Miyambo 8 – CCL & NAV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 8:1-36

Nzeru Ikuyitana

1Kodi nzeru sikuyitana?

Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?

2Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira,

imayima pa mphambano ya misewu.

3Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda,

pa makomo olowera imafuwula kuti,

4Inu anthu, ndikuyitana inu;

ndikuyitanatu anthu onse.

5Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera;

inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.

6Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri;

ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.

7Pakamwa panga pamayankhula zoona

ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.

8Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama;

mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.

9Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona;

kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.

10Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva,

nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.

11Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali,

ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.

12Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera.

Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.

13Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa.

Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama,

kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.

14Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino;

ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.

15Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira.

Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.

16Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula.

Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.

17Ndimakonda amene amandikonda,

ndipo amene amandifunafuna amandipeza.

18Ine ndili ndi chuma ndi ulemu,

chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.

19Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala;

zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.

20Ndimachita zinthu zolungama.

Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.

21Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda

ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.

22“Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba.

Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.

23Ndinapangidwa kalekalelo,

pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.

24Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi,

zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.

25Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo,

mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,

26lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake;

lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.

27Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga,

pamene ankalemba malire a nyanja yozama,

28pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga

ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,

29pamene anayikira nyanja malire

kuti madzi asadutse malirewo,

ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.

30Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri;

ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku,

kusangalala nthawi zonse pamaso pake.

31Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse

ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”

32“Ndiye tsono ana inu, ndimvereni;

odala anthu amene amasunga njira zanga.

33Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru;

musanyozere mawu anga.

34Wodala munthu amene amandimvera,

amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku,

kudikirira pa chitseko changa.

35Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo

ndipo Yehova amamukomera mtima.

36Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha;

onse amene amandida amakonda imfa.”

Ketab El Hayat

الأمثال 8:1-36

نداء الحكمة

1أَلا تُنَادِي الْحِكْمَةُ؟ أَلا يَرْتَفِعُ صَوْتُ الْفِطْنَةِ هَاتِفاً؟ 2إِنَّهَا تَقِفُ عَلَى الْمُرْتَفَعَاتِ، فِي مُحَاذَاةِ الطَّرِيقِ، وَعِنْدَ مُلْتَقَى الشَّوَارِعِ. 3إِلَى جُوَارِ أَبْوَابِ الْمَدِينَةِ وَفِي مَدْخَلِ الثَّغْرِ، تَنْتَصِبُ مُجَاهِرَةً قَائِلَةً: 4إِيَّاكُمْ أَدْعُو أَيُّهَا النَّاسُ وَأَرْفَعُ صَوْتِي بِالنِّدَاءِ إِلَى كُلِّ بَنِي الْبَشَرِ. 5أَيُّهَا الْحَمْقَى، تَعَلَّمُوا الْفِطْنَةَ، وَأَيُّهَا الأَغْبِيَاءُ اكْتَسِبُوا فَهْماً. 6أَنْصِتُوا لأَنَّنِي سَأَنْطِقُ بِأَقْوَالٍ أَثِيرَةٍ، وَأَفْتَحُ شَفَتَيَّ بِكَلامٍ قَوِيمٍ. 7لأَنَّ فَمِي يَتَكَلَّمُ بِالصِّدْقِ، وَشَفَتَيَّ تَمْقُتَانِ الإِثْمَ. 8كُلُّ أَقْوَالِ فَمِي عَادِلَةٌ خَالِيَةٌ مِنْ كُلِّ الْتِوَاءٍ وَاعْوِجَاجٍ. 9قَوِيمَةٌ لَدَى الْفَهِيمِ، وَمُسْتَقِيمَةٌ لِلَّذِينَ أَدْرَكُوا الْمَعْرِفَةَ. 10اخْتَرْ إِرْشَادِي عِوَضَ الْفِضَّةِ، وَالْمَعْرِفَةَ بَدَلَ الذَّهَبِ الْخَالِصِ. 11لأَنَّ الْحِكْمَةَ أَفْضَلُ مِنَ اللَّآلِئِ، وَكُلُّ مُشْتَهَيَاتِكَ لَا تُعَادِلُهَا.

