Miyambo 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 4:1-27

Nzeru Iposa Zonse

1Ananu, mverani malangizo a abambo anu;

tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.

2Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino.

Choncho musasiye malangizo anga.

3Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga;

mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.

4Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti,

“Ugwiritse mawu anga pa mtima pako,

usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.

5Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu;

usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.

6Usasiye nzeru ndipo idzakusunga.

Uziyikonda ndipo idzakuteteza.

7Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru.

Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.

8Uyilemekeze nzeruyo ndipo idzakukweza;

ikumbatire nzeruyo ndipo idzakupatsa ulemu.

9Idzayika sangamutu yokongola yamaluwa pamutu pako;

idzakupatsa chipewa chaufumu chaulemu.”

10Mwana wanga, umvere ndi kuvomereza zimene ndikunena,

ndipo zaka za moyo wako zidzakhala zochuluka.

11Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru.

Ndakutsogolera mʼnjira zolungama.

12Pamene ukuyenda, mapazi ako sadzawombana;

ukamadzathamanga, sudzapunthwa.

13Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi.

Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.

14Usayende mʼnjira za anthu oyipa

kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.

15Pewa njira zawo, usayende mʼmenemo;

uzilambalala nʼkumangopita.

16Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa;

tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.

17Paja chakudya chawo ndicho kuchita zoyipa basi

ndipo chakumwa chawo ndi chiwawa.

18Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha

kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.

19Koma njira ya anthu oyipa ili ngati mdima wandiweyani;

iwo sadziwa chomwe chimawapunthwitsa.

20Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena;

tchera khutu ku mawu anga.

21Usayiwale malangizo angawa,

koma uwasunge mu mtima mwako.

22Pakuti amapatsa moyo kwa aliyense amene awapeza

ndipo amachiritsa thupi lake lonse.

23Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu

pakuti ndiwo magwero a moyo.

24Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota;

ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.

25Maso ako ayangʼane patsogolo;

uziyangʼana kutsogolo molunjika.

26Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako

ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.

27Usapatukire kumanja kapena kumanzere;

usapite kumene kuli zoyipa.