Mlaliki 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 4:1-16

Matsoka ndi Mavuto a Moyo Uno

1Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano:

ndinaona misozi ya anthu opsinjika,

ndipo iwo alibe owatonthoza;

mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo

ndipo iwonso analibe owatonthoza.

2Ndipo ndinanena kuti akufa,

amene anafa kale,

ndi osangalala kuposa amoyo,

amene akanalibe ndi moyo.

3Koma wopambana onsewa

ndi amene sanabadwe,

amene sanaone zoyipa

zimene chimachitika pansi pano.

4Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

5Chitsiru chimangoti manja ake lobodo

ndi kudzipha chokha ndi njala.

6Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere,

kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto,

ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.

7Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:

8Panali munthu amene anali yekhayekha;

analibe mwana kapena mʼbale.

Ntchito yake yolemetsa sinkatha,

ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake.

Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani?

Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?”

Izinso ndi zopandapake,

zosasangalatsa!

9Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,

chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:

10Ngati winayo agwa,

mnzakeyo adzamudzutsa.

Koma tsoka kwa munthu amene agwa

ndipo alibe wina woti amudzutse!

11Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana.

Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?

12Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa,

koma anthu awiri akhoza kudziteteza.

Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.

Kutukuka Nʼkopandapake

13Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo. 14Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo. 15Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu. 16Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.