12أَنَا الْحِكْمَةُ أَسْكُنُ التَّعَقُّلَ، وَأَمْلِكُ الْمَعْرِفَةَ وَالتَّدْبِيرَ. 13مَخَافَةُ الرَّبِّ كَرَاهَةُ الشَّرِّ. أَنَا قَدْ أَبْغَضْتُ الْكِبْرِيَاءَ وَالْغَطْرَسَةَ وَطَرِيقَ السُّوءِ وَفَمَ الْمَكْرِ. 14لِي الْمَشُورَةُ وَالرَّأْيُ الصَّائِبُ، لِي الْفِطْنَةُ وَالْقُوَّةُ. 15بِمَعُونَتِي يَحْكُمُ الْمُلُوكُ، وَيَشْتَرِعُ الْحُكَّامُ مَا هُوَ عَدْلٌ. 16بِمَعُونَتِي يَسُودُ الرُّؤَسَاءُ وَالْعُظَمَاءُ وَكُلُّ قُضَاةِ الأَرْضِ. 17أُحِبُّ مَنْ يُحِبُّونَنِي، وَمَنْ يَجِدُّ فِي الْبَحْثِ عَنِّي يَعْثُرُ علَيَّ. 18لَدَيَّ الثَّرَاءُ وَالْمَجْدُ وَالْغِنَى الدَّائِمُ وَالصَّلاحُ. 19ثَمَرِي أَفْضَلُ مِنَ الذَّهَبِ الْخَالِصِ، وَغَلَّتِي خَيْرٌ مِنَ الْفِضَّةِ الْمُنْتَقَاةِ. 20أَمْشِي فِي طَرِيقِ الْبِرِّ، وَفِي سُبُلِ الْعَدْلِ أَسِيرُ. 21لِكَيْ أَوَرِّثَ مُحِبِّيَّ غِنىً، وَأَمْلأَ خَزَائِنَهُمْ كُنُوزاً.

22اقْتَنَانِي الرَّبُّ مُنْذُ بَدْءِ خَلْقِهِ، مِنْ قَبْلِ الشُّرُوعِ فِي أَعْمَالِهِ الْقَدِيمَةِ. 23مُنْذُ الأَزَلِ أَنَا هُوَ، مُنْذُ الْبَدْءِ قَبْلَ أَنْ تُوجَدَ الأَرْضُ. 24وُلِدْتُ مِنْ قَبْلِ أَنْ تَتَكَوَّنَ اللُّجَجُ وَالْيَنَابِيعُ الْغَزِيرَةُ الْمِيَاهِ. 25وُلِدْتُ مِنْ قَبْلِ الْجِبَالِ وَالتِّلالِ. 26إِذْ لَمْ يَكُنْ قَدْ خَلَقَ الأَرْضَ بَعْدُ، وَلا الْبَرَارِيَ وَلا بِدَايَةَ أَتْرِبَةِ الْمَسْكُونَةِ. 27وَعِنْدَمَا ثَبَّتَ الرَّبُّ السَّمَاءَ، وَحِينَ رَسَمَ دَائِرَةَ الأُفُقِ حَوْلَ وَجْهِ الْغَمْرِ، كُنْتُ هُنَاكَ. 28عِنْدَمَا ثَبَّتَ السُّحُبَ فِي الْعَلاءِ، وَرَسَّخَ يَنَابِيعَ اللُّجَجِ. 29عِنْدَمَا قَرَّرَ لِلْبَحْرِ تُخُوماً لَا تَتَجَاوَزُهَا مِيَاهُهُ مُتَعَدِّيَةً عَلَى أَمْرِ الرَّبِّ، وَحِينَ رَسَمَ أُسُسَ الأَرْضِ، 30كُنْتُ عِنْدَهُ صَانِعاً مُبْدِعاً، وَكُنْتُ كُلَّ يَوْمٍ لَذَّتَهُ، أَفِيضُ بَهْجَةً دَائِماً أَمَامَهُ. 31مُغْتَبِطَةً بِعَالَمِهِ الْمَسْكُونِ، وَمَسَرَّاتِي مَعَ بَنِي آدَمَ.

32وَالآنَ أَصْغُوا إِلَيَّ أَيُّهَا الأَبْنَاءُ، إِذْ طُوبَى لِمَنْ يُمَارِسُونَ طُرُقِي. 33اسْتَمِعُوا إِلَى إِرْشَادِي، وَكُونُوا حُكَمَاءَ وَلا تَتَجَاهَلُوهُ. 34طُوبَى لِلإِنْسَانِ الَّذِي يَسْتَمِعُ إلَيَّ، الْحَرِيصِ عَلَى السَّهَرِ عِنْدَ أَبْوَابِي، حَارِساً قَوَائِمَ مَصَارِيعِي، 35لأَنَّ مَنْ يَجِدُنِي يَجِدُ حَيَاةً، وَيَحُوزُ عَلَى مَرْضَاةِ الرَّبِّ. 36وَمَنْ يَضِلُّ عَنِّي يُؤْذِي نَفْسَهُ، وَمَنْ يُبْغِضُنِي يُحِبُّ الْمَوْتَ.