Mlaliki 5 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 5:1-20

Lemekeza Mulungu

1Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.

2Usamafulumire kuyankhula,

usafulumire mu mtima mwako

kunena chilichonse pamaso pa Mulungu.

Mulungu ali kumwamba

ndipo iwe uli pa dziko lapansi,

choncho mawu ako akhale ochepa.

3Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oyipa,

ndipo kuchuluka kwa mawu kumadzetsa uchitsiru.

4Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako. 5Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo. 6Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako? 7Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.

Chuma Nʼchopandapake

8Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa. 9Anthu onse amatengako zokolola za mʼminda: koma ndi mfumu yokha imene imapeza phindu la mindayi.

10Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo;

aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza.

Izinso ndi zopandapake.

11Chuma chikachuluka

akudya nawo chumacho amachulukanso.

Nanga mwini wake amapindulapo chiyani

kuposa kumangochiyangʼana ndi maso ake?

12Wantchito amagona tulo tabwino

ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri,

koma munthu wolemera, chuma

sichimulola kuti agone.

13Ine ndinaona choyipa chomvetsa chisoni pansi pano:

chuma chokundikidwa chikupweteka mwini wake yemwe,

14kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka,

kotero kuti pamene wabereka mwana

alibe kanthu koti amusiyire.

15Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake,

ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho.

Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta

palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake.

16Izinso ndi zoyipa kwambiri:

munthu adzapita monga momwe anabwerera,

ndipo iye amapindula chiyani,

pakuti amagwira ntchito yolemetsa yopanda phindu?

17Masiku ake onse ndi odzaza ndi mdima,

kukhumudwa kwakukulu, masautso ndi nkhawa.

18Tsono ndinazindikira kuti nʼchabwino ndi choyenera kuti munthu azidya ndi kumwa, ndi kukhutitsidwa ndi ntchito yake yolemetsa imene amayigwira pansi pano pa nthawi yake yochepa imene Mulungu amamupatsa, poti ichi ndiye chake. 19Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. 20Munthu wotereyu saganizirapo za masiku a moyo wake, chifukwa Mulungu amamutanganidwitsa ndi chisangalalo cha mu mtima mwake.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

傳道書 5:1-20

敬畏上帝

1你進入上帝的殿時要小心謹慎,近前傾聽勝過愚人獻祭,因為他們不知道自己是在作惡。 2在上帝面前不要冒失開口,不可急於發言,因為祂在天上,你在地上。所以,你要少言寡語。 3事務繁雜,夜裡多夢;多言多語,顯出愚昧。 4你向上帝許願,不可遲遲不還,因為祂不喜歡這樣的愚人。要還所許的願。 5與其許了願不還,倒不如不許。 6不要在言語上犯罪,也不要在祭司5·6 祭司」希伯來文是「使者」。面前說許錯了願。為什麼用言語惹上帝發怒,以致祂摧毀你手中的工作呢? 7多夢多言都是虛空。你只要敬畏上帝!

財富虛空

8若你在某地看見窮人受欺壓,公平正義被扭曲,不要震驚,因為官上有官,在眾官之上還有更高的官。 9況且,地的出產滋養萬物,就是君王也需要從田地得到供應。 10貪愛錢財的,金銀不能使他滿足;貪圖富裕的,再多的利益也不能叫他稱心。這也是虛空! 11財富增加,消費的人也增加,這對財富的主人有什麼益處呢?只是過眼雲煙罷了! 12勞力的人不管吃多吃少,總是睡得香甜;富人的萬貫家財卻害得他不能成眠。 13我看到日光之下有一件可悲的事:有人積攢財寶,反而害了自己。 14經營不善,便財富盡失,什麼也不能留給兒子。 15人怎樣從母腹空空而來,也必照樣空空而去;勞碌一生,什麼也不能帶走。 16這是多麼可悲啊!人怎樣來,也要怎樣去,為風勞碌有什麼益處呢? 17他一生活在黑暗中,飽受煩惱、病痛和憤怒的困擾。 18我認為人生最美最善的是,在上帝所賜的短暫歲月中盡情吃喝,享受自己在日光之下勞苦得來的成果。因為這是人當得的。 19上帝不單給人財富,也叫他能吃能喝,享用自己所當得的,並在勞碌中得到快樂,這都是上帝的恩賜。 20他不用擔憂自己壽命的長短,因為上帝使他心裡充滿喜樂。