Nahumu 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nahumu 2:1-13

Kugwa kwa Ninive

1Wodzathira nkhondo akubwera

kudzalimbana nawe, Ninive.

Tetezani malinga anu,

dziyangʼanani ku msewu,

konzekerani nkhondo,

valani dzilimbe.

2Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo

ngati ulemerero wa Israeli,

ngakhale anthu owononga anawawononga kotheratu

ndipo anawononganso mpesa wawo.

3Zishango za ankhondo ake ndi zofiira;

asilikali ake avala zovala zofiirira.

Zitsulo za pa magaleta zikunyezimira

tsiku la kukonzekera kwake.

Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.

4Magaleta akuthamanga mʼmisewu

akungothamangathamanga pa mabwalo.

Akuoneka ngati miyuni yoyaka;

akuthamanga ngati chingʼaningʼani.

5Iye akuyitanitsa asilikali ake wolemekezeka,

koma iwo akubwera napunthwa.

Akuthamangira ku linga la mzinda;

akuyimika chodzitchinjirizira pamalo pake.

6Atsekula zipata zotchinga madzi a mu mtsinje

ndipo nyumba yaufumu yagwa.

7Zatsimikizika kuti mzinda

utengedwa ndi kupita ku ukapolo.

Akapolo aakazi akulira ngati nkhunda

ndipo akudziguguda pachifuwa.

8Ninive ali ngati dziwe,

ndipo madzi ake akutayika.

Iwo akufuwula kuti, “Imani! Imani!”

Koma palibe amene akubwerera.

9Funkhani siliva!

Funkhani golide!

Katundu wake ndi wochuluka kwambiri,

chuma chochokera pa zinthu zake zamtengowapatali!

10Iye wawonongedwa, wafunkhidwa ndipo wavulidwa!

Mitima yasweka, mawondo akuwombana,

anthu akunjenjemera ndipo

nkhope zasandulika ndi mantha.

11Kodi tsopano dzenje la mikango lili kuti,

malo amene mikango inkadyetserako ana ake,

kumene mkango waumuna ndi waukazi unkapitako,

ndipo ana a mkango sankaopa kanthu kalikonse?

12Mkango waumuna unkapha nyama yokwanira ana ake

ndiponso kuphera nyama mkango waukazi,

kudzaza phanga lake ndi zimene wapha

ndiponso dzenje lake ndi nyama imene waphayo.

13Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Ine ndikutsutsana nawe.

Ndidzatentha magaleta ako mpaka utsi tolotolo,

ndipo lupanga lidzapha mikango yako yayingʼono;

sindidzakusiyira chilichonse choti udye pa dziko lapansi.

Mawu a amithenga anu sadzamvekanso.”