Miyambo 5 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 5:1-23

Chenjezo kwa Mkazi Wachigololo

1Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi,

tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,

2kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru

ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.

3Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi.

Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,

4koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu;

ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.

5Mapazi ake amatsikira ku imfa;

akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.

6Iye saganizirapo za njira ya moyo;

njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.

7Tsopano ana inu, mundimvere;

musawasiye mawu anga.

8Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,

usayandikire khomo la nyumba yake,

9kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;

ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,

10kapenanso alendo angadyerere chuma chako

ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.

11Potsiriza pa moyo wako udzabuwula,

thupi lako lonse litatheratu.

12Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo!

Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!

13Sindinamvere aphunzitsi anga

kapena alangizi anga.

14Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke

pakati pa msonkhano wonse.”

15Imwa madzi a mʼchitsime chakochako,

madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.

16Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu?

Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?

17Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha,

osati uyigawireko alendo.

18Yehova adalitse kasupe wako,

ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.

19Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino.

Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse,

ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.

20Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo?

Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?

21Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona,

ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.

22Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha;

zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha.

23Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo,

adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.