa tsiku la Sabata. 22Ndipo ndinalamulira Alevi kuti adziyeretse okha ndi kubwera kudzalonda pa zipata ndi cholinga choti tsiku la Sabata likhale tsiku loyera.

Inu Mulungu wanga, kumbukireninso ine pa zimenezi ndipo mundisunge malingana ndi chikondi chanu chachikulu chosasinthika.

23Masiku amenewo ndinaonanso anthu a ku Yuda amene anakwatira akazi ochokera ku Asidodi, Amoni ndi Mowabu. 24Theka la ana awo linkayankhula chiyankhulo cha Asidodi kapena chiyankhulo chimodzi cha anthu ena, ndipo sankathanso kuyankhula chiyankhulo cha Ayuda. 25Tsono ndinakangana nawo ndi kuwatemberera. Ndinamenya ena mwa anthuwo ndi kuzula tsitsi lawo. Ine ndinawalumbiritsa mʼdzina la Mulungu kuti, “Inu musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena inuyo ngakhale ana anu aamuna kukwatira ana awo aakazi. 26Kodi Solomoni mfumu ya Israeli suja anachimwa chifukwa cha ukwati ngati umenewu. Pakati pa mitundu yambiri panalibe mfumu ngati iyi. Iye anakondedwa ndi Mulungu wake, ndipo Mulungu anamuyika kukhala mfumu ya Israeli yense, koma iyeyo anachimwa chifukwa cha akazi achilendo. 27Kodi tsopano ife tizimva inu kuti mukuchita choyipa chachikulu chimenechi, kupandukira Yehova Mulungu wathu pomakwatira akazi achilendo?”

28Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada mwana Eliyasibu mkulu wa ansembe nʼkuti nthawi imeneyi ali mpongozi wa Sanibalati wa ku Horoni. Choncho ndinamuthamangitsa pamaso panga.

29Inu Mulungu wanga, mukumbukire mmene iwo anayipitsira unsembe, pangano la unsembe komanso la Alevi.

30Motero ndinayeretsa ansembe ndi Alevi powachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndinakhazikitsa ntchito zawo, kuti aliyense akhale pa ntchito yake. 31Ndiponso kupereka nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha pa nthawi yake.

Ndikumbukireni pondikomera mtima, Inu Mulungu wanga.