Mlaliki 9 – CCL & CST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 9:1-18

Mathero a Zinthu Zonse ndi Wofanana

1Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani. 2Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe.

Zomwe zimachitikira munthu wabwino,

zimachitikiranso munthu wochimwa,

zomwe zimachitikira amene amalumbira,

zimachitikiranso amene amaopa kulumbira.

3Choyipa chimene chili mʼzonse zochitika pansi ndi ichi: Mathero a zonse ndi amodzi. Ndithu, mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoyipa, ndipo mʼmitima mwawo muli zamisala pamene ali ndi moyo, potsiriza pake iwo amakakhala pamodzi ndi anthu akufa. 4Aliyense amene ali ndi moyo amakhala ndi chiyembekezo, pajatu galu wamoyo aposa mkango wakufa!

5Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,

koma akufa sadziwa kanthu;

alibe mphotho ina yowonjezera,

ndipo palibe amene amawakumbukira.

6Chikondi chawo, chidani chawo

ndiponso nsanje yawo, zonse zinatha kalekale;

sadzakhalanso ndi gawo

pa zonse zochitika pansi pano.

7Pita, kadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti tsopano Mulungu akukondwera ndi zochita zako. 8Uzivala zovala zoyera nthawi zonse, uzidzola mafuta mʼmutu mwako nthawi zonse. 9Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano. 10Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.

11Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano:

opambana pa kuthamanga si aliwiro,

kapena opambana pa nkhondo si amphamvu,

ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru,

kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri,

kapena okomeredwa mtima si ophunzira;

koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.

12Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti:

monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde,

kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha,

chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa,

pamene tsoka limawagwera mosayembekezera.

Nzeru Iposa Uchitsiru

13Ine ndinaonanso pansi pano chitsanzo ichi cha nzeru chimene chinandikhudza kwambiri: 14Panali mzinda waungʼono umene unali ndi anthu owerengeka. Ndipo mfumu yamphamvu inabwera kudzawuthira nkhondo, inawuzungulira ndi kumanga mitumbira yankhondo. 15Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo. 16Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake.

17Mawu oyankhula mofatsa a munthu wanzeru, anthu amawasamalira kwambiri

kupambana kufuwula kwa mfumu ya zitsiru.

18Nzeru ndi yabwino kupambana zida zankhondo,

koma wochimwa mmodzi amawononga zinthu zambiri zabwino.

Nueva Versión Internacional (Castilian)

Eclesiastés 9:1-18

Un destino común

1A todo esto me dediqué de lleno, y en todo esto comprobé que los justos y los sabios, y sus obras, están en las manos de Dios; que el hombre nada sabe del amor ni del odio, aunque los tenga ante sus ojos. 2Para todos hay un mismo final:

para el justo y el injusto,

para el bueno y el malo,

para el puro y el impuro,

para el que ofrece sacrificios

y para el que no los ofrece;

para el bueno y para el pecador,

para el que hace juramentos

y para el que no los hace.

3Hay un mal en todo lo que se hace en esta vida: que todos tienen un mismo final. Además, el corazón del hombre rebosa de maldad; la locura está en su corazón toda su vida, y su fin está entre los muertos. 4¿Por quién, pues, decidirse? Entre todos los vivos hay esperanza, pues

vale más perro vivo

que león muerto.

5Porque los vivos saben que han de morir, pero los muertos no saben nada ni esperan nada, pues su memoria cae en el olvido. 6Sus amores, odios y pasiones llegan a su fin, y nunca más vuelven a tener parte en nada de lo que se hace en esta vida.

7¡Anda, come tu pan con alegría! ¡Bebe tu vino con buen ánimo, que Dios ya se ha agradado de tus obras! 8Que sean siempre blancos tus vestidos, y que no falte nunca el perfume en tus cabellos. 9Goza de la vida con la mujer amada cada día de la vida sin sentido que Dios te ha dado en este mundo. ¡Cada uno de tus absurdos días! Esto es lo que te ha tocado de todos tus afanes en este mundo. 10Y todo lo que esté en tu mano hacer, hazlo con todo empeño; porque en el sepulcro, adonde te diriges, no hay trabajo ni planes ni conocimiento ni sabiduría.

Más vale maña que fuerza

11Me fijé en que en esta vida la carrera no la ganan los más veloces, ni ganan la batalla los más valientes; que tampoco los sabios tienen qué comer, ni los inteligentes abundan en dinero, ni los instruidos gozan de simpatía, sino que a todos les llegan buenos y malos tiempos.

12Vi además que nadie sabe cuándo le llegará su hora. Así como los peces caen en la red maligna y las aves caen en la trampa, también los hombres se ven atrapados por una desgracia que de pronto les sobreviene.

13También vi en este mundo un notable caso de sabiduría: 14una ciudad pequeña, con pocos habitantes, contra la cual se dirigió un rey poderoso que la sitió y construyó a su alrededor una impresionante maquinaria de asalto. 15En esa ciudad había un hombre, pobre pero sabio, que con su sabiduría podría haber salvado a la ciudad, ¡pero nadie se acordó de aquel hombre pobre!

16Yo digo que «más vale maña que fuerza», aun cuando se menosprecie la sabiduría del pobre y no se preste atención a sus palabras.

17Más se atiende a las palabras tranquilas de los sabios

que a los gritos del jefe de los necios.

18Vale más la sabiduría

que las armas de guerra.

Un solo error

acaba con muchos bienes.