Miyambo 9 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 9:1-18

Za Nzeru ndi Uchitsiru

1Nzeru inamanga nyumba yake;

inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.

2Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake;

inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.

3Nzeruyo inatuma adzakazi ake,

kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,

4“Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!”

Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,

5“Bwerani, dzadyeni chakudya changa

ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.

6Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo;

yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”

7Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo;

aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.

8Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe;

dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.

9Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru;

ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.

10Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;

kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.

11Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka,

ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.

12Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa;

ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.

13Uchitsiru ndi mkazi waphokoso,

wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.

14Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake,

pamalo aatali a mu mzinda,

15kuti aziyitana anthu ongodutsa,

amene akunka nayenda njira zawo.

16Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,”

ndipo kwa wopanda nzeru amati,

17“Madzi akuba ndiye amatsekemera;

chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”

18Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko,

ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.