Miyambo 31 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 31:1-31

Mawu a Mfumu Lemueli

1Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake:

2Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga?

Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro?

3Usapereke mphamvu yako kwa akazi.

Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu.

4Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu,

mafumu sayenera kumwa vinyo.

Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa

5kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko,

nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka.

6Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa,

vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;

7amwe kuti ayiwale umphawi wawo

asakumbukirenso kuvutika kwawo.

8Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha.

Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.

9Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo.

Uwateteze amphawi ndi osauka.

Mathero: Mkazi Wangwiro

10Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani?

Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.

11Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira

ndipo mwamunayo sasowa phindu.

12Masiku onse a moyo wake

mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.

13Iye amafunafuna ubweya ndi thonje;

amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.

14Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda,

amakatenga chakudya chake kutali.

15Iye amadzuka kusanache kwenikweni;

ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya

ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.

16Iye amalingalira za munda ndi kuwugula;

ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.

17Iye amavala zilimbe

nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.

18Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu,

choncho nyale yake sizima usiku wonse.

19Iye amadzilukira thonje

ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.

20Iye amachitira chifundo anthu osauka

ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.

21Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu;

pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda.

22Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake;

amavala zovala zabafuta ndi zapepo.

23Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda,

ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo.

24Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa;

amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.

25Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake;

ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.

26Iye amayankhula mwanzeru,

amaphunzitsa anthu mwachikondi.

27Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake

ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.

28Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala;

ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,

29“Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana

koma iwe umawaposa onsewa.”

30Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa;

koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.

31Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita

ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